Pitani ku nkhani yake

Nyumba ya banja lina la Mboni yomwe inapseratu ndi motowu

APRIL 25, 2019
SOUTH KOREA

Moto Wolusa Unayaka M’dera la M’mbali mwa Nyanja Kum’mawa kwa South Korea

Moto Wolusa Unayaka M’dera la M’mbali mwa Nyanja Kum’mawa kwa South Korea

Pa 4 April, 2019, moto wamphamvu wa m’nkhalango unayaka m’dera la m’mphepete mwa nyanja m’chigawo cha Gangwon ku South Korea. Motowu unafalikira mofulumira kwambiri ndipo zimenezi zinachititsa boma kulengeza kuti dzikolo lakumana ndi vuto lalikulu kwambiri. Ozimitsa moto asanachepetse motowu, unali utawononga kale maekala oposa 4,000 komanso kupha anthu awiri.

Malipoti ochokera ku ofesi ya nthambi akusonyeza kuti palibe wa Mboni aliyense yemwe anavulala kapena kufa ndi motowu. Komabe, nyumba 8 zinaonongeka ndipo abale ndi alongo athu 27 anakhudzidwa. Mogwirizana ndi malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi, Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi ndiponso woyang’anira dera m’chigawochi, akugwira ntchito limodzi ndi akulu m’mipingo polimbikitsa anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi ndi mfundo za m’Baibulo komanso kuwapatsa chithandizo.

Tikukhulupirira kuti, kwa abale athu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi, Yehova akhala ‘pothawira pawo ndi mphamvu yawo, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.’—Salimo 46:1.