Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziwa Tanthauzo la Zizindikiro N’kofunika Kwambiri

Kudziwa Tanthauzo la Zizindikiro N’kofunika Kwambiri

Kudziwa Tanthauzo la Zizindikiro N’kofunika Kwambiri

“Poyamba ndinkaganiza kuti Andreas, mwana wathu ankangomva mutu kupweteka. Koma analinso kulephera kudya ndipo thupi limatentha kwambiri. Mutu unapitirizabe kupweteka kwambiri ndipo ndinada nkhawa. Mwamuna wanga atabwera ku nyumba, tinapita naye kwa dokotala. Adokotala atam’pima ndi kuona zizindikirozo, nthawi yomweyo anam’tumiza ku chipatala. Vutoli linali lalikulu kwambiri. Sunali mutu chabe. Andreas anali ndi matenda oumitsa khosi. Anam’patsa mankhwala ndipo posapita nthawi anakhala bwino.”​—Anatero Getrude, mayi wa ku Germany.

ZIMENE zinachitikira Getrude mwina makolo ambiri akuzidziwa. Iwo amaona zizindikiro zosonyeza kuti mwana wawo angakhale akudwala. Ngakhale kuti si matenda onse amene amakhala aakulu, makolo sangangosiya osachitapo kanthu akaona zizindikiro zosonyeza kuti mwana wawo akudwala. Kuona zizindikiro ndi kuchitapo kanthu kungakhale kothandiza kwambiri. Ndipo n’kofunika kwambiri.

Kuona zizindikiro n’kofunikanso pankhani zina kuwonjezera pa za thanzi. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi tsoka la tsunami limene linachitikira madera a kunyanja ya mchere ya Indian Ocean mu December 2004. Mabungwe a boma m’mayiko a Australia ndi Hawaii anadziwa kuti kumpoto kwa Sumatra kwachitika chivomezi. Ndipo anadziwa ngozi yaikulu yomwe idzakhalapo chifukwa cha chivomezicho. Koma panalibe njira yochenjezera anthu okhala m’madera angoziwo kapena njira imene anthuwo akanachitira pambuyo poti achenjezedwa. Chifukwa cha zimenezi, anthu oposa 220,000 anafa.

Zizindikiro Zofunika Koposa

Nthawi imene Yesu Kristu anali padziko lapansi, anaphunzitsa omvera ake kufunika koona zizindikiro ndi kuchitapo kanthu. Iye anali kunena za chinthu chofunika koposa. Baibulo limati: “Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, nam’funsa iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba. Koma iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwe; popeza thambo lili lacheza. Ndipo m’mawa, Lero n’kwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino, simungathe kuzindikira.”​—Mateyu 16:1-3.

Potchula “zizindikiro za nyengo,” Yesu anasonyeza kuti Ayuda omwe anali kumvetsera panthawiyo anayenera kudziwa kufunika kwa nthawi imene anali kukhala. Dongosolo la zinthu lachiyuda linali pafupi kukumana ndi tsoka lokhudza iwo onse. Kutatsala masiku ochepa imfa yake isanachitike, Yesu analankhula ndi ophunzira ake za chizindikiro china. Ichi chinali chizindikiro cha kukhalapo kwake. Zimene ananena panthawiyo n’zofunika kwambiri kwa munthu aliyense masiku ano.