JANUARY 21, 2019
ZATSOPANO
Baibulo la Dziko Latsopano Linatulutsidwa M’chiyankhulo cha Chitagalogi
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso linatulutsidwa m’chiyankhulo cha Chitagalogi pa 20 January, 2019 ku Quezon City m’dziko la Philippines. Baibulo la Dziko Latsopano lamasuliridwa lathunthu kapena mbali zake zina m’ziyankhulo 179 kuphatikizapo m’ziyankhulo 19 zomwe zakonzanso Mabaibulo awo mogwirizana ndi Baibulo lomwe linatulutsidwa mu 2013.

