Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Olimbikitsa a “Ana Aang’ono”

Mawu Olimbikitsa a “Ana Aang’ono”

Mu December 2009, Khoti Lalikulu la ku Russia linavomereza chigamulo cha khoti lina choti Mboni za Yehova zisakhalenso bungwe lovomerezeka ndi boma mumzinda wa Taganrog. Linavomerezanso kuti Nyumba ya Ufumu ilandidwe ndipo zinthu zokwana 34 monga mabuku, magazini ndiponso timapepala zisamafalitsidwe chifukwa si zabwino kwa anthu. Lipoti la nkhaniyi linaikidwa pa Webusaiti ya Mboni za Yehova limodzi ndi zithunzi za abale, alongo ndiponso ana a ku Taganrog amene anakhudzidwa ndi nkhaniyi.

Patangopita miyezi yochepa, nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko la Russia, inalandira bokosi lokhala ndi kalata komanso mphatso. Bokosili linachokera ku banja lina la Mboni ku Queensland, m’dziko la Australia. Banjali linaona lipotili pa Intaneti ndipo linalemba kuti: “Okondedwa abale, Ana athu Cody ndi Larissa anakhudzidwa kwambiri atamva za mayesero a abale athu ku Russia ndiponso za chikhulupiriro chawo. Anawa alemba timakadi ndiponso makalata. Tatumiza zimenezi limodzi ndi timphatso kuti mupereke kwa ana a ku Taganrog. Tikufuna kuti anawo adziwe kuti m’mayiko ena mulinso ana amene akutumikira Yehova mokhulupirika omwe amawaganizira. Ana athuwa akuperekanso moni ndipo akuwafunira anzawowo zabwino zonse.”

Ana a ku Taganrog atalandira zinthuzi, analemba makalata komanso kujambula zithunzi pothokoza banja la ku Australia. M’bale wina wa ku Beteli ya ku Russia ataona zimene anawa anachita, analembera kalata Cody ndi Larissa. M’kalatayo analemba kuti: “Mukudziwa kuti ana ndi akulu omwe amavutika maganizo akamalangidwa popanda chifukwa. Abale ndi alongo athu ku Taganrog sanalakwe chilichonse koma alandidwa Nyumba ya Ufumu. Panopa ndi okhumudwa kwambiri. Adzasangalala kudziwa kuti anthu akutali amawaganizira. Tikuthokoza kwambiri pa zabwino zimene mwachitazi.”—Sal. 8:2.

Akhristufe tili pa ubale wapadziko lonse ndipo kukondana kwathu kumathandiza kuti tipirire mayesero ndi mavuto amene timakumana nawo. Mboni za Yehova zaimbidwa mlandu woti zimadanitsa anthu koma chikondi chimene ana athuwa asonyeza, chaonetseratu kuti timakondana ndiponso kuganizirana. Kusiyana mitundu ndi mayiko sikutilepheretsa kuchita zimenezi. Mawu a Yesu ndi oonadi. Iye anati: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:35.