Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu a Yehova Amakana Kuchita Zosalungama

Anthu a Yehova Amakana Kuchita Zosalungama

“Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.”—2 TIM. 2:19.

1. Tchulani chinthu chofunika pa kulambira kwathu.

KODI mumamva bwanji mukaona dzina lakuti Yehova litalembedwa pamalo ena abwino amene simunayembekezere kulionapo? Muyenera kuti mumachita chidwi kwambiri chifukwa monga Mboni za Yehova, dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri pa kulambira kwathu. Padziko lonse palibe gulu lina la anthu limene limadziwika kwambiri ndi dzinali kuposa ifeyo. Komabe tiyenera kukumbukira kuti timakhalanso ndi udindo chifukwa chodziwika ndi dzina la Mulungu.

2. Kodi tili ndi udindo wotani chifukwa chodziwika ndi dzina la Mulungu?

2 Kungogwiritsa ntchito dzina la Mulungu sikungachititse kuti Yehova azisangalala nafe. Koma tiyeneranso kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za Mulungu. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti anthu a Yehova ayenera ‘kupatuka pa zinthu zoipa.’ (Sal. 34:14) Mtumwi Paulo ananenanso mfundo imeneyi pamene analemba kuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.” (Werengani 2 Timoteyo 2:19.) Popeza kuti ndife Mboni za Yehova timadziwika kuti timatchula dzina  lake. Koma kodi tingapewe bwanji kuchita zosalungama?

PEWANI KUCHITA ZINTHU ZOIPA

3, 4. Kodi ndi mfundo iti imene yakhala ikuimitsa mitu akatswiri a Baibulo ndipo n’chifukwa chiyani?

3 Kodi Paulo ankafotokoza za chiyani pamene analemba mawu a pa 2 Timoteyo 2:19? Ankafotokoza za “maziko olimba a Mulungu” ndipo anatchula mfundo ziwiri zimene zinadindidwa pa mazikowo. Mfundo yoyamba ndi yakuti, “Yehova amadziwa anthu ake,” ndipo zikuoneka kuti ikuchokera pa Numeri 16:5. (Onani nkhani yoyamba.) Mfundo yachiwiri ndi yakuti, “Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama.” Kwa zaka zambiri, mfundo yachiwiriyi yakhala ikuimitsa mitu akatswiri a Baibulo. Chifukwa chiyani zili choncho?

4 Zimene Paulo ananenazi zimaoneka ngati anachita kugwira mawu a lemba linalake. Komatu m’Malemba Achiheberi simupezeka mawu amenewa. Ndiyeno kodi Paulo ankanena za chiyani pamene analemba kuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama”? Pamene iye ankalemba zimenezi, anali atangogwira kumene mawu a mu Numeri chaputala 16. Chaputalachi chimafotokoza za kupanduka kwa Kora. Ndiye kodi tinene kuti mfundo yachiwiriyi ikukhudzanso nkhani ya Kora?

5-7. Kodi pa 2 Timoteyo 2:19, Paulo ankanena za nkhani iti ya m’nthawi ya Mose? (Onani chithunzi patsamba 12.)

5 Baibulo limanena kuti Datani ndi Abiramu, omwe anali ana a Eliyabu, anagwirizana ndi Kora poukira Mose ndi Aroni. (Num. 16:1-5) Iwo ankasonyeza kuti salemekeza Mose ndipo ankatsutsa zoti Mulungu anamupatsa udindo. Anthu oukirawa ankakhalabe limodzi ndi anthu a Mulungu ndipo akanatha kusokoneza atumiki ena okhulupirika. Litafika tsiku loti Yehova asiyanitse anthu okhulupirika ndi opanduka, iye anapereka malangizo omveka bwino.

