2 Timoteyo 3:1-17

3  Koma dziwa kuti, masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.+  Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo,+ osayamika, osakhulupirika,+  osakonda achibale awo,+ osafuna kugwirizana ndi anzawo,+ onenera anzawo zoipa,+ osadziletsa, oopsa,+ osakonda zabwino,+  achiwembu,+ osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada,+ okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu,+  ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu+ koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uwapewe.+  Pakati pa anthu amenewa pamachokera anthu amene amalowerera mozemba m’mabanja,+ ndi kugwira amayi osiyanasiyana kuti akhale akapolo awo. Amayiwo amakhala ofooka, olemedwa ndi machimo, ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana,+  amene amakhala akuphunzira nthawi zonse, koma satha kudziwa choonadi molondola.+  Tsopano monga mmene Yane ndi Yambure+ anatsutsira Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi.+ Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri,+ ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.+  Ngakhale zili choncho, iwo sadzapita patali, chifukwa misala yawo idzaonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi misala ya anthu awiri aja.+ 10  Koma iwe wayesetsa kutsatira chiphunzitso changa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga. 11  Ukudziwanso mazunzo ndi masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo,+ ndi ku Lusitara.+ Komabe, Ambuye anandipulumutsa m’mazunzo onsewa.+ 12  Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+ 13  Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+ 14  Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa anthu amene anakuphunzitsa.+ 15  Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke+ kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.+ 16  Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa,+ kudzudzula,+ kuwongola zinthu+ ndi kulangiza m’chilungamo,+ 17  kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino+ ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.+

Mawu a M'munsi