2 Petulo 2:1-22
2 Komabe, pakati pa anthuwo panadzakhala aneneri onyenga. Momwemonso padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.+ Amenewa adzabweretsa mwakachetechete timagulu tampatuko towononga ndipo adzakana ngakhale iye amene anawagula,+ n’kudzibweretsera chiwonongeko chofulumira.
2 Kuwonjezera apo, ambiri adzatsatira+ khalidwe lotayirira+ la aphunzitsiwo, ndipo chifukwa cha amenewa, anthu adzalankhula monyoza njira ya choonadi.+
3 Komanso chifukwa chosirira mwansanje, adzakudyerani masuku pamutu ndi mawu achinyengo.+ Koma chiweruzo chawo chimene chinagamulidwa kalekale+ chikubwera mofulumira, ndipo chiwonongeko chawo sichikuzengereza.+
4 Ndithu, Mulungu sanalekerere angelo+ amene anachimwa aja osawapatsa chilango, koma mwa kuwaponya mu Tatalasi,*+ anawaika m’maenje a mdima wandiweyani powasungira chiweruzo.+
5 Anaperekanso chilango padziko lakale lija ndipo sanalilekerere,+ koma anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo,+ pomupulumutsa pamodzi ndi anthu ena 7,+ pamene anabweretsa chigumula+ padziko la anthu osaopa Mulungu.
6 Anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto,+ kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.+
7 Koma anapulumutsa Loti, munthu wolungama+ amene anavutika mtima kwambiri ndi kulowerera kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayirira.+
8 Munthu wolungama ameneyo anali kuzunzika tsiku ndi tsiku ndi zimene anali kuona ndi kumva pamene anali kukhala pakati pawo, ndiponso chifukwa cha zochita zawo zosamvera malamulo.
9 Chotero, zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.+ Koma anthu osalungama amawasungira tsiku loweruza kuti adzawawononge,+
10 koma makamaka anthu amene amafunafuna kugonana ndi anthu ena n’cholinga choti awaipitse,+ ndiponso amene amanyoza owalamulira.+
Anthu amenewa ndi opanda mantha ndiponso ndi omva zawo zokha, ndipo sanjenjemera ndi anthu aulemerero. M’malomwake, amalankhula zinthu zowanyoza.+
11 Koma angelo, ngakhale kuti ndi amphamvu kwambiri, saneneza aphunzitsi onyengawo ndi mawu onyoza,+ pakuti amalemekeza Yehova.+
12 Ndipo anthu amenewa, mofanana ndi nyama zopanda nzeru zimene zimabadwira kuti zidzagwidwe ndi kuwonongedwa, amalankhula monyoza za zinthu zimene sakuzidziwa,+ moti adzawonongedwa chifukwa cha njira yawo yachiwonongeko,
13 ndipo akudzilakwira okha+ monga mphoto yawo ya kuchita zoipa.+
Iwo amaona kuti kuchita masana zinthu zokhutiritsa chilakolako cha thupi lawo n’kosangalatsa.+ Anthu amenewa ali ngati mawanga ndi zilema pakati panu, ndipo amakondwera kwadzaoneni akamakuphunzitsani zinthu zonyenga pamene akudya nanu limodzi.+
14 Ali ndi maso odzaza ndi chigololo+ komanso olephera kupewa kuchita tchimo,+ ndipo amakopa anthu apendapenda. Ali ndi mtima wophunzitsidwa kusirira mwansanje.+ Iwo ndi ana otembereredwa.+
15 Popeza anasiya njira yowongoka, asocheretsedwa. Atsatira njira ya Balamu+ mwana wa Beori, amene anakonda mphoto ya kuchita zoipa,+
16 koma anadzudzulidwa pa cholakwa chake.+ Nyama yosalankhula yonyamula katundu inalankhula ngati munthu+ ndi kulepheretsa zochita zamisala za mneneriyo.+
17 Amenewa ndi akasupe opanda madzi,+ ndi nkhungu yotengeka ndi mphepo yamkuntho, ndipo anawasungira mdima wandiweyani.+
18 Pakuti amalankhula mawu odzitukumula opanda pake, ndipo pogwiritsa ntchito zilakolako za thupi+ komanso makhalidwe otayirira, amakopa+ amene akungopulumuka+ kumene kwa anthu ochita zolakwa.
19 Pamene akuwalonjeza ufulu,+ eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa.+ Pakuti aliyense amene wagonjetsedwa, amakhala kapolo kwa womugonjetsayo.+
20 Ndithudi, ngati anapulumuka ku zoipitsa za dzikoli+ mwa kumudziwa molondola Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, koma alowereranso m’zinthu zomwe zija ndi kugonjetsedwa nazo,+ potsirizira pake makhalidwe awo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba.+
21 Zikanakhala bwino akanapanda kudziwa molondola njira ya chilungamo,+ kusiyana n’kuidziwa bwinobwino kenako n’kupatuka pa lamulo loyera lomwe anapatsidwa.+
22 Mwambi woona uja wakwaniritsidwa pa iwo. Mwambiwo umati: “Galu+ wabwerera kumasanzi ake, ndipo nkhumba imene inasambitsidwa yapita kukagubudukanso m’matope.”+
Mawu a M'munsi
^ “Tatalasi” ndi mkhalidwe wonyozeka wofanana ndi kukhala m’ndende. Uwu ndiwo mkhalidwe umene Mulungu anaikamo angelo osamvera m’nthawi ya Nowa.”