Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufuna kukondedwa

Kufuna kukondedwa

Kufuna kukondedwa

Kalekale, mu mzinda wina umene unali m’dziko limene panopa limatchedwa Turkey, munali mtsikana wina dzina lake Leya. Leya anali wosaoneka bwino kwenikweni, koma mng’ono wake Rakele, anali wokongola.

RAKELE anakumana ndi mwamuna amene anamukonda kwambiri moti mwamunayo anavomera kugwirira ntchito bambo ake a Rakele kwa zaka seveni kuti amukwatire. Koma usiku wa tsiku la ukwatilo, bambo wa atsikanawo anapatsa mwamunayo Leya m’malo mwa mng’ono wake. Sitikudziwa kuti Leya anamva bwanji ndi zimene bambo ake anachitazo, koma ayenera kuti anadziwa kuti imeneyi sinali njira yabwino yolowera m’banja.

Atazindikira zomwe zinachitika, mwamunayo anakwiya kwambiri. Bambowo anafotokoza kuti pa chikhalidwe chawo, mwana wamkazi wamkulu ndi amene amayenera kuyamba kukwatiwa. Choncho, Leya anapezeka kuti wakwatiwa mwachinyengo ndi mwamuna amenenso kenako anadzakwatira mng’ono wake. Leya ayenera kuti zinkamupweteka kwambiri kuona kuti mwamunayo anali kukonda kwambiri mng’ono wakeyo. Leya sanakhalepo pa chibwenzi ndi mwamunayo, ndiponso mwina analibe zinthu zabwino zilizonse zoti angakumbukire zomwe zinachitika pa tsiku la ukwati wake. Ayenera kuti ankalakalaka kwambiri atamakondedwa ngati mmene Rakele ankakondedwera. Choncho, chifukwa cha zochitika zomwe sakanatha kuzisintha, Leya mwina nthawi zambiri ankamva kuti sakondedwa ndiponso safunidwa. *

Anthu ambiri masiku ano mwina nawonso anayamba amvapo ngati momwe Leya ankamvera. Tonsefe mwachibadwa timafuna kukonda anthu ena ndi kuti anthu ena azitikonda. Mwina timafuna mwamuna kapena mkazi woti azitikonda. Timafunanso kuti makolo athu, ana athu, achibale athu, ndi anzathu azitikonda. Mofanana ndi Leya, mwina timaona kuti anthu ena akukondedwa pamene ifeyo sitikondedwa.

Kuyambira tili ana, timamva nkhani zachikondi zokhudza anthu okongola amene anayamba kukondana ndipo anakhala osangalala moyo wawo wonse. Oimba amangokhalira kuimba za chikondi, ndipo olemba ndakatulo nawonso amatamanda kwambiri chikondi. Komabe, munthu wina wofufuza nkhani ya chikondi analemba kuti: “Palibe ntchito kapena chochitika china chilichonse chimene chimayamba ndi chiyembekezo chabwino kwambiri, koma chomwe nthawi zambiri chimakanika kuposa mmene chimachitira chikondi.” Zoonadi, anthu amene timayenera kukondana nawo kwambiri ndi amene nthawi zambiri amatikhumudwitsa, ndipo amatibweretsera chisoni m’malo mwa chimwemwe chokhalitsa. M’mayiko angapo, pafupifupi mabanja 40 pa mabanja 100 alionse amasudzulana, ndipo mabanja ambiri amene sasudzulana ndi osasangalala.

M’mayiko ambiri, mabanja a kholo limodzi ndiponso mabanja amene ali ndi mavuto akuwonjezeka, ndipo ana nawonso akuzunzika. Komatu, ana makamaka amafunika kukhala m’banja lachikondi, momwe angamamve kuti ndi otetezeka ndiponso amakondedwa. Choncho, kodi chikondi chapita kuti? Kodi n’kuti komwe tingaphunzire za khalidwe lofunika kwambiri limeneli? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Nkhani imeneyi imapezeka mu chaputala 29 ndi 30 m’buku la m’Baibulo la Genesis.