Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Upainiya Umalimbitsa Ubwenzi Wathu ndi Mulungu

Upainiya Umalimbitsa Ubwenzi Wathu ndi Mulungu

“Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.”—SAL. 147:1.

1, 2. (a) Kodi chimachitika n’chiyani tikamaganizira ndiponso kuuza ena za mnzathu? (Onani chithunzi choyamba.) (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani ino?

TIKAMAGANIZIRA ndiponso kuuza anthu ena za mnzathu, timayamba kumukonda kwambiri mnzathuyo. Ndi mmene zililinso ndi ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Pamene Davide anali m’busa nthawi zambiri ankayang’ana nyenyezi usiku n’kumaganizira za Yehova amene anazilenga. Iye analemba kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizira, ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?” (Sal. 8:3, 4) Nayenso Paulo ataganizira zimene Yehova akuchita pokwaniritsa cholinga chake chokhudza Isiraeli wauzimu, anati: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.”—Aroma 11:17-26, 33.

2 Tikamalalikira, timaganizira ndiponso kuuza anthu za Yehova. Kuchita zimenezi kumatithandiza kwambiri. Anthu ambiri amene akuchita upainiya, aona kuti ayamba kukonda kwambiri Mulungu chifukwa chowonjezera nthawi imene amalalikira. Kaya mukuchita upainiya kapena muli ndi cholinga choti muuyambe, mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi upainiya ungalimbitse bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova?’ Ngati ndinu mpainiya, dzifunseni kuti, ‘N’chiyani chingandithandize kupitiriza utumiki wosangalatsawu?’ Ngati simunayambe upainiya dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingasinthe zinthu ziti kuti ndiyambe?’ Tiyeni tione mmene utumikiwu ungalimbitsire ubwenzi wathu ndi Mulungu.

 KODI UPAINIYA UMALIMBITSA BWANJI UBWENZI WATHU NDI MULUNGU?

3. Kodi chimachitika n’chiyani tikamakambirana ndi anthu za madalitso amene Ufumu udzabweretse?

3 Tikamakambirana ndi anthu za madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, timayamba kukonda kwambiri Yehova. Kodi ndi malemba ati amene mumakonda kuwagwiritsa ntchito mukamalalikira? Kodi mumakonda kugwiritsa ntchito Salimo 37:10, 11; Danieli 2:44; Yohane 5:28, 29 kapena Chivumbulutso 21:3, 4? Nthawi iliyonse pamene tikukambirana ndi anthu za malonjezo amenewa, ifenso timakumbutsidwa kuti Mulungu ndi wowolowa manja ndipo amapereka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” Zimenezi zimachititsa kuti tizimukonda kwambiri.—Yak. 1:17.

4. Kodi chimachitika n’chiyani tikaona kuti anthu ambiri ndi osasangalala komanso samvetsa bwino Mawu a Mulungu?

4 Tikamalalikira timaona kuti anthu ndi osasangalala ndipo sadziwa bwino Mawu a Mulungu. Zimenezi zimatithandiza kuyamikira kwambiri zimene taphunzira. Anthu m’dzikoli amasowa malangizo owathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino komanso azikhala osangalala. Ambiri amada nkhawa akaganizira zam’tsogolo ndipo alibe chiyembekezo. Iwo amayesetsa kuti adziwe cholinga cha moyo koma amalephera. Ngakhale anthu amene amapita kutchalitchi sadziwa bwinobwino Malemba. Amafanana ndi anthu a ku Nineve. (Werengani Yona 4:11.) Tikawonjezera nthawi imene timalalikira, timaona bwinobwino kuti anthu ambiri sadziwa Mawu a Mulungu ngati mmene anthu a Yehova amawadziwira. (Yes. 65:13) Timaonanso kuti Yehova ndi wabwino kwambiri. Iye amatiphunzitsa ndiponso amapereka mwayi kwa anthu onse kuti akhale naye pa ubwenzi wabwino komanso akhale ndi chiyembekezo.—Chiv. 22:17.

