NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) August 2015

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa September 28 mpaka October 25, 2015.

MBIRI YA MOYO WANGA

“Zilumba Zambiri Zisangalale”

Werengani mbiri ya moyo wa Geoffrey Jackson, wa m’Bungwe Lolamulira.

Tiziganizira Kwambiri Chikondi cha Yehova

N’chiyani chingakuthandizeni kukhulupirira kuti Yehova ali nanu ngakhale pa nthawi ya mavuto?

Tiziyembekezerabe

Pali zifukwa ziwiri zikuluzikulu zotichititsa kukhala maso kwambiri nthawi yamapeto ino.

Tizikonzekera Moyo wa M’dziko Latsopano

Anthu a Mulungu ali ngati anthu amene akukonzekera kusamukira m’dziko lina.

Tizisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo M’masiku Otsiriza Ano

Tiyenera kusamala posankha anzathu, zinthu zimene timawerenga, kumvetsera ndiponso kuonera.

Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Chitsanzo cha Jowana?

Kodi anasintha zinthu ziti kuti azitsatira Yesu?

KALE LATHU

“Yehova Anakubweretsani ku France Kuti Muphunzire Baibulo”

Mu 1919 dziko la France linalola kuti anthu a ku Poland asamukire m’dzikolo ndipo izi zinathandiza kuti ena aphunzire Baibulo.