Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mbiri ya Moyo Wanga

Ubwenzi wa Zaka 60, Koma Akuti N’chiyambi Chabe

Ubwenzi wa Zaka 60, Koma Akuti N’chiyambi Chabe

Tsiku lina madzulo m’chaka cha 1951, achinyamata anayi a zaka za m’ma 20 anapita pamalo oimbira foni ku Ithaca ku New York, m’dziko la United States. Iwo ankaimbira mafoni ku Michigan, ku Iowa ndi ku California. Onse anali ndi uthenga wosangalatsa kwambiri.

IZI zisanachitike, apainiya okwana 122 anasonkhana ku South Lansing ku New York kuti alowe kalasi ya nambala 17 ya Sukulu ya Giliyadi. Umenewu unali mwezi wa February. M’gululi munali Lowell Turner, William (Bill) Kasten, Richard Kelsey ndi Ramon Templeton. Lowell ndi Bill anachokera ku Michigan, Richard anachokera ku Iowa ndipo Ramon anachokera ku California. Abalewa anayamba kugwirizana kwambiri.

Patatha miyezi 5, ophunzira anasangalala kwambiri atamva kuti M’bale Nathan Knorr wochokera kulikulu la dziko lonse akubwera kudzalankhula nawo. Pa nthawiyi, ophunzira ankayembekezera kuuzidwa mayiko amene azikatumikira. Abale anayi tawatchulawa ankafunitsitsa atatumizidwa kudziko limodzi.

Aliyense anatchera khutu pamene M’bale Knorr anayamba kutchula mayiko amene ophunzirawo azikatumikira. Oyamba kutchulidwa anali abale anayiwa. Iwo anasangalala kwabasi kumva kuti onse azikatumikira ku Germany. Ophunzira onse atamva, anadabwa kwambiri ndipo anaomba m’manja kwa nthawi yaitali.

Abale ndi alongo padziko lonse ankadabwa kwambiri akamva za kukhulupirika kwa Mboni za Yehova ku Germany. Kuyambira mu 1933, Mboni za Yehova zinazunzidwa kwambiri mu ulamuliro wa Hitler. Ophunzira ambiri m’kalasiyi ankakumbukira nthawi imene ankatumiza zovala ndi zinthu zina pofuna kuthandiza abale a ku Ulaya pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Kunena zoona, anthu a Mulungu ku Germany anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ankadalira Yehova, anali olimba mtima ndipo sanabwerere m’mbuyo. Lowell atamva zimenezi, ankadziuza mumtima kuti, ‘Eyaa, tsopano tikaonana ndi abale ndi alongo athu okondedwa ku Germany.’ M’pake kuti madzulo a tsiku limeneli, aliyese anaimba foni yodziwitsa achibale ake zoti akupita ku Germany.

ULENDO WA KU GERMANY

Pa July 27, 1951, anauyamba ulendo wopita ku Germany. Iwo anakwera sitima yapamadzi ku New York, mumtsinje wa East River. Ulendo wake unali wa masiku 11. M’bale Albert Schroeder, yemwe anali mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi ndipo anadzakhala  m’Bungwe Lolamulira, anawaphunzitsa ziganizo zingapo za Chijeremani. Musitimayo munali anthu ambiri a ku Germany, moti abalewa ankaganiza kuti apeza mwayi wophunzira mawu ena a chilankhulochi. Koma vuto linali lakuti kalankhulidwe ka anthuwo kankakhala kosiyanasiyana moti zinkangowasokoneza.

Pa ulendowu, abalewa anadwala chifukwa choyenda nthawi yaitali pamadzi. Koma kenako Lachiwiri m’mawa pa August 7, anafika ku Hamburg m’dziko la Germany. Paliponse pamene ankayenda ankaona mmene nkhondo inawonongera zinthu. Pa nthawiyi n’kuti patatha zaka 6 kuchokera pamene nkhondoyi inatha. Iwo anamva chisoni kwambiri. Kenako anakwera sitima yapamtunda yopita ku Wiesbaden, kumene kunali ofesi ya nthambi.