6 Baibulo limati: “Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Uza khamulo kuti, “Chokani kumahema a Kora, Datani ndi Abiramu!”’ Kenako Mose ananyamuka n’kupita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akulu a Isiraeli anapita naye limodzi. Atafika anauza khamulo kuti: ‘Chonde, chokani kumahema a anthu oipawa, ndipo musakhudze chinthu chawo chilichonse, kuti musaphedwe nawo limodzi chifukwa cha kuchimwa kwawo.’ Nthawi yomweyo anthuwo anachoka kumbali zonse za mahema a Kora, Datani ndi Abiramu.” (Num. 16:23-27) Ndiyeno Yehova anapha opandukawo. Koma atumiki okhulupirika amene anakana zosalungama n’kuchoka kumahemawo anapulumuka.

7 Pa 2 Timoteyo 2:19, Paulo analemba kuti: “Yehova amadziwa anthu ake.” Ndiye monga tanenera, mfundoyi ikuchokera pa Numeri 16:5. Choncho polemba kuti: “Aliyense wotchula dzina la Yehova aleke kuchita zosalungama” mwina ankanenanso za nkhani ya pa Numeri 16:5, 23-27. Pamenepa zikuoneka kuti mfundo zonsezi zikuchokera pa zimene zinachitika nthawi ya Mose. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo ziwirizi? Tikuphunzira kuti Yehova amadziwa zimene zili mumtima mwa munthu. Choncho amadziwa anthu ake okhulupirika koma amafuna kuti iwo asamayandikire anthu osalungama.

‘TIZIKANA MAFUNSO OPUSA NDI OPANDA NZERU’

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kungotchula dzina la Yehova kapena kungokhala mumpingo wachikhristu si kokwanira?

8 Paulo ananena zimene zinachitika  m’nthawi ya Mose pofuna kukumbutsa Timoteyo kuti azichita zinthu molimba mtima poteteza ubwenzi wake ndi Yehova. M’nthawi ya Mose sizinali zokwanira kungotchula dzina la Yehova basi. Chimodzimodzinso m’nthawi ya Paulo. Munthu ankayenera kukana zosalungama molimba mtima osati kungokhala mumpingo basi. Ndiyeno kodi Timoteyo ankafunika kuchita chiyani? Nanga masiku ano anthu a Yehova angaphunzirepo chiyani pa malangizo a Paulowa?

9. Kodi “mafunso opusa ndi opanda nzeru” anakhudza bwanji mpingo m’nthawi ya atumwi?

9 Mawu a Mulungu amapereka malangizo omveka bwino pa nkhani ya zinthu zosalungama zimene Akhristu ayenera kukana. Mwachitsanzo, m’mavesi oyandikana ndi 2 Timoteyo 2:19, Paulo anauza Timoteyo kuti “asamakangane pa mawu” komanso ‘apewe nkhani zopeka.’ (Werengani 2 Timoteyo 2:14, 16, 23.) Anthu ena mumpingo ankalimbikitsa anzawo kukhulupirira zinthu zampatuko. Zikuonekanso kuti anthu ena ankalimbikitsa maganizo omwe ankayambitsa mikangano. Mwina maganizowa sanali otsutsana ndi Malemba koma ankachititsa kuti anthu azikangana pa mawu. Izi zinkasokoneza mgwirizano mumpingo. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Uzikana mafunso opusa ndi opanda nzeru.”

10. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikakumana ndi ampatuko?

10 Masiku ano zampatuko sizichitikachitika mumpingo. Koma tikamva mfundo zotsutsana ndi Malemba kuchokera kwa munthu wina aliyense tiyenera kuzikana kwamtuwagalu. Si nzeru kukambirana ndi ampatuko kaya pamasom’pamaso, pa Intaneti kapena m’njira ina iliyonse. Mwina tingaganize kuti tikhoza kuthandiza anthuwo. Koma tikalankhula nawo ndiye kuti tikunyalanyaza malangizo a m’Baibulo amene takambiranawa. Anthu a Yehovafe tiyenera kupeweratu ampatuko.

Pewani kulankhula ndi anthu ampatuko (Onani ndime 10)

11. (a) N’chiyani chingayambitse mikangano yopanda nzeru? (b) Kodi akulu angakhale bwanji chitsanzo chabwino pa nkhaniyi?

