Malo a Nkhani
A Mboni za Yehova Asaina Pangano Logulitsa Nyumba Zawo ku Brooklyn
A Mboni akugulitsa nyumba zawo zomwe zili ku Brooklyn, zomwe poyamba ankazigwiritsa ntchito posindikiza mabuku awo. Iwo akugulitsanso nyumba yogona yosanja ka 30. Iwo akugulitsa nyumbazi chifukwa akufuna kusamutsira likulu lawo ku Warwick, New York.
Khoti la ku Ulaya Lateteza Ufulu wa Mboni za Yehova pa Mlandu Wokhudza Kusungiridwa Chinsinsi
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lalamula boma la Russia kuti lipereke chipukuta misozi kwa anthu amene linawaphwanyira ufulu wachibadwidwe wofunika kwambiri wokhudza kusungiridwa chinsinsi.
A Mboni za Yehova Akonzanso Nyumba Yakalekale Yophunzirira Baibulo
A Mboni za Yehova anatsegulira nyumba yakalekale yotchedwa Stanley ku Jersey City, m’chigawo cha New Jersey pambuyo poikonzanso kwa miyezi 6.
Dziko la Germany Lapereka Mendulo Yaulemu kwa Mayi Wina wa Mboni za Yehova Poyamikira Ntchito Yake Yotamandika
Mathilde Hartl analandira mendulo yaulemu imene boma la Germany limapereka kwa anthu okhawo amene achita zinthu zazikulu. Anapereka menduloyi ndi nduna yaikulu ya chigawo cha Bavaria.
A Mboni za Yehova Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Australia
Mphepo yotchedwa Tropical Cyclone Oswald inayambitsa mvula yamphamvu ku Australia. A Mboni za Yehova a m’derali anakhazikitsa komiti yopereka chithandizo kuti ithandize anthu okhudzidwa.
Khoti Linagamula kuti, “Sitili M’chaka cha 1937”
Woweruza milandu wa m’bwalo la milandu lalikulu ku Russia anatsutsa chigamulo chimene khoti laling’ono linalamula
Bungwe la UN Lauza Boma la Turkey Kuti Lizilemekeza Zimene Anthu a M’dzikolo Amakhulupirira
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chigamulo chimene bungwe la UN linapereka chopatsa anthu a ku Turkey ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Khoti Lalamula Dziko la Armenia Kuti Lipereke Chipukuta Misozi kwa Anthu 17 a Mboni za Yehova
Pa November 27, 2012, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linalamula dziko la Armenia kuti lipereke chipukuta misozi cha ndalama zokwana madola 145,226 kwa anthu 17 chifukwa chowaphwanyira ufulu. Anthuwa anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Kavidiyo: Ku Manhattan Kwayambika Ntchito Yapadera
A Mboni za Yehova ku Manhattan mumzinda wa New York, ayambitsa ntchito yapadera yogawira mabuku awo ofotokoza nkhani za m’Baibulo a m’zinenero zosiyanasiyana. Iwo akumaika mabukuwo pamatebulo omwe akumawaika m’malo osiyanasiyana ku Grand Central Station. Kodi anthu akunena zotani?
Timavidiyo: Japan: Moyo ukuyambiranso ku Japan patapita chaka chimodzi chivomezi chitachitika
Anthu a Mboni za Yehova akupitiriza kuthandiza anthu amene anapulumuka kutachitika chivomezi ndi madzi osefukira.