Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera M’dzina la Yesu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera M’dzina la Yesu?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu anakonza zoti ngati tikufuna kuti iye amve mapemphero athu, tizipemphera m’dzina la Yesu basi. Yesu anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Iye anauzanso atumwi ake okhulupirika kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yohane 16:23.

Zifukwa zina zopempherera m’dzina la Yesu

  •   Timasonyeza kuti timalemekeza Yesu ndiponso Atate wake Yehova Mulungu.—Afilipi 2:9-11.

  •   Timasonyeza kuti timayamikira Mulungu chifukwa chakuti anatumiza Yesu kudzatifera kuti tipulumutsidwe.—Mateyu 20:28; Machitidwe 4:12.

  •   Timasonyeza kuti tikudziwa zoti Yesu ndi mkhalapakati wa ife ndi Mulungu.—Aheberi 7:25.

  •   Timasonyeza kuti tikulemekeza udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe amene angatithandize kuti tikhalenso paubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Aheberi 4:14-16.