NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) July 2014

M’magaziniyi muli nkhani zimene tiphunzire kuyambira pa September 1 mpaka 28, 2014.

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Micronesia

Anthu ochokera kumayiko ena amene akutumikira kuzilumba za m’nyanja ya Pacific zimenezi nthawi zambiri amakumana ndi mavuto atatu. Kodi amathana nawo bwanji?

“Yehova Amadziwa Anthu Ake”

Kodi “maziko” komanso “chidindo” zotchulidwa pa 2 Timoteyo 2:19 zimatithandiza bwanji kudziwa anthu a Yehova?

Anthu a Yehova Amakana Kuchita Zosalungama

Kodi nkhani yokana kuchita zosalungama ikukhudzana bwanji ndi zimene zinachitika nthawi ya Mose? Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitika pa nthawiyo?

MBIRI YA MOYO WANGA

Bambo Anga Anamwalira Koma Ndinapeza Bambo Ena

Werengani mbiri ya moyo wa M’bale Gerrit Lösch, wa m’Bungwe Lolamulira.

“Inu Ndinu Mboni Zanga”

Kodi kukhala Mboni za Yehova kumatanthauza chiyani?

“Mudzakhala Mboni Zanga”

N’chifukwa chiyani Yesu anati: “Mudzakhala mboni zanga,” osati za Yehova? Tingatani kuti tikhalebe akhama pa ntchito yolalikira?