Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 3, 2012
ARMENIA

Khoti Lalamula Dziko la Armenia Kuti Lipereke Chipukuta Misozi kwa Anthu 17 a Mboni za Yehova

Khoti Lalamula Dziko la Armenia Kuti Lipereke Chipukuta Misozi kwa Anthu 17 a Mboni za Yehova

STRASBOURG, France​—⁠Pa November 27, 2012, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linalamula dziko la Armenia kuti lipereke chipukuta misozi cha ndalama zokwana madola 145,226 kwa anthu 17 chifukwa chowaphwanyira ufulu. Anthuwa anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

M’chaka cha 2005, anyamata 17 a Mboni za Yehova ankagwira ntchito imene anapatsidwa kuti azigwira m’malo molowa usilikali. Kenako anazindikira kuti ntchitoyo inali yogwirizana ndi zausilikali ndipo inkayang’aniridwa ndi asilikali. Iwo anazindikira kuti zimenezi zinali zosemphana ndi zimene amakhulupirira ndipo anasiya kugwira ntchitoyo. Izi zinachititsa kuti amangidwe komanso kuimbidwa mlandu. Ena anatsekeredwa m’chitokosi kwa miyezi ingapo akudikirira kuimbidwa mlandu ndipo patapita nthawi anthu 11 anaweruzidwa kuti akakhale kundende ena zaka ziwiri ena zitatu.

Khoti la ku Ulaya linaweruza kuti dziko la Armenia linalakwa kuimba mlandu komanso kumanga anthuwa chifukwa m’chaka cha 2005, m’dzikoli munalibe lamulo loimba mlandu munthu amene wasiya kugwira ntchito imene anapatsidwa atakana kulowa usilikali. Khotili linati dziko la Armenia linaphwanyira anthu a Mboniwa ufulu wochita zimene akufuna komanso ufulu wotetezedwa umene umapezeka pagawo 5 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Ngakhale kuti pambuyo pake dziko la Armenia linathetsa mlandu wa anthu 17 a Mboniwa, dzikoli linakana kupatsa anthuwa chipukuta misozi chifukwa chowaimba mlandu komanso kuwatsekera m’ndende popanda mlandu. Choncho khotili linalamula dziko la Armenia kuti lipereke ndalama za chipukuta misozi kwa anthuwa komanso ndalama zimene zinawonongedwa poyendetsa mlanduwu.

Khoti la ku Ulaya linapereka chigamulochi limodzi ndi zigamulo zina zitatu zokhudzana ndi zimene dziko la Armenia linkachitira anthu okana kulowa usilikali. Pa milandu 4 yonseyi, akuluakulu a dziko la Armenia anapezeka olakwa pa nkhani yochitira nkhanza anthu a Mboni za Yehova amene ankakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndipo a Mboniwa ankapatsidwo chilango ngati kuti anali zigawenga zoopsa.

Bambo André Carbonneau, omwe ndi loya wa anthu 17 a Mboniwa, ananena kuti: “Zimene khotili lagamula pa nkhaniyi zithandiza kuthetsa zinthu zopanda chilungamo zimene a Mboni za Yehova akuchitiridwa. Zithandizanso kuti mayiko ena a ku Ulaya, komanso mayiko ena monga Eritrea ndi South Korea, ndiponso mayiko a m’dera la pakati pa Asia, kuti ayambe kulemekeza ufulu wa anthu a Mboni za Yehova pa nkhani yokana kulowa usilikali.”

Lankhulani ndi:

David Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Armenia: Tigran Harutyunyan, tel. +374 93 900 482