Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zilema Zanga Sizinandifooketse

Zilema Zanga Sizinandifooketse

Zilema Zanga Sizinandifooketse

Yosimbidwa ndi Kouamé NʹGuessan

Tikafika pa chikweza chilichonse ineyo ndi mnzanga tinkangokoka njinga imene tinayendapo paulendowu. Umu munali mu November 2002, ndipo nkhondo ya pachiweniweni inali ili m’kati m’dziko la Ivory Coast, kuno ku Africa. Motero zinali zoopsa kuyenda mumsewu wopanda anthuwu. Patsogolo pathu panali malo otsatira amene asilikali ankasechera anthu apaulendo. Kodi n’chifukwa chiyani ndinali kuyenda ulendo woopsawu panthawi yankhondo?

NDINABADWA mu 1978 ndi matenda enaake. Matendawo ankangokulirakulira. Poyamba ndinali ndi vuto la kumva ndiponso kuphwanya m’miyendo. Ndili mwana azibale anga ankandiseka kuti ndili ndi ‘timiyendo tolobodoka ndiponso kuti ndine gonthi.’ Akuluakulu ankandinyoza ndipo ana ankandikuwiza kuti ndine wopunduka ndi kuti timiyendo tanga n’topanda ntchito.

Nditangoyamba sukulu ndili ndi zaka eyiti anzanga komanso aphunzitsi kusukuluko anayamba kundiseka. Nthawi zambiri ndinkangolakalaka pansi patatseguka n’kundimeza. Poona kuti ndinkachita mantha, anthu ankandiseka. Ndikachoka kunyumba ndinkangopita kusukulu basi.

Ndinkadzifunsa kuti, ‘N’dalakwanji ine kuti ndikhale ndi matendawa?’ Mayi anga anandiuza kuti n’zamuwanthu. Nthawi zina ndikaona olumala ena ndinkadzifunsa kuti, ‘Ndiye kuti nawonso anachita kulodzedwa eti?’

Mu 1992, ndinayamba kumva ululu wadzaoneni m’kasukusuku. Ululuwu utachepako, manja anga anasiya kuwongoka. Patatha zaka ziwiri, diso langa lakumanzere linasiya kuona. Makolo anga anandipititsa kwa asing’anga osiyanasiyana, koma sizinathandize. Ndinasiya sukulu chifukwa cha matenda angawa.

Kufuna Kumvetsa Mawu a Mulungu

Mnzanga wina wokonda Mawu a Mulungu anandipempha kuti ndizipita naye kutchalitchi. Ndinapita kutchalitchiko kwa chaka chathunthu ngakhale kuti m’banja mwathu tinali a chipembedzo cha makolo chokhulupirira mizimu. * Kutchalitchiko sanandithandize kudziwa bwino Baibulo, motero ndinayamba kuona kuti zipembedzo zotchuka sizopindulitsa kwenikweni.

Pali ziphunzitso zina za kutchalitchi zimene zinkandichititsa mantha, makamaka chiphunzitso cha moto wa helo. Ndinkaona kuti siine munthu woipa kwambiri woyenera kukapsa kumoto. Koma sindinkaonanso kuti ndine munthu wabwino moti n’kudzapita kumwamba. Popeza kuti Mawu a Mulungu sindinkawamvetsabe, chidwi changa pa zinthu zachipembedzo chinayamba kuchepa.

Chaka chotsatira ndinaitanidwa ku msonkhano wamachiritso ku Abidjan, likulu la dziko la Ivory Coast, pamtunda wa makilomita 150 kuchokera kumudzi kwathu ku Vavoua. Tisananyamuke, ndinauza akuluakulu a kutchalitchi kuti ndilibe ndalama zokalowera kumsonkhanowo ndiponso zokapezera chakudya. Iwo anandiuza mawu osonyeza kuti ndikakafika ku Abidjan ndikasamalidwa bwinobwino, koma si mmene zinayendera. Ngakhale kuti ndinali m’kati mwa chikhamu cha anthu pafupifupi 40,000 kapena 50,000, ndinali wosungulumwa ndiponso wosasangalala. Aliyense ankangondinyalanyaza.

Ndinabwerera kwathu ku Vavoua matenda anga aja ali chikhalire, koma apa n’kuti nditasokonezekanso maganizo posadziwa chochita. Akuluakulu a tchalitchi ya kwathu kuja anandiuza kuti Mulungu sanandichiritse chifukwa choti ndilibe chikhulupiriro. Zitatero, ndinasiyiratu kupita kutchalitchi.