5. Kodi kuphunzitsa ena kumatithandiza bwanji tikakhala pa mavuto?

5 Tikamaphunzitsa anthu ena Mawu a Mulungu timasiya kuganizira kwambiri mavuto athu. Mpainiya wina dzina lake Trisha anaona umboni wa zimenezi pamene makolo ake anathetsa banja lawo. Iye anati: “Izi zitachitika, ndinasokonezeka kwabasi.” Tsiku lina atakhumudwa kwambiri anaganiza zongokhala kunyumba. Koma kenako anapita kukaphunzira ndi ana atatu amene analinso pa mavuto aakulu. Bambo awo anawasiya ndipo mchimwene wawo ankawazunza kwambiri. Trisha anati: “Mavuto anga anali aang’ono kwambiri ndikawayerekezera ndi mavuto awo. Pamene tinkaphunzira, iwo ankasekerera kwambiri ndipo timaso tawo tinkachita kuonekeratu kuti akusangalala ndi zimene akuphunzira. Kunena zoona, Yehova anagwiritsa ntchito anawa kuti andilimbikitse tsiku limenelo.”

6, 7. (a) Kodi kuphunzitsa ena Baibulo kumalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu? (b) Kodi chimachitika n’chiyani tikaona mmene mfundo za m’Baibulo zikuthandizira anthu pa moyo wawo?

6 Kuphunzitsa ena mfundo za m’Baibulo kumalimbitsa chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo analemba za Ayuda ena amene sankatsatira zimene iwowo ankaphunzitsa. Iye anati: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha?” (Aroma 2:21) Koma si mmene zilili ndi apainiya masiku ano. Iwo amaphunzitsa anthu ambiri Baibulo. Kuti aphunzitse mogwira mtima, amafunika kukonzekera bwino komanso kufufuza mayankho a mafunso. Mpainiya wina dzina lake Janeen anati: “Nthawi iliyonse imene ndimaphunzitsa anthu mfundo za m’Baibulo zimakhazikikanso mumtima mwanga. Izi zimachititsa kuti chikhulupiriro changa chizilimba kwambiri.”

7 Tikamaona mmene mfundo za m’Baibulo zikuthandizira anthu pa moyo wawo, timaona kuti nzeru za Mulungu ndi zapamwamba kwambiri. (Yes. 48:17, 18) Izi zimatilimbikitsa kuti tipitirize kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. Mpainiya wina dzina lake Adrianna anati: “Anthu akamadalira nzeru  zawo, moyo wawo umasokonekera kwambiri. Koma akayamba kudalira nzeru za Yehova, nthawi yomweyo zinthu zimayamba kuwayendera bwino.” Nayenso Phil anati: “Mumaona anthu amene ankalephera kusintha paokha akuthandizidwa ndi Yehova n’kumasintha bwinobwino.”

8. Kodi kulalikira limodzi ndi Akhristu anzathu kumatithandiza bwanji?

8 Kulalikira limodzi ndi Akhristu anzathu kumatilimbikitsa. (Miy. 13:20) Apainiya ambiri amalalikira ndi Akhristu anzawo nthawi ndi nthawi. Izi zimathandiza kuti ‘azilimbikitsana.’ (Aroma 1:12; werengani Miyambo 27:17.) Mpainiya wina dzina lake Lisa anati: “Kuntchito, anthu amakonda kupikisana komanso kuchitirana nsanje. Aliyense amafuna kuti apose anzake. Tsiku lililonse umamva anthu akujeda anzawo kapena kutukwana. Nthawi zina umanyozedwa kapena kusekedwa chifukwa chokhala ndi makhalidwe abwino. Koma ukamalalikira limodzi ndi Akhristu anzako umalimbikitsidwa kwambiri. Ukamaweruka mu utumiki umakhala utatopa koma utalimbikitsidwa kwabasi.”

9. Kodi chimachitika n’chiyani tikamachita upainiya ndi mwamuna kapena mkazi wathu?

9 Kuchita upainiya ndi mwamuna kapena mkazi wathu kumalimbitsa banja komanso ubwenzi wathu ndi Mulungu. (Mlal. 4:12) Madeline amachita upainiya limodzi ndi mwamuna wake ndipo anati: “Ine ndi mwamuna wanga timakonda kukambirana zimene zachitika mu utumiki. Timakambirananso mfundo zimene tawerenga m’Baibulo zomwe zingatithandize mu utumiki. Kuchitira limodzi upainiya kwathandiza kuti tizikondana kwambiri.” Nayenso Trisha anati: “Tonse timayesetsa kupewa ngongole, choncho sitikangana pa nkhani za ndalama. Nthawi imene timalowa mu  utumiki imakhala yofanana. Izi zimathandiza kuti tizipitira limodzi ku maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo. Chifukwa cha zimenezi, timamvetsetsana ndiponso kulimbikitsana.”