11 Koma pali zinthu zinanso zomwe zingasokoneze mtendere mumpingo. Mwachitsanzo, kusiyana maganizo pa nkhani ya zosangalatsa kungayambitse mikangano yopanda nzeru. Komabe anthu mumpingo akayamba kulimbikitsa ena kuchita zosangalatsa zoipa, akulu sayenera kulekerera zimenezi poopa kukangana ndi anthuwo. (Sal. 11:5; Aef. 5:3-5) Ngakhale zili choncho, akulu ayenera kusamala kuti asayambe kulimbikitsa anthu kuti aziyendera maganizo a akuluwo. Iwo amatsatira mokhulupirika malangizo a m’Malemba akuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu . . . Osati mochita ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”—1 Pet. 5:2, 3; werengani 2 Akorinto 1:24.

12, 13. (a) Kodi gulu la Mboni za Yehova limatsatira mfundo za Malemba ati pa nkhani ya zosangalatsa? (b) Kodi mfundo zimene takambirana m’ndime 12 zimakhudzanso bwanji nkhani zina?

12 Gulu lathu sililemba mndandanda wa mafilimu, masewera apakompyuta, mabuku kapena nyimbo zimene tiyenera kupewa. Izi zili choncho chifukwa chakuti Baibulo limalimbikitsa munthu aliyense kuti aziphunzitsa ‘mphamvu zake za kuzindikira kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheb. 5:14) Malemba amafotokoza mfundo zimene zingathandize Akhristu kusankha bwino pa nkhani ya zosangalatsa. Pa zonse zimene timachita tiyenera ‘kutsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’ (Aef. 5:10) Koma Baibulo limaphunzitsanso kuti mitu ya  mabanja ili ndi ufulu woletsa zosangalatsa zina m’banja lawo. *1 Akor. 11:3; Aef. 6:1-4.

13 Mfundo za m’Baibulo zimene takambiranazi sizikhudza zosangalatsa zokha. Kusiyana maganizo pa nkhani ngati kavalidwe, chakudya kapena mankhwala kungayambitsenso mikangano. Ngati maganizo a munthu sakusemphana ndi mfundo za m’Baibulo tingachite bwino kupewa mikangano pa nkhani ngati zimenezi. Paja Baibulo limati: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.”—2 Tim. 2:24.

TISAMAGWIRIZANE NDI ANTHU OIPA

14. Kodi Paulo analemba fanizo liti polimbikitsa Akhristu kuti azipewa kugwirizana ndi anthu oipa?

14 Kodi ‘anthu otchula dzina la Yehova’ angachitenso chiyani kuti apewe zosalungama? Iwo ayenera kupewa kucheza kwambiri ndi anthu ochita zosalungama. Kodi mwaona fanizo limene Paulo ananena atangotchula za “maziko olimba a Mulungu”? Iye analemba kuti: “M’nyumba yaikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha ayi, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Ziwiya zina zimakhala za ntchito yolemekezeka koma zina zimakhala za ntchito yonyozeka.” (2 Tim. 2:20, 21) Ndiyeno ananena kuti Akhristu ayenera ‘kupewa ziwiya za ntchito yonyozekazo.’

15, 16. Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo lonena za ‘nyumba yaikulu’?

15 Kodi fanizoli likunena za chiyani? Paulo anayerekezera mpingo ndi ‘nyumba yaikulu’ ndipo Mkhristu aliyense ali ngati “chiwiya” cha m’nyumbayo. Kodi inuyo mungatani ngati chiwiya cha m’nyumba mwanu chada kapena chakhudzidwa ndi zinthu zomwe zingakudwalitseni? N’zosachita kufunsa kuti mudzachisiyanitsa ndi ziwiya zina zoyera monga za kukhitchini.

 16 Ndi mmene zililinso ndi anthu a Yehova omwe amayesetsa kukhala oyera. Iwo ayenera kupewa aliyense mumpingo amene amakonda kunyalanyaza mfundo za Yehova. (Werengani 1 Akorinto 15:33.) Ndiye ngati zili choncho ndi anthu amene ali mumpingo kuli bwanji anthu amene sali mumpingo? Ambiri mwa iwo ndi ‘okonda ndalama, osamvera makolo, osakhulupirika, onenera anzawo zoipa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu ndiponso okonda zosangalatsa m’malo mokonda Mulungu’ ndipo tiyenera ‘kuwapewa.’—2 Tim. 3:1-5.

