Uzbekistan
Makhoti Akuluakulu ku Uzbekistan Anagwirizana ndi Zoti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wokhala ndi Mabuku Ofotokoza za Baibulo
Zigamulo zaposachedwapa zomwe makhoti akuluakulu anapanga, zathandiza kuti abale athu asakhale ndi milandu ndipo sakuyenera kupereka chindapusa.
Kodi Zinthu Ziyamba Kuwayendera Bwino a Mboni za Yehova ku Uzbekistan?
Zikuonetsa kuti akuluakulu a boma la Uzbekistan, akuyesetsa kuti ayambe kulemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu. A Mboni za Yehova akukhulupiriranso kuti posachedwapa, akuluakulu a boma akhoza kuvomereza kuti alembetse mipingo yawo yatsopano.