Kuchita upainiya kungakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala (Onani ndime 9)

10. Kodi tikaika zinthu za Ufumu patsogolo n’kuona Yehova akutithandiza, timamva bwanji?

10 Tikaika zinthu za Ufumu patsogolo n’kuona kuti Yehova akutithandiza ndiponso kuyankha mapemphero athu, timayamba kumudalira kwambiri. Mfundo imeneyi imagwira ntchito kwa Akhristu onse okhulupirika. Komabe apainiya ayenera kudalira kwambiri Yehova kuti asasiye utumiki wawo. (Werengani Mateyu 6:30-34.) M’bale wina dzina lake Curt amachita upainiya limodzi ndi mkazi wake komanso amatumikira monga woyang’anira dera wogwirizira. Nthawi ina anavomera kukachezera mpingo wakutali moti anafunika kuyenda pa galimoto kwa maola awiri ndi hafu. Koma mafuta amene anali m’galimoto yawo anali ongokwanira kukafika ku mpingowo osati kubwerera. Komanso pa nthawiyo, kunali kutatsala mlungu umodzi kuti alandire malipiro ake. Curt anati: “Ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi bwino kuti tipiteko?’” Koma atapempherera nkhaniyi, anaona kuti akhoza kupita ndipo ankakhulupirira kuti Mulungu awathandiza. Atangotsala pang’ono kunyamuka, mlongo wina anawaimbira foni n’kunena kuti ali ndi kamphatso koti awapatse. Mphatso yake inali ya ndalama zokwanira ndendende mafuta ogwiritsira ntchito pobwerera. Curt anati: “Zinthu ngati zimenezi zikamachitikachitika umaoneratu kuti Yehova akukuthandiza.”

11. Kodi apainiya amapeza madalitso otani?

11 Apainiya ambiri amaona kuti akamachita khama mu utumiki n’kumakonda kwambiri Yehova amapeza madalitso osaneneka. (Deut. 28:2) N’zoona kuti apainiya amakumana ndi mavuto ena. Ndipotu mtumiki wa Yehova aliyense amakumana ndi mavuto obwera chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Apainiya ena amafika posiya kaye utumiki wawo chifukwa cha mavuto. Komabe mavuto ena amakhala oti tikhoza kulimbana nawo mwinanso kuwapewa. Kodi n’chiyani chingathandize apainiya kuti asasiye utumiki wawo?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUTI MUSASIYE UPAINIYA

12, 13. (a) Kodi mpainiya ayenera kuchita chiyani ngati zikumuvuta kukwaniritsa maola ofunika? (b) N’chifukwa chiyani mpainiya ayenera kupeza nthawi yowerenga Baibulo, kuphunzira ndiponso kuganizira mozama zimene waphunzirazo?

12 Apainiya amatanganidwa kwambiri moti akhoza kuvutika kuti achite zinthu zonse zofunika. Choncho ayenera kuchita zinthu mwadongosolo kwambiri. (1 Akor. 14:33, 40) Ngati mpainiya akuvutika kukwaniritsa maola ofunika, angachite bwino kuonanso mmene akugwiritsira ntchito nthawi yake. (Aef. 5:15, 16) Angadzifunse kuti: ‘Kodi ndimathera nthawi yochuluka bwanji pa zosangalatsa? Kodi ndikufunika kudziletsa pa nkhani imeneyi? Kodi ndikhoza kuchepetsa nthawi imene ndimagwira ntchito?’ Mkhristu aliyense angavomereze kuti n’zosavuta kuwonjezera zochita pa nthawi yochepa imene ali nayo. Choncho nthawi ndi nthawi apainiya angafunike kuona mmene zinthu zilili pa moyo wawo n’kusintha ngati pakufunika kutero.

13 Mpainiya ayenera kupezanso nthawi yowerenga Baibulo, kuphunzira ndiponso kuganizira mozama zimene waphunzirazo. Choncho ayenera kudziletsa kuti apewe kuchita zinthu zimene zingamuwonongere nthawi yochitira zinthu zofunika. (Afil. 1:10) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mpainiya wafika panyumba atakhala mu utumiki tsiku lonse. Ndiyeno madzulowo ali ndi cholinga chokonzekera misonkhano. Koma choyamba akupita kukacheza kwa mnzake. Atabwerako akuyatsa TV kuti aonere nkhani. Nkhanizo zitatha, pulogalamu ina imene amaikonda ikuyamba ndipo akutengeka  nayo. Kenako akuzindikira kuti patha maola awiri koma sanayambe kukonzekera misonkhano ija. Zimenezitu zingakhale zoopsa. Akatswiri othamanga ayenera kusamalira matupi awo ngati akufuna kupitiriza kuthamanga. Nawonso apainiya ayenera kumapeza nthawi yophunzira paokha kuti apeze mphamvu zopitirizira utumiki wawo.—1 Tim. 4:16.

