NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) September 2013

Magaziniyi ikufotokoza zimene tingachite kuti tizisankha zochita mwanzeru, tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu ndiponso mmene zikumbutso za Yehova zingatithandizire.

Kusiyanitsa Zinthu N’kothandiza Kwambiri

Kawirikawiri Yesu ankagwiritsa ntchito mawu osiyanitsa zinthu. Onani mmene mungagwiritsire ntchito mawu amenewa pophunzitsa ena Baibulo.

Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalirika

Yehova wakhala akugwiritsa ntchito zikumbutso kuti azitsogolera anthu ake. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira zikumbutso za Mulungu masiku ano?

Kodi Zikumbutso za Yehova Zimakondweretsa Mtima Wanu?

Kodi timatsatira malamulo a Yehova mosangalala kapena nthawi zina timawaona ngati chimtolo cholemetsa? Kodi tingatani kuti tizikhulupirira zikumbutso zake?

Kodi Mwasandulika?

N’chifukwa chiyani Akhristu onse ayenera ‘kusandulika’? Kodi timafunika kusintha zinthu ziti kuti tisandulike ndipo n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi?

Muzisankha Zochita Mwanzeru

Kodi tingatsimikize bwanji kuti zimene tasankha kuchita n’zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu? N’chiyani chingatithandize kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi zimene tasankha?

Upainiya Umalimbitsa Ubwenzi Wathu ndi Mulungu

Onani zinthu 8 zimene zingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova mukamachita upainiya. N’chiyani chingakuthandizeni kupitiriza utumiki wosangalatsa umenewu?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Malinga ndi Yohane 11:35, n’chifukwa chiyani Yesu anagwetsa misozi asanaukitse Lazaro?