Lachitatu m’mawa anakumana ndi Hans. Iye anali Mboni yoyamba kukumana nayo ku Germany ndipo dzina lakeli linali lofala kwambiri kumeneko. Iye anawatenga pa galimoto kuchoka kusiteshoni ya sitima kupita ku Beteli. Atafika ku Beteli, anawasiya m’manja mwa mlongo wina wachikulire amene sankadziwa Chingelezi ngakhale pang’ono. Poona kuti alendowo sakumva Chijeremani, iye anayamba kuwalankhula mokweza kwambiri kuti mwina angamve. Koma izi sizinaphule kanthu ndipo zinangowaumitsa pakamwa. Mwamwayi, panatulukira M’bale Erich Frost, yemwe anali mtumiki wa nthambi. Iye anawalandira bwino n’kuwapatsa moni m’Chingelezi. Apa zinthu zinayamba kuyenda.

Chakumapeto kwa August, abalewa anapita ku msonkhano woyamba wachijeremani wa mutu wakuti “Kulambira Koyera.” Msonkhanowu unachitikira kumzinda wa Frankfurt am Main. Panasonkhana anthu 47,432 ndipo anthu 2,373 anabatizidwa. Zimenezi zinalimbikitsa kwambiri abale anayiwa kulalikira mwakhama monga amishonale. Koma patangopita masiku ochepa, M’bale Knorr anawauza kuti azitumikira pa Beteli pomwepo.

Anayamba kusangalala ndi utumiki moti anazindikira kuti Yehova amadziwa zinthu kuposa anthufe

Ramon ankafunitsitsa kukhala mmishonale moti m’mbuyomo anali atakana kupita ku Beteli ya ku United States. Nayenso Richard ndi Bill sankaganiza zotumikira ku Beteli. Koma anayamba kusangalala kwambiri ndi utumiki wa pa Beteli moti anazindikira  kuti Yehova amadziwa bwino zinthu kuposa anthufe. Kunena zoona, ndi bwino kutsatira malangizo ake osati zofuna za mtima wathu. Munthu akamatero, amasangalala ndi utumiki uliwonse kwina kulikonse.

N’ZOSALOLEKA!

Abale ndi alongo ambiri ku Beteli ya ku Germany anasangalala kutumikira ndi abale ochokera ku America. Anaona kuti tsopano ali ndi mwayi wophunzira Chingelezi. Koma tsiku lina ali m’chipinda chodyera anazindikira kuti mwayi umenewu palibe. M’bale Frost, amene ankakonda kufotokoza zinthu mwamphamvu, anangoyamba kulankhula nkhani ina yofunika kwambiri m’Chijeremani. Chipinda chonse chinangoti zii. Abale achilendowo sanatolepo kanthu koma anazindikira kuti nkhaniyo ndi yonena za iwowo. Ndiyeno M’bale Frost ananena mokweza kuti “N’ZOSALOLEKA!” Kenako anabwerezanso mawuwa mokuwa kwambiri. Abale anayiwo anadabwa n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi talakwa chiyani?’

Atatha kudya aliyense anangoti wewerere kuchipinda chake. Ndiyeno m’bale wina anawauza kuti: “Anthunu mungatithandize kokha ngati muzilankhula Chijeremani. N’chifukwa chake M’bale Frost uja ananena kuti N’ZOSALOLEKA kulankhula nanu Chingelezi mpaka mutaphunzira Chijeremani.”

Banja lonse la Beteli linamvera malangizowa. Izi zinathandiza alendowo kuphunzira Chijeremani. Zinasonyezanso kuti malangizo amene abale athu achikondi amapereka angaoneke ovuta kwambiri poyamba koma kawirikawiri amakhala othandiza. M’bale Frost anasonyeza kuti ankaganizira kwambiri zinthu zimene zingathandize gulu la Yehova komanso ankakonda abale. * Pamapeto pake, abale anayiwo anayamba kumukonda kwambiri.

