Pitani ku nkhani yake

25 JANUARY, 2017
SOUTH KOREA

“Chigamulo cha Khoti Chabwino Kwambiri Chaka Chino”

“Chigamulo cha Khoti Chabwino Kwambiri Chaka Chino”

Khoti la apilo linapeza kuti anyamata atatu omwe mayina awo ndi Hye-min Kim, Lak-hoon Cho, komanso Hyeong-geun Kim ndi osalakwa ndipo anasangalala kwambiri kuti sanagamulidwe kuti akakhale kundende. Mlandu umene anyamatawa ankazengedwa unali wokhudza kukana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Chigamulochi chinali chodabwitsa kwambiri chifukwa amuna ambiri ku South Korea amamangidwa chaka chilichonse chifukwa chokana usilikali. Mlandu wofanana ndi umenewu unachititsa kuti azibambo a anyamatawa komanso anthu ena okwana 19,000, aikidwe m’ndende ndipo anyamatawa ankayembekezera kuti nawonso aikidwa m’ndende. Chigamulo choti anyamatawa si olakwa chomwe chinaperekedwa ndi Khoti la Apilo la Gwangju, chithandiza anthu kusintha maganizo awo pankhaniyi.

Khoti la Apilo Lapereka “Chigamulo Chabwino Kwambiri Chaka Chino”

Nyumba zofalitsa nkhani pafupifupi 200 zinaulutsa nkhaniyi. Ofalitsa nkhaniwa anatsindika kuti chigamulo choyambachi choti anthu amene akana usilikali ndi osalakwa chomwe khoti la apilo linapereka, ndi chabwino kwambiri. Ndipo anafotokozanso kuti anthu ambiri akuchita chidwi ndi nkhaniyi. Nyuzipepala ina inanena kuti ichi ndi “chigamulo chabwino kwambiri chimene khoti lapanga chaka chino.” Nyuzipepala inanso inaika chigamulochi m’gulu la zigamulo 5 zapamwamba zimene zinachitika ku South Korea mu 2016.

Zimene khoti la apiloli linagamula zikusonyeza kuti akatswiri a zamalamulo komanso oweruza milandu akusintha maganizo awo pankhaniyi. Pa milandu ingapo yaposachedwapa, oweruza milandu anaona kuti azibambo a Mboni ankakana ntchito ya usilikali chifukwa choti amatsatira kwambiri mfundo za makhalidwe abwino komanso zimene amakhulupirira. Iwo anaonanso kuti kukakamiza a Mboniwo kugwira ntchito ya usilikali kapena kuwalanga chifukwa chokana usilikali kukhoza kuphwanya ufulu wawo wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chawo. Oweruza milanduwo ananena kuti anthuwo anali ndi zifukwa zomveka zokanira ntchito ya usilikali. M’malo moona azibambo a Mboniwo kuti akuthawa usilikali, oweruza milandu anapereka zigamulo zinanso zokwana 16 zokomera anthu okana usilikali pa miyezi 20 yapitayi.

Loya wina dzina lake Du-jin Oh, yemwe wakhala akuimira anthu ambiri okana ntchito ya usilikali anati: “Kusinthaku ndi kofunika kwambiri.” Loyayu ananenanso kuti: “Ndine wosangalala chifukwa cha kuchuluka kwa zigamulo zokomera anthu okana usilikali, komanso kuti posachedwapa zigamulo zoterezi zakhala zikupangidwa ndi khoti lalikulu. Chigamulo choterechi chikaperekedwa, loya woimira boma amayembekezeredwa kupanga apilo nkhaniyo. Koma kusintha maganizo kwa oona zamalamulo a ku South Korea pankhaniyi, kuthandizanso kwambiri Khoti Loona za Malamulo a Dziko pa milandu yomwe likuyembekezera kugamula yokhudza ufulu wa munthu wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake.”

Kufunafuna Njira Yothetsera Vutoli

Aliyense akuyembekezera kuti Khoti Loona za Malamulo a Dziko ku South Korea lipereke chigamulo chake. Khotili likuwunika ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima umene malamulo oyendetsera dzikolo amapereka, n’kuuyerekezera ndi chilango chimene munthu ayenera kulandira akakana ntchito ya usilikali pogwiritsa ntchito ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira kapena chipembedzo chake.

A Dae-il Hong, omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku South Korea anati: “Mabanja masauzande ambiri akusangalala ndi chigamulo chimene chikulemekeza zosankha za anyamata omwe sakufuna kukakamizidwa kulowa usilikali malinga ndi zimene amakhulupirira. Tikuyembekezera mwachidwi chigamulo cha Khoti Loona za Malamulo a Dziko chomwe chingagwirizane ndi zosankha za anyamatawa.”