Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 88

Yohane Abatiza Yesu

Yohane Abatiza Yesu

ONANI nkhunda ikutsikira pamutu pa munthu’yo. Iye ndiye Yesu. Ali ndi zaka 30 tsopano. Ndipo uyo ali nayeyo ndi Yohane. Tinaphunzira kale za iye. Mukukumbukira paja pamene Mariya anamka kukachezera wachibale wake Elizabeti, ndipo mwana wa m’mimba mwa Elizabeti analumpha mosangalala? Mwana wosabadwa’yo anali Yohane. Koma kodi Yohane ndi Yesu akuchitanji tsopano?

Yohane wangomiza kumene Yesu m’madzi a Mtsinje wa Yordano. Umu ndimo m’mene munthu amabatizidwira. Choyamba, akumizidwa m’madzi, nabvuulidwa. Chifukwa chakuti izi ndizo zimene iye amachitira anthu, akuchedwa Yohane M’batizi. Koma kodi iye wabatiziranji Yesu?

Eya, iye anakuchita chifukwa chakuti Yesu anadza nam’pempha kum’batiza. Yohane amabatiza anthu amene akufuna kosonyeza kuti ali ndi chisoni chifukwa cha zoipa zimene iwo achita. Koma kodi Yesu anachitapo choipa chiri chonse kwakuti n’kukhala wachisoni? Ai, iye sanachite konse, chifukwa ndiye Mwana wa Mulungu wa kumwamba. Chotero anapempha Yohane kum’batiza kaamba ka chifukwa china. Tiyeni tione chimene chinali chifukwa’cho.

Yesu asanadze kwa Yohane kuno, anali mmisiri wopala matabwa. Mmisiri wa matabwa ndiye munthu wopanga zinthu ndi matabwa, monga ngati matebulo, mipando ndi mabenchi. Mwamuna wa Mariya Yosefe anali mmisiri wa matabwa, ndipo anaphunzitsa’nso Yesu. Koma Yehova sanatumizire Mwana wake pa dziko pano kudzakhala wopala matabwa. Anali ndi ntchito yapadera kaamba ka iye, ndipo nthawi yafika yoti iye aiyambe. Chotero kuti asonyeze kuti tsopano wadza kudzachita chifuniro cha Atate wake, Yesu akupempha Yohane kum’batiza. Kodi Mulungu akukondwera nazo?

Inde, chifukwa, Yesu atabatizidwa natulukamo, mau ochokera kumwamba akuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga, amene ndikondwera naye.’ Ndipo’nso, kukuonekera kuti miyamba ikutseguka nkhunda’yi naitsikira pa Yesu. Koma si nkhunda yeni-yeni. Ikukhala ngati ndiyo. Ndi mzimu woyera wa Mulungu.

Tsopano Yesu ali ndi zochuluka zoziganizira, chotero akumka ku malo a yekha kwa masiku 40. Kumene’ko Satana akudza kwa iye. Katatu Satana akuyesa kuchititsa Yesu kuchita kanthu kena kosemphana ndi malamulo a Mulungu. Koma Yesu sakukachita.

Pambuyo pake, iye akubwerera ndipo akukumana ndi amuna ena amene akukhala atsatiri ake, kapena ophunzira. Ena a maina ao ndiwo Andreya, Petro (wochedwa’nso Simoni), Filipo ndi Natanayeli (wochedwa’nso Bartolomeyo). Yesu ndi ophunzira amene’wa akuchoka kumka ku chigawo cha Galileya. Kumene’ko Yesu akumka ku phwando lalikulu la ukwati, ndipo akuchita chozizwitsa chake choyamba. Kodi mukuchidziwa? Kusandutsa madzi kukhala vinyo.