TINAPHUNZIRA ZAMBIRI KWA ANZATHU

Chitsanzo cha anzathu oopa Mulungu chingatithandize kukhala mabwenzi a Yehova. Abale anayiwa anaphunzira zambiri kwa abale ndi alongo okhulupirika a ku Germany. Aliyense wa anayiwa ankaphunziranso zinthu kwa mnzake. Richard anati: “Lowell ankadziwa ndithu Chijeremani ndipo ankalankhula bwino koma enafe sitinkachitha kwenikweni. Iye analinso wamkulu pakati pathu moti tinkadalira iyeyo kutsogolera zinthu komanso kutithandiza tikamavutika ndi Chijeremani.” Ramon anati: “Ndinasangalala kwambiri m’bale wina wa ku Switzerland atatiuza kuti patchuthi tipite kwawo  ndipo tizikakhala m’nyumba yake yokongola. Apa n’kuti titatumikira kwa chaka chathunthu. Tinatengadi tchuthi cha milungu iwiri ndipo ndinkaona kuti tipuma pa vuto lathu lolephera Chijeremani. Koma ndinaiwala kuti tili ndi Lowell. Iye ankatiumiriza kuti tizichita lemba la tsiku m’Chijeremani. Zinkandibowa kwabasi koma Lowell sanasinthe maganizo. Apanso ndinaphunzira kanthu kena. Ndi bwino kumvera anthu amene amatifunira zabwino ngakhale pamene sitikugwirizana ndi zimene akutiuzazo. Mfundo imeneyi yatithandiza kwabasi kwa zaka zambiri. Takwanitsa kutsatira malangizo a m’gulu la Mulungu popanda kuvutika kwambiri.”

Abale anayiwa aphunziranso kuyamikira mbali zimene mnzawo aliyense amachita bwino. Paja lemba la Afilipi 2:3 limati: ‘Modzichepetsa, tiziona ena kukhala otiposa.’ Atatuwo ankalemekeza Bill pomuuza kuti azichita zinthu zimene iwowo akuona kuti ndi iye yekha amene angazichite bwino. Lowell anati: “Zinthu zikafika pa mwana wakana phala, tinkadalira Bill. Nthawi zina atatufe tinkalephera kuchita zinthu zina zoyenera chifukwa cha mantha. Koma Bill anali ndi luso linalake moti zinthu ngati zimenezo sinalinso nkhani.”

MABANJA ACHIMWEMWE

Ndiyeno mmodzimmodzi anayamba kukwatira. Abalewa ankagwirizana chifukwa chokonda kwambiri Yehova komanso utumiki wa nthawi zonse. Chifukwa cha zimenezi, iwo ankafunitsitsa kuti akwatire akazi amene amaika Yehova patsogolo. Utumiki wa nthawi zonse unawathandiza kudziwa kuti kupatsa n’kumene kumabweretsa chimwemwe kuposa kulandira. Anadziwanso kuti zinthu zokhudza Ufumu ziyenera kukhala pa malo oyamba osati zolakalaka zawo. Choncho, iwo ankafufuza alongo amene anali atayamba kale utumiki wa nthawi zonse mwa kufuna kwawo. Aliyense anapeza wakewake ndipo anali mabanja achimwemwe kwambiri.

Kuti ubwenzi kapena ukwati ukhale wolimba, anthu onse ayenera kukonda Yehova. (Mlal. 4:12) Mkazi wa Bill ndi wa Ramon anamwalira. Koma pa nthawi imene anali moyo, akazi awiriwa anali okhulupirika ndipo ankathandiza kwambiri abalewa. Lowell ndi Richard adakali ndi akazi awo ndipo akusangalala nawo. Bill anakwatira mkazi wina. Iye anasankhanso bwino moti pano adakali mu utumiki wa nthawi zonse.

Patapita nthawi, abalewa ankapatsidwa mautumiki ena amene ankachititsa kuti asiyane. Ena ankapita m’madera ena a m’dziko la Germany, ku Austria, ku Luxembourg, ku Canada ndiponso ku United States. Chifukwa cha zimenezi, ankacheza mwa apo ndi apo. Ngakhale kuti ankasiyana, iwo ankalankhulanabe. Zinthu zikamayenda bwino, amasangalala limodzi ndipo zikavuta amaliranso limodzi. (Aroma 12:15) Ngati tili ndi mabwenzi oterewa tiziyamikira kwambiri. Tingati ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. (Miy. 17:17) Masiku ano, mabwenzi oterewa ndi osowa kwambiri. Koma Mkhristu woona aliyense akhoza kukhala ndi mabwenzi oterewa ambirimbiri. Tikutero chifukwa tili pa ubale wapadziko lonse ndipo koposa zonse, tili pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu.

 Tonsefe timakumana ndi mavuto pa moyo wathu. Ndi mmene zililinso ndi abalewa. Ena akazi awo anamwalira, ena akhala akudwala ndipo ena ankasamalira makolo awo okalamba. Ena anadzakhala ndi ana n’kumayesetsa kuwasamalira uku akuchita utumiki wa nthawi zonse. Ena ankakayikira ngati angakwanitse utumiki wina umene anapatsidwa ndipo panopa akuvutika ndi ukalamba. Chinthu china chimene aphunzira n’chakuti anthufe timafuna anzathu kuti tilimbane ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo. Anzathu ena timakhala nawo pafupi ndipo ena ali kutali.

UBWENZI WATHU UDZAPITIRIRA MPAKA MUYAYA

N’zosangalatsa kuti abalewa anadzipereka kwa Yehova ali achinyamata. Lowell anabatizidwa ali ndi zaka 18, Ramon ali ndi zaka 12, Bill ali ndi zaka 11 ndipo Richard ali ndi zaka 10. Onsewa anayamba utumiki wa nthawi zonse ali ndi zaka za pakati pa 17 ndi 21. Tingati anatsatiradi lemba la Mlaliki 12:1 lomwe limati: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”

Ngati ndinu m’bale wachinyamata, Yehova angasangalale mutayamba utumiki wa nthawi zonse. Ngati mungakwanitse, yambani utumikiwu ndipo iye adzakudalitsani komanso mudzasangalala kwambiri ngati mmene achitira abale anayiwa. Mwina mudzakhala oyang’anira madera, oyang’anira zigawo, oyendera nthambi, otumikira pa Beteli, a m’Komiti ya Nthambi, alangizi a Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kapena Sukulu ya Utumiki Waupainiya ndipo mwina mungapatsidwe nkhani pa misonkhano yachigawo. Abale anayiwa amasangalala kwambiri kudziwa kuti athandiza anthu ambirimbiri pa utumiki wawo. Izi zatheka chifukwa chakuti anadzipereka kwa Yehova adakali achinyamata kuti am’tumikire ndi moyo wawo wonse.—Akol. 3:23.

Panopa, Lowell, Richard ndi Ramon akutumikiranso limodzi ku ofesi ya nthambi ku Selters, m’dziko la Germany. Koma n’zomvetsa chisoni kuti Bill anamwalira m’chaka cha 2010 ndipo pa nthawiyi anali akuchita upainiya wapadera ku United States. Imfa yasokoneza ubwenzi wa anthu anayiwa womwe wakhalapo kwa zaka pafupifupi 60. Ubwino wake ndi wakuti Mulungu wathu Yehova saiwala anzake. Tikudziwa kuti m’dziko latsopano, ubwenzi uliwonse wa Akhristu umene wasokonezeka chifukwa cha imfa udzayambiranso.

“Takhala mabwenzi kwa zaka 60 ndipo zinthu zinkayenda bwino kwambiri”

Bill atatsala pang’ono kumwalira, analemba kuti: “Takhala mabwenzi kwa zaka 60 ndipo zinthu zinkayenda bwino kwambiri. Nthawi zonse ndinkaona kuti ubwenzi wathu ndi wamtengo wapatali kwambiri.” Anzake atatuwa akuyembekeza kuti ubwenzi wawo ndi Bill udzapitirira m’dziko latsopano. Iwo anati, “Chimenechi n’chiyambi chabe cha ubwenzi wathu.”

^ ndime 17 Mbiri ya moyo wa M’bale Frost ili mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 15, 1961, tsamba 244 mpaka 249.