Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikondwerero cha Chikunja Chingakhale cha Chikhristu?

Kodi Chikondwerero cha Chikunja Chingakhale cha Chikhristu?

 Kodi Chikondwerero cha Chikunja Chingakhale cha Chikhristu?

M’CHAKA cha 2004 panyengo ya Khirisimasi ku Italy, panali kusiyana maganizo. Aphunzitsi ena ankanena kuti m’pofunika kuchepetsa kapena kuthetseratu miyambo ya pa Khirisimasi. Iwo ankanena zimenezi chifukwa cholemekeza ana a sukulu ambiri amene si Akatolika kapenanso amene si a matchalitchi ena achikhristu. Komabe, aphunzitsi ena ndiponso anthu ena ogwira ntchito zina anati miyambo ya pa Khirisimasi iyenera kupitirira ndiponso kulemekezedwa.

Komabe, tiyeni tiganizire kaye funso ili: Kodi miyambo yambiri ya pa Khirisimasi inayamba bwanji? Kusiyana maganizoku kutafika pachimake, nyuzipepala ina yachikatolika ya ku Vatican (yotchedwa L’Osservatore Romano) inanena mfundo ina yosangalatsa pankhaniyi.

Ponena za tsiku lokondwerera Khirisimasi, nyuzipepalayi inati: “Tsiku lenileni limene Yesu anabadwa silikudziwika, chifukwa tikafufuza m’mbiri yonse ya dziko la Roma ndi m’kalembera amene ankachitika mu nthawi imeneyi ndiponso m’mabuku a m’zaka zotsatira, sasonyeza tsiku lenileni limene iye anabadwa. . . . M’zaka za m’ma 300 C.E., Tchalitchi cha Roma ndicho chinasankha tsiku la 25 December, lomwe ndi lodziwika bwino kwambiri. Panthawiyi  Aroma ankalambira milungu yambirimbiri ndipo tsikuli linali lokumbukira mulungu wa Dzuwa . . . Ngakhale kuti Constantine anali atakhazikitsa Chikhristu mwalamulo ku Roma, nkhani . . . ya mulungu wa Dzuwa inali yotchukabe, makamaka pakati pa asilikali. Miyambo ya pachikondwerero chimenechi yomwe inkachitika pa 25 December, inachokera ku miyambo ina yachikunja yotchuka kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti Tchalitchi cha Roma chisinthe tsikuli n’kukhala lachikhristu. Anachita zimenezi mwa kusintha mwambo wolambira mulungu wa Dzuwa womwe unkachitika pa tsikuli n’kukhala wokumbukira kubadwa kwa Dzuwa Lachilungamo lomwe ndi Yesu Khristu.”

Nanga kodi mtengo wa pa Khirisimasi umene Akatolika amaugwiritsa ntchito masiku ano pamwambowu unayamba bwanji?

Nkhani ya m’nyuzipepala ija inanena kuti kalekale anthu “ankakhulupirira kuti mitengo imene imakhala yobiriwira nthawi zonse monga paini ili ndi mphamvu zinazake zapadera zomwe zingateteze munthu kumatenda.” Nkhaniyi inapitiriza kuti: “Pa 24 December, anthu ankakumbukira Adamu ndi Hava pamwambo womwe panali kukambidwa nthano yodziwika kwambiri ya Mtengo wa m’Paradaiso wa padziko lapansi . . . Mtengowo umayenera kukhala wa ma apulo, koma popeza panyengo imeneyi mitengo ya ma apulo sikhala ndi masamba obiriwira, amagwiritsa ntchito mtengo wa paini n’kukolowekakoloweka ma apulo m’nthambi zake. Ndiyeno poyerekezera mwambo wosonyeza kuomboledwa ku machimo, amatenga timakeke timene timaimira ukalisitiya womwe ndi chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. Komanso pamakhala masiwiti ndi mphatso zina zimene amapereka kwa ana.” Nangano chinkachitika n’chiyani mwambowu ukatha?

Potchula kuti mwambo wogwiritsa ntchito mtengo wa pa Khirisimasi unayambira ku Germany m’zaka za m’ma 1500, nyuzipepala ija inatinso: “Dziko la Italy ndi limodzi mwa mayiko amene anali omaliza kuvomereza kugwiritsa ntchito mtengo wa pa Khirisimasi mwina chifukwa cha mphekesera yakuti mwambowu unachokera ku matchalitchi amene anagalukira Chikatolika. Motero ankaona kuti ndi bwino kukonza chithunzi choyerekezera malo amene Yesu anabadwira.” N’chifukwa chake Papa Paulo wachisikisi “anayambitsa mwambo [ku tchalitchi cha St. Peter ku Roma] wokhala ndi mtengo waukulu kwambiri wa pa Khirisimasi” pafupi ndi chithunzi choyerekezera malo amene Yesu anabadwira.

Kodi mukuganiza kuti ndi zomveka kuti mtsogoleri wa chipembedzo asinthe miyambo yakale yachikunja n’kukhala yachikhristu? N’chifukwa chaketu Malemba amalangiza Akhristu oona zoyenera kuchita kuti: “Pali ubale wanji pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? Kapena pali kuyanjana kwanji pakati pa kuwala ndi mdima?”​—2 Akorinto 6:14-17.

[Zithunzi patsamba 8, 9]

Mtengo wa pa Khirisimasi (kumanzereko) ndi chithunzi cha ku Vatican choyerekezera malo amene Yesu anabadwira

[Mawu a Chithunzi]

© 2003 BiblePlaces.com

[Chithunzi patsamba 9]

Uyu ndi mulungu wa dzuwa

[Mawu a Chithunzi]

Museum Wiesbaden