YEHOVA AMATIDALITSA TIKAMACHITA ZINTHU MOLIMBA MTIMA

17. Kodi Aisiraeli okhulupirika anachita chiyani posonyeza kuti amakana zosalungama?

17 Baibulo limafotokoza momveka bwino zimene Aisiraeli anachita atauzidwa kuti: “Chokani kumahema a Kora, Datani ndi Abiramu.” Limanena kuti: “Nthawi yomweyo anthuwo anachoka.” (Num. 16:24, 27) Sanazengereze ngakhale pang’ono. Malemba amanenanso kuti: ‘Anthuwo anachoka kumbali zonse za mahemawo.’ Anthu okhulupirikawo sankafuna kuika moyo wawo pa ngozi. Iwo anamvera ndi mtima wonse. Anasonyezeratu kuti ali kumbali ya Yehova ndiponso kuti amakana zosalungama. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa chitsanzo chawo?

18. Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pouza Timoteyo kuti ‘athawe zilakolako zaunyamata’?

18 Nafenso tiyenera kuchita zinthu mwamsanga ndiponso molimba mtima poteteza ubwenzi wathu ndi Yehova. N’chifukwa chake Paulo anauza Timoteyo kuti: “Thawa zilakolako zaunyamata.” (2 Tim. 2:22) Pa nthawiyo, mwina Timoteyo anali ndi zaka za m’ma 30. Komabe anthu akhoza kukhala ndi “zilakolako zaunyamata” ngakhale atakula. Ndiyeno Timoteyo ankayenera ‘kuthawa’ zinthu zimene zikanamuchititsa kukhala ndi zilakolakozi. Choncho tinganene kuti anayenera kukana zosalungama. Yesu anapereka malangizo ofanananso ndi amenewa ponena kuti: “Ngati diso lako limakupunthwitsa ulikolowole n’kulitaya.” (Mat. 18:9) Masiku anonso, Akhristu ayenera kutsatira malangizo amenewa pochita zinthu molimba mtima komanso mwamsanga akakumana ndi zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova.

19. Kodi anthu ena achita chiyani kuti ateteze ubwenzi wawo ndi Yehova?

19 Anthu ena amene ankalephera kudziletsa pa nkhani ya mowa asanakhale a Mboni asankha kuti asamamwe n’komwe. Ndipo ena amasankha kupeweratu zosangalatsa zina zomwe mwina si zolakwika koma zimene akuona kuti zikhoza kuwachititsa kulakalaka zinthu zoipa. (Sal. 101:3) Mwachitsanzo, m’bale wina asanakhale wa Mboni ankakonda kupita kumadansi ndi anthu amakhalidwe oipa. Iye ataphunzira Baibulo, anayamba kupeweratu kuvina ngakhale pamene ali kocheza ndi abale ndi alongo. Ankatero poopa kuti angayambe kulakalaka zakale zija. N’zoona kuti Akhristu sayenera kupeweratu kumwa mowa, kuvina kapena zosangalatsa zina zimene Baibulo sililetsa. Koma tonsefe tiyenera kuchita zinthu molimba mtima kuti titeteze ubwenzi wathu ndi Yehova.

20. Ngakhale kuti kukana zosalungama si kophweka, kodi n’chiyani chingatilimbikitse?

20 Popeza kuti timadziwika ndi dzina la Mulungu tilinso ndi udindo. Tiyenera kukana zosalungama ndiponso ‘kupatuka pa zinthu zoipa.’ (Sal. 34:14) N’zoona kuti kuchita zimenezi si kophweka. Koma timalimbikitsidwa tikakumbukira kuti Yehova sadzasiya kukonda “anthu ake” omwe amatsatira njira zake zolungama.—2 Tim. 2:19; werengani 2 Mbiri 16:9a.

^ ndime 12 Onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?” Nkhaniyi ikupezeka pa chigawo chakuti ZOKHUDZA IFEYO> MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI.