2 Timoteyo 4:1-22

4  Pamaso pa Mulungu ndi pa Khristu Yesu, amene anaikidwiratu kudzaweruza+ amoyo ndi akufa,+ akadzaonekera+ bwinobwino ndiponso akadzabwera mu ufumu wake,+ ndikukulamula mwamphamvu kuti,  lalikira mawu.+ Lalikira modzipereka, m’nthawi yabwino+ ndi m’nthawi yovuta.+ Dzudzula,+ tsutsa, dandaulira. Chita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri.+  Pakuti idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso cholondola,+ koma mogwirizana ndi zilakolako zawo, adzadzipezera aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.+  Iwo adzasiya kumvetsera choonadi, n’kutembenukira ku nkhani zonama.+  Koma iwe ukhalebe woganiza bwino+ pa zinthu zonse, imva zowawa,+ gwira ntchito ya mlaliki,*+ ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.+  Pakuti ine ndayamba kale kukhuthulidwa ngati nsembe yachakumwa,+ ndipo nthawi yakuti ndimasuke+ yatsala pang’ono kukwana.  Ndamenya nkhondo yabwino.+ Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.+ Ndasunga chikhulupiriro.+  Kuyambira panopa mpaka m’tsogolo, andisungira chisoti chachifumu chachilungamo.+ Ambuye, woweruza wolungama,+ adzandipatsa mphotoyo+ m’tsikulo.+ Sadzapatsa ine ndekha ayi, komanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.  Uchite chilichonse chotheka kuti ubwere kwa ine posachedwa.+ 10  Pakuti Dema+ wandisiya chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi* ino,+ ndipo wapita ku Tesalonika. Keresike wapita ku Galatiya,+ ndipo Tito wapita ku Dalimatiya. 11  Luka yekha ndiye amene ali ndi ine. Pobwera utengenso Maliko, pakuti iye ndi wofunika kwa ine chifukwa amandithandiza+ pa utumiki wanga. 12  Koma Tukiko+ ndamutuma ku Efeso. 13  Unditengerekonso chovala champhepo chimene ndinachisiya ku Torowa+ kwa Karipo ndi mipukutu, makamaka yazikopa ija. 14  Alekizanda,+ wosula zinthu zamkuwa uja, anandichitira zoipa zambiri. Yehova adzamubwezera malinga ndi ntchito zake,+ 15  ndipo iwenso uchenjere naye, chifukwa anatsutsa mawu athu mwamphamvu. 16  Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha.+ Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.+ 17  Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine+ ndi kundipatsa mphamvu,+ kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.+ Ndiponso ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.+ 18  Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse+ ndipo adzandisungira ufumu wake wakumwamba.+ Iye apatsidwe ulemerero mpaka muyaya. Ame. 19  Undiperekere moni kwa Purisika+ ndi Akula, ndi banja la Onesiforo.+ 20  Erasito+ anatsalira ku Korinto,+ koma Terofimo+ ndinamusiya akudwala ku Mileto.+ 21  Uchite chilichonse chotheka kuti ufike kuno nyengo yachisanu isanayambe. Ebulo, Pude, Lino ndiponso Kalaudiya ndi abale onse, akupereka moni. 22  Ambuye akhale nawe chifukwa cha mzimu umene umaonetsa.+ Kukoma mtima kwake kwakukulu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

“Mlaliki” palembali akutanthauza “mmishonale.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.