Ndinalimbikitsidwa Mwauzimu

Mu 1996 munthu wina wa Mboni za Yehova anafika pakhomo pathu. Ndinali ndisanalankhulanepo ndi wa Mboni, koma ndinamvetsera nawo nkhani zosangalatsa zimene mchimwene wanga ndi wa Mboniyo anali kukambirana. Mchimwene wangayo analibe nazo chidwi, koma ine zinandichititsa chidwi. Mawu aliwonse amene wa Mboniyo anali kunena ankandifika pamtima.

Iye analongosola kuti uchimo wa anthu onse unachokera pa kusamvera kwa munthu woyamba. Kugalukira kumeneko kunachititsa kuti anthu onse akhale opanda ungwiro ndiponso kuti azifa. Koma Yesu anapereka moyo wake kuti ukhale dipo pofuna kuti machimo athu athe kukhululukidwa ndi kuti tithe kudzakhala ndi moyo wosatha. (Aroma 3:23; 5:12, 17-19) Kuphatikizanso apo, wa Mboniyo anandisonyeza m’Baibulo kuti posachedwapa, Yehova Mulungu, kudzera mwa Ufumu wake, adzasintha dzikoli kuti likhale paradaiso ndipo adzachotsa uchimo ndi zovuta zonse zobwera chifukwa cha uchimo.—Yesaya 33:24; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4.

Ziphunzitso za m’Baibulozi zinandifika pamtima ndipo zinandikhudza kwabasi. Wa Mboniyu dzina lake anali Robert, ndipo anakonza zoti aziphunzira nane Baibulo kawiri pa mlungu. Patangotha miyezi yochepa chabe, ndinadziwa zinthu zambiri za m’Baibulo, motero ndinayamba kupita ndi a Mboniwo mu utumiki wawo wa khomo ndi khomo. Zimenezi zinali zovuta, chifukwa choti ndinkamangika kwambiri ndi anthu.

Kukumana ndi Mavuto

Achibale anga sanasangalale kuti ndikuphunzira Baibulo. Pofuna kundipsetsa mtima, mchimwene wanga ankasuta fodya m’chipinda ine ndikugona usiku. M’mawa mutu unkandiwawa ndipo ndinkadwala. Vuto linanso linali chakudya chathu. Bambo anali mlenje waluso kwambiri, ndipo chakudya chachikulu chimene tinkadya pabanja pathu chinali nyama zimene ankabweretsa kuulenjeko. Ndinawalongosolera kuti Baibulo limaletsa kudya nyama yosazinga. (Machitidwe 15:28, 29) Komabe iwo anakana kumazinga nyamazo. Nthawi zina mayi ankaika mpunga wanga padera popanda kuuphatikiza ndi nyamayo, koma nthawi zambiri sindinkadya chakudya chokwanira.

Ngakhale kuti Nyumba ya Ufumu ya ku Vavoua inali kutali ndi kwathu, ndinkapitabe kumisonkhano ngakhale kunja kukapanda kucha bwino. Ndinabatizidwa mu September 1997 pa Msonkhano Wachigawo wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” wa ku Ivory Coast. Ndinapita patsogolo mu utumiki wanga n’kukhala mpainiya, kapena kuti mtumiki wa nthawi zonse wa Mboni za Yehova.

Mavuto Enanso

Mikangano ya zandale inachititsa nkhondo yapachiweniweni mu September 2002. M’milungu yochepa chabe, asilikali aboma anali atayandikira ku Vavoua. Poopa kuphedwa, anthu ena anathawa, kuphatikizaponso a Mboni za Yehova ambiri. Patatha masiku asanu chichokereni anthuwo asilikali analanda tauniyo ndipo nthawi yomweyo analetsa kuchita msonkhano uliwonse. Zitatero, anthu ambiri a ku Vavoua anabalalika, kuphatizapo a Mboni onse amene anatsala.

Popeza kuti kunalibe mabasi aliwonse, anthu ankayenda ulendo wautali kuti akafike m’matauni oyandikana nawo. Ndinalephera kuyenda ulendo wautali choncho, motero wa Mboni ndinatsala ndekha ku Vavoua. Ndinapitiriza kulalikira, ndipo anthu ena a kumeneku ankabwera ku misonkhano ya mpingo imene ndinkachititsa.

Ndinayesetsa Kuti Ndikapezeke ku Msonkhano

M’tauni ya Daloa anakonza tsiku la msonkhano wapadera wa Mboni za Yehova m’mwezi wa November. Ndinapemphera kwa Yehova kuti ndikufuna kukakhala nawo pamsonkhanowu. Kenaka wa Mboni wina amene anali atachoka kale anabwerera mwadzidzidzi. Ndinam’pempha kuti anditenge panjinga yake kupita ku malo amsonkhanowo, omwe anali pamtunda wa makilomita 50. Iye anavomera mosavuta, ngakhale kuti nayenso anali ndi zilema zazikulu.

Anthu ambiri mitima inali m’mwamba motero tinaona kuti sibwino kuti tinyamuke panthawiyi. Analetsa magalimoto onse ochoka ku Vavoua kupita ku Daloa. Msilikali wa gulu lililonse pa magulu omenyanawo akanatha kuwombera munthu wosadziwika wapaulendo chifukwa chomukayikira. Komabe, Loweruka m’mawa, pa November 9, 2002, tinanyamuka ku Vavoua panjinga n’kulowera ku Daloa, monga ndalongosolera pachiyambi pa nkhani ino.

Posakhalitsa tinafika pa malo oyamba amene asilikali ankasecherapo anthu apaulendo. Anatisecha paliponse ndipo anatilola kupita. Ulendo wathu unali wautali ndiponso wotopetsa. Pokwera chitunda tinkayenda pansi ndipo njingayo tinkaikwera pamtsetse pokhapokha kuti iziyenda popanda kupalasa.

Kenaka, wanjinga wina anatikomera mtima n’kundikweza pa kaliyala ya njinga yake. Munthuyu akupalasa njingayo, ineyo ndinapezerapo mwayi womuuza za Ufumu wa Mulungu. Ndinamulongosolera kuti boma la Mulungu ndi la kumwamba ndi kuti posachedwapa lidzabweretsa mtendere wosatha padziko lapansi pano. Anachita chidwi zedi ndipo anandifunsa mafunso ambiri. Titafika ku Daloa, iye anatigulira chakudya n’kulonjeza kuti mawa lake, adzakhalapo pa tsiku la msonkhano wapadera.

Ku Daloa tinafika madzulo, tili otopa koma osangalala kuti tafika. Ulendo wathu wa maola naini unali wovuta kwambiri. Anthu a m’banja lina la Mboni la kumeneku anatilandira bwino kwambiri ndipo anatiuza kuti tikhale kunyumba kwawo mpaka kudzakhale bata. N’zomvetsa chisoni kuti msonkhano uja unalephereka chifukwa cha mikangano ya zandale ija. Komabe sikuti tinayenda ulendo wachabe. Ulendowu unathandiza kuti ndilandire maudindo ena potumikira Akristu anzanga ku Daloa.

Ndadalitsidwa Chifukwa cha Khama

Tsopano ndine mtumiki wothandiza ndiponso mpainiya wokhazikika mu mpingo wina wa ku Daloa. Ndimathandizanso kukonza Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Daloa. Ndimagulitsa agulugufe osema ndekha pofuna kupeza ndalama zodzithandizira, komanso ndimalemba zikwangwani.

Kwa zaka zambiri ndinkachoka panyumba popita kusukulu basi, koma panopo ndayenda maulendo ambirimbiri pofunafuna anthu ofuna kudziwa choonadi pa nkhani yoti kodi n’chifukwa chiyani timadwala ndi kuvutika chonchi? Panopo, podikira kuti Ufumu wa Mulungu udzachotse matenda ndi zilema zonse, ndikupitirizabe kuuza anthu a ku Ivory Coast uthenga wabwino wolimbikitsa wonena za cholinga cha Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Pa chipembedzo chimenechi amakhulupirira kuti zinyama, zomera, ndi zinthu zina m’chilengedwe zimakhala ndi moyo womatha kudziwa zimene zikuchitika.

[Chithunzi patsamba 13]

Ndikupita kumsonkhano ku Daloa

[Chithunzi patsamba 13]

Kuthandiza kusamalira Nyumba ya Msonkhano yakwathu ku Daloa

[Chithunzi patsamba 13]

Ndimapeza ndalama zodzithandizira pogulitsa agulugufe amene ndimasema