Chichewa
Malo a Nkhani
https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/d71826a198/images/syn_placeholder_sqr.png

Malo a Nkhani

 

2014-11-05

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Zimene a Mboni za Yehova Akuchita Polimbana ndi Ebola

A Mboni za Yehova akuphunzitsa anthu a chipembedzo chawo kuopsa kwa matendawa, m’mene anthu angawatengere, mmene angawapewere komanso zimene angachite kuti asawafalitse.

2014-10-22

RUSSIA

A Mboni za Yehova a ku Samara Apanga Apilo Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe Lawo Lovomerezeka ndi Boma Kukhoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia

Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia liweruza mlandu umene a Mboni za Yehova a ku Samara apanga apilo. Mlanduwu ndi wokhudza kutsekedwa kwa bungwe lawo lovomerezeka ndi boma komanso woti bungweli limachita zinthu monyanyira komanso zosokoneza maganizo a anthu.

2014-11-05

UNITED STATES

Zokhudza Misonkhano ya Mayiko: A Mboni Anachita Msonkhano Wosaiwalika ku Sitediyamu Yotchedwa MetLife

Anthu ambirimbiri anadzazana m’sitediyamu yotchedwa MetLife kummawa kwa Rutherford, NJ, USA, kuti amvere msonkhano wamayiko wakuti ‘Pitirizani Kufunafuna Ufumu Wa Mulungu Choyamba’ pa June 20-22, 2014. Ndi pa June 27-29, 2014.

2014-10-10

ERITREA

Kodi Anthu Amene Atha Zaka 20 Ali M’ndende ku Eritrea Adzatuluka?

Azibambo atatu a Mboni atha zaka 20 ali m’ndende popanda kuimbidwa mlandu. Enanso ambiri ali m’ndende. Kodi dziko la Eritrea lidzasiya kuzunza anthu chifukwa cha chipembedzo chawo?

2014-10-22

TURKMENISTAN

Mayi Wina Watulutsidwa Kundende M’dziko la Turkmenistan

Bibi Rahmanova anatulutsidwa m’ndende mwadzidzidzi pa September 2, 2014. Ngakhale kuti mayiko ndi mabungwe ena anadandaula za nkhaniyi, oweruza sanathetse mlanduwu.

2014-10-07

GERMANY

Ku Sachsenhausen Kunachitika Mwambo Wokumbukira wa Mboni za Yehova Yemwe Anaphedwa ndi Chipani cha Nazi

Pa September 16, 2014, Bungwe la Brandenburg Memorials Foundation linachita mwambo wokumbukira kuti patha zaka 75 kuchokera pamene a August Dickmann anaphedwa kundende ya Sachsenhausen. Iwowa anali oyamba kuphedwa anthu ena akuona, pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndi chipani cha Nazi chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira.

2014-10-07

UNITED STATES

Mayi Lillian Gobitas Klose Anamwalira Ali ndi Zaka 90

Zimene anasankha zosachitira ulemu mbendera zinachititsa kuti mlandu wawo ukaweruzidwenso ndi khoti lalikulu kwambiri m’dziko la United States.

2014-10-10

TURKMENISTAN

Mayi wa Mwana Wazaka 4 ku Turkmenistan Amuweruza Mopanda Chilungamo Kuti Akakhale Kundende

Dziko la Turkmenistan limakonda kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova komanso kuwaphwanyira ufulu wachibadwidwe. Mayi Bibi Rahmanova ndi banja lawo akuchitiridwa zopanda chilungamo ndi akuluakulu a boma a ku Dashoguz.

2014-08-19

NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni Ayamba Ntchito Yodziwitsa Anthu za Webusaiti Yawo ya JW.ORG, Yomwe Ayimasulira M’zinenero Zambiri

Pa 1 August, a Mboni za Yehova anayamba ntchito yapadera yodziwitsa anthu za webusaiti yawo ya jw.org komanso akugawira kapepala kakuti, Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?

2014-08-19

RUSSIA

Khoti la ku Taganrog Lapeza a Mboni za Yehova Kuti ndi Olakwa Chifukwa Chochita Zinthu Zokhudzana ndi Chipembedzo Chawo

Ufulu wolambira wa a Mboni 160,000 ku Russia, uli pangozi chifukwa cha chigamulochi.

2014-08-19

UKRAINE

Anthu Akuvulazidwabe ku Ukraine Chifukwa Chakuti Olakwa Sakupatsidwa Chilango

Anthu omwe akuvutitsa anzawo chifukwa chodana ndi chipembedzo chawo sakupatsidwa chilango chilichonse. A Mboni za Yehova omwe ndi anthu okonda mtendere akupitirizabe kuvutitsidwa.

2014-08-19

CROATIA

A Mboni Anathandiza Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi ku Balkans

Nthawi yomweyo a Mboni za Yehova anayamba kuthandiza ndiponso kulimbikitsa anthu omwe anakhudzidwa ndi ngozi ya madzi osefukira ya pa May 2014 yomwe sinachitikepo ku Bosnia-Herzegovina, Croatia ndi Serbia.

2014-08-19

A Mboni za Yehova Analandira Ulemu Pamwambo Wokumbukira Anthu Amene Anazunzidwa M’ndende ya Gusen

Pa April 13, 2014, Anaika chipilala chokumbukira anthu 450 Mboni amene anamangidwa ndi chipani cha Nazi m’ndende ya Mauthausen ndi Gusen ku Austria.

2014-08-19

UKRAINE

Lipoti Lokhudza Mboni za Yehova ku Ukraine ndi ku Crimea

A Mboni za Yehova adzachita misonkhano yoposa 40 ku Ukraine ndi ku Crimea ngakhale kuti m’mayikowa zinthu sizikuyenda bwino. Misonkhanoyi idzafotokoza za mmene anthu tizidzakhalira mwantendere Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira.