6 JULY 2026
RUSSIA
Mlongo Irina Shishkina
“Musaope”
Pa 29 June 2026, Khoti la m’chigawo cha Rudnichniy ku Prokopyevsk linapeza kuti Mlongo Irina Shishkina ndi wolakwa ndipo linagamula kuti azitsatira malamulo ena ake ali kunyumba kwawo kwa zaka 4. Koma panopa sakufunika kupita kundende.
Zokhudza Mlongoyu
Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kuthandiza komanso kulimbitsa anthu ake pamene tikupirira mokhulupirika mavuto a m’masiku otsiriza ano.—Ekisodo 14:13.

