Pitani ku nkhani yake

NOVEMBER 1, 2018
SOUTH KOREA

Chigamulo Chosaiwalika cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea

Chigamulo Chosaiwalika cha Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea

Lachinayi pa 1 November, 2018, Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea linagamula kuti si mlandu kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene umakhulupirira. Pa oweruza 13 omwe ankaweruza nkhaniyi, 9 ndi amene anagwirizana ndi zoti kuchita zimenezi si mlandu pamene 4 ananena kuti ndi mlandu. Malinga ndi chigamulochi, kukana kulowa usilikali chifukwa cha chipembedzo ndi “chifukwa chomveka.” Chigamulo chomwe khoti lalikulu kwambiri ku South Korea lapangachi n’chosaiwalika, ndipo chithandiza kuti makhoti ena onse m’dzikoli, aweruze mokomera abale oposa 900 omwe akuyembekezera kuti milandu yawo izengedwe.

Kumayambiriro kwa chaka chino, Khoti Loona za Malamulo a Dziko la Korea linagamula kuti pomafika mu December 2019, anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, azipatsidwa ntchito zina m’malo mwa usilikali.

Tikusangalala komanso kutamanda Yehova chifukwa cha chigamulo chosaiwalika chimenechi.