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani apainiya ayenera kukhala moyo wosalira zambiri? (b) Kodi mpainiya ayenera kutani akakumana ndi mavuto?

14 Kuti munthu apitirize upainiya, amafunika kukhala moyo wosalira zambiri. Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti akhale ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi. (Mat. 6:22) Nayenso ankakhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti asamadodometsedwe pa utumiki wake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.” (Mat. 8:20) Mpainiya amene akufuna kutsanzira Yesu ayenera kukumbukira kuti katundu akachuluka pamakhalanso ntchito yaikulu yosamalira ndiponso kukonzetsa zinthuzo.

15 Apainiya amadziwa kuti iwo si anthu apadera. Paja utumiki uliwonse umene tingakhale nawo m’gulu la Yehova timalandira chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu. Choncho kuti mpainiya apitirize utumikiwu, ayenera kudalira Yehova. (Afil. 4:13) N’zoona kuti apainiya amakumana ndi mavuto. (Sal. 34:19) Zikatero, ayenera kupemphera kwa Yehova kuti awatsogolere m’malo mofulumira kuganiza zongosiya utumikiwo. (Werengani Salimo 37:5.) Akamaona kuti Mulungu akuwathandiza mwachikondi, adzayamba kumukonda kwambiri monga Atate wawo wakumwamba.—Yes. 41:10.

KODI INUNSO MUNGAYAMBE UPAINIYA?

16. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kuyamba upainiya?

16 Ngati inunso mukufuna kupeza madalitso amene apainiya amalandira, muuzeni Yehova zimenezi m’pemphero. (1 Yoh. 5:14, 15) Muzikambirana ndi anthu amene panopa akuchita upainiya. Komanso muyenera kukhala ndi zolinga zimene zingakuthandizeni kuyamba utumiki umenewu. M’bale wina dzina lake Keith ndi mkazi wake Erika anachita zimenezi. Onse awiri anali pa ntchito ndipo atangokwatirana anagula nyumba ndi galimoto yatsopano. Iwo anati: “Tinkaganiza kuti zinthuzo zitithandiza kukhala osangalala. Koma si mmene zinalili.” Keith atauzidwa kuti aime kaye ntchito, anayamba upainiya wothandiza. Iye anati: “Upainiya unandikumbutsa kuti utumiki ndi wosangalatsa kwambiri.” M’bale ndi mlongoyu anayamba kucheza ndi banja lina lomwe linkachita upainiya. Banjali linawathandiza kuzindikira ubwino wochita utumikiwu ndiponso wokhala moyo wosalira zambiri. Kodi Keith ndi Erika anachita chiyani? Iwo anati: “Tinalemba zolinga zathu n’kumata pafiriji. Kenako tinkachonga cholinga chilichonse chimene tachikwaniritsa.” Patapita nthawi, iwo anayambadi upainiya.

17. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuti muganizire zosintha zinthu pa moyo wanu kuti muchite upainiya?

17 Kodi inunso mungayambe upainiya? Ngati panopa mukuona kuti simungakwanitse zimenezi, yesetsani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova pochita zonse zimene mungathe mu utumiki. Koma mwina mutapempherera nkhaniyi ndi kuiganizira, mungaone kuti mukhoza kuchita upainiya mutasintha zinthu zina pa moyo wanu. Ngati mutayamba utumikiwu, muona kuti mudzapeza madalitso ambiri kuposa zinthu zonse zimene munazisiya kuti muuyambe. Mudzakhala osangalala kwambiri chifukwa choika patsogolo Ufumu m’malo mwa zofuna zanu. (Mat. 6:33) Mudzakhalanso osangalala chifukwa chothandiza anthu ena. Komanso mudzakhala ndi nthawi yochuluka yoganizira ndiponso kuuza ena za Yehova. Zimenezi zidzakuthandizani kumukonda kwambiri ndipo mudzamusangalatsa.