Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 80

“Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

“Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

(Salimo 34:8)

  1. 1. Kutumikira Mulungu

    Kumatisangalatsadi.

    Kulalikira ndikofunika,

    Timakupezera nthawi.

    (KOLASI)

    Mawu akuti: ‘Talawani

    Yehova ndi wabwino.’

    Atidalitsa tikachita

    Zonse zomwe tingathe.

  2. 2. Mtumiki wanthawi zonse

    M’lungu amamudalitsa.

    Amamupatsa zofunikira.

    Amakhala wokhutira.

    (KOLASI)

    Mawu akuti: ‘Talawani

    Yehova ndi wabwino.’

    Atidalitsa tikachita

    Zonse zomwe tingathe.