Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anandidalitsa ndi Choloŵa Chapadera

Anandidalitsa ndi Choloŵa Chapadera

Mbiri ya Moyo Wanga

Anandidalitsa ndi Choloŵa Chapadera

YOSIMBIDWA NDI CAROL ALLEN

Ndinali ndekha, nditagwira buku langa labwino latsopano. Mantha anandigwira, ndipo ndinagwetsa misozi. Ndi iko komwe, ndinali kamtsikana kakang’ono ka zaka zisanu ndi ziŵiri zokha basi nditasokera pakati pa anthu zikwizikwi mumzinda wosaudziŵa!

POSACHEDWAPA, zaka pafupifupi 60 zitatha, ndinakumbukira bwino lomwe zochitika za ubwana wanga zimenezo, pamene tinakacheza kumalo okongola a Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, New York ndi mwamuna wanga, Paul. Anamuitana kumeneko kukakhala nawo m’kalasi yachiŵiri ya sukulu ya oyang’anira oyendayenda a Mboni za Yehova.

Pamene tinali kuyang’ana malo owala olandirirako alendo, ndinaona malo oonetsera zinthu olembedwa kuti “MISONKHANO YACHIGAWO.” Chapakati pake panali chithunzi chakale cha mtundu wakuda ndi woyera cha ana amene mokondwera ananyamula makope awo m’mwamba a buku la ubwana wanga! Ndinafulumira kuŵerenga mawu ofotokoza chithunzicho akuti: “1941​—Ku St. Louis, Missouri, pamene chigawo cha m’maŵa chinayamba, ana 15,000​—a zaka zoyambira 5 mpaka 18​—anasonkhana m’bwalo kutsogolo kwenikweni kwa pulatifomu. . . . Mbale Rutherford analengeza kutulutsidwa kwa buku latsopano la mutu wakuti Children (Ana).”

Mwana aliyense anam’patsa buku lake. Kenaka anawo anabwerera kumene makolo awo anakhala​—onse kungotsala ineyo. Ndinali nditasokera! Kalinde waubwenzi anandinyamula nandiimiriritsa pa bokosi la zopereka lalitali n’kundiuza kuti ndiyang’ane wina amene ndinali kum’dziŵa. Ndili ndi nkhaŵa, ndinayang’anitsitsa namtindi wa anthuwo amene amatsika pamasitepe. Mwadzidzidzi, ndinaona munthu amene ndinam’dziŵa wochokera cha kwathu! “Malume Bob! Malume Bob!” Anandipeza! Bob Rainer anandinyamula kupita nane kumene makolo anga oda nkhaŵawo anali kudikirira.

Zochitika Zakale Zimene Zinaumba Moyo Wanga

Kuyang’ana malo oonetsera zinthu amenewo kunandikumbutsa zambiri​—zochitika zimene zinaumba moyo wanga ndi kuchititsa kuti tikhale nawo pa malo okongolawo ku Patterson. Ndinakumbukira zochitika zaka zoposa zana limodzi zapitazo, zimene ndinamva makamaka kuchokera kwa agogo ndi makolo anga.

Mu December 1894 mtumiki wa nthaŵi zonse wa Ophunzira Baibulo, mmene Mboni za Yehova zinkadziŵikira nthaŵi imeneyo, anafika pa nyumba ya agogo anga a Clayton J. Woodworth, bambo a bambo anga, ku Scranton, Pennsylvania, U.S.A. A Clayton anali atangokwatira kumene. Analembera kalata pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, Charles Taze Russell, ndipo inasindikizidwa mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1895. Ananena kuti:

“Ndife banja lachinyamata ndipo tinali m’tchalitchi mwa dzina lokha kwa zaka pafupifupi khumi; ndipo tsopano, tikhulupirira kuti tikuchoka mumdima wake kuloŵa m’kuwala kwa tsiku latsopano limene panopo likuchera ana odzipereka a Wam’mwambamwamba. . . . Kalekale tisanakumane n’komwe, chikhumbo chathu chachikulu chinali chakuti tidzatumikire Ambuye monga amishonale m’dziko lina, ngati chingakhale chifuno chake.”

Ndiyeno, mu 1903, a Sebastian ndi a Catherine Kresge, makolo a agogo a amayi anga, anakondwa kumva uthenga wa m’Baibulo umene oimira Watch Tower aŵiri anabweretsa ku famu yaikulu imene anali kukhala, m’mapiri okongola a Pocono ku Pennyslvania. Ana awo aakazi, Cora ndi Mary, anali kukhalanso komweko pamodzi ndi amuna awo, Washington ndi Edmund Howell. Oimira Watch Tower, Carl Hammerle ndi Ray Ratcliffe, anakhala nawo mlungu wonse, akumawaphunzitsa zinthu zambiri. Onse asanu ndi mmodzi m’banja limeneli anamvera, n’kuphunzira, ndipo posatenga nthaŵi anakhala Ophunzira Baibulo achangu.

M’chaka chomwecho cha 1903, Cora ndi Washington Howell anabereka mwana wamkazi dzina lake Catherine. Mmene anakwatiwira ndi bambo anga pomaliza pake, a Clayton J. Woodworth, amene anatenga dzina la bambo awo, ndi nkhani yosangalatsa, ndipo ndikukhulupirira kuti ndi yatanthauzo kwambiri. Imasonyeza chikondi komanso nzeru ya agogo anga, a Clayton J. Woodworth ndi nkhaŵa yawo monga kholo.

Bambo Anga Athandizidwa Mwachikondi

Bambo anga a Clayton, anabadwira ku Scranton mu 1906, mtunda wautali pafupifupi makilomita 80 kuchoka ku famu ya a Howell. M’zaka zoyambirira zimenezo, agogo a Woodworth analidziŵa bwino banja lalikulu la a Howell, limene kaŵirikaŵiri linkawachereza ndipo linali lotchuka ndi zimenezo. Ankathandiza kwambiri mpingo wa Ophunzira Baibulo m’deralo. Patapita nthaŵi, agogo anaitanidwa kukamangitsa maukwati a ana aamuna atatu a a Howell, ndipo pofunira mwana wawo wamwamuna zabwino, anakonza zomapita naye ku uliwonse wa maukwatiwo.

Panthaŵiyo n’kuti Bambo asakuchita nawo mwachangu utumiki wa Ophunzira Baibulo. Inde, anali kuyendetsa agogo pagalimoto kuwaperekeza ku utumiki wawo. Koma ngakhale agogowo anali kuwalimbikitsa, bambo sanachite khama ayi. Panthaŵi imeneyo, bambo anga ankakonda zoimba kuposa zina zilizonse, ndipo cholinga chawo chinali choti akhale katswiri wa nyimbo.

Catherine, mwana wamkazi wa Cora ndi Washington Howell, analinso woimba bwino, wodziŵa kuimba piyano komanso kuphunzitsa piyano. Koma atatsala pang’ono kuti akhale katswiri, anazikankhira pambali nayamba kuchita nawo utumiki wa nthaŵi zonse. Agogo sakanachitira mwina kusiyapo kuganiza kuti munthu ameneyu akhale bwenzi la mwana wawo wamwamunayo​—malinga ndi mmene ndinaonera! Bambo anabatizidwa, ndipo patapita miyezi isanu ndi umodzi, anakwatira mayi anga mu June 1931.

Agogo anali kunyadira nthaŵi zonse ndi luso loimba la mwana wawo wamwamunayo. Anakondwera kwambiri pamene bambo anapemphedwa kuphunzitsa nyimbo zamalimba kagulu kokaimba pamsonkhano waukulu wa mayiko wa ku Cleveland, Ohio mu 1946. Zaka zotsatira, bambo anatsogolera gulu loimbalo pamisonkhano ina ikuluikulu ya Mboni za Yehova.

Agogo Azengedwa Mlandu Komanso Moyo Wawo Kundende

Tili m’chipinda cholandirira alendo muja ku Patterson, ine ndi Paul tinaona chithunzi chimene chili patsamba lotsatirali. Ndinachizindikira msanga chithunzicho, popeza kuti agogo ananditumizira chithunzi chofananacho zaka zoposa 50 zapitazo. Ndi amene ali cha uko kudzanja lamanjawo.

Panthaŵi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse pamene anthu anali ndi mzimu womangokonda dziko lawo, Ophunzira Baibulo asanu ndi atatu ameneŵa​—kuphatikizapo Joseph F. Rutherford (amene akhala pakati), pulezidenti wa Watch Tower Society​—anamangidwa mosayenera ndipo sanaloledwe belo. Mlandu wawo unachokera pa zimene zinalembedwa mu voliyumu yachisanu ndi chiŵiri ya Studies in the Scriptures, ya mutu wakuti The Finished Mystery. Zolembazo anaziona molakwa monga zofooketsa United States kuti asaloŵe nawo mu nkhondo yoyamba ya padziko lonse.

Panyengo ya zaka zambiri, Charles Taze Russell analemba mavoliyumu oyamba asanu ndi limodzi a Studies in the Scriptures, ndipo anamwalira asanalembe voliyumu yachisanu ndi chiŵiri. Choncho notsi zake anazipereka kwa agogo ndi Wophunzira Baibulo wina, ndipo iwo analemba voliyumu yachisanu ndi chiŵiriyo. Voliyumu imeneyo inatulutsidwa mu 1917, nkhondo isanathe. Powazenga milandu, agogo pamodzi ndi anzawo enawo anawapeza ndi milandu inayi ndipo chilango pamlandu uliwonse chinali chakuti akhale m’ndende zaka 20.

Mawu ofotokoza chithunzicho pamalo olandirira alendowo ku Patterson amati: “Patapita miyezi isanu ndi inayi kuchokera pamene Rutherford ndi anzakewo anapatsidwa chilango​—ndipo nkhondo itatha​—pa March 21, 1919, khoti la apilo linalamula kuti onse asanu ndi atatu oimbidwa mlanduwo awapatse belo. Ndipo pa March 26, anawamasula ku Brooklyn aliyense atalipira ndalama zokwana madola 10,000 za belo. Pa May 5, 1920, J. F Rutherford ndi enawo anawapeza opanda mlandu uliwonse.”

Atangowamanga, koma asanawatumize ku ndende ku Atlanta, Georgia, asanu ndi atatuwo anakhala masiku angapo m’ndende ya ku Raymond Street ku Brooklyn, New York. Ali kumeneko, agogo analemba kalata kufotokoza kuti anaikidwa m’lumande ya mamita pafupifupi aŵiri m’lifupi ndi mamita aŵiri ndi theka m’litali “pakati penipeni pa uve wosaneneka komanso malo opanda udongo.” Iwo anati: “Umakhala ndi mulu wa nyuzipepala, ndipo ukapanda kuziganizira bwino poyamba, sizimakutengera nthaŵi kuti uzindikire kuti nyuzipepalazo ndi sopo komanso kansalu kosambira, n’zimene zingakuthandize kukhala waukhondo ndi kusunga ulemu wako.”

Komabe, agogo nthabwala zawo sanazisiye. Anatcha ndendeyo “Hôtel de Raymondie,” akumati, “nthaŵi yanga yokhala muno ikadzangoti yatha, basi ndidzachoka nthaŵi yomweyo.” Anasimbanso za zimene anakumana nazo atakayenda kubwalo. Nthaŵi inayake pamene anaima kanthaŵi kochepa kuti apese tsitsi lawo, wopisa m’matumba anatsomphola watchi yawo yam’thumba, koma monga mmene analembera, “Tcheni lake linaduka ndipo ndinaipulumutsa.” Pamene ndinali kukacheza ku Beteli ya ku Brookyln mu 1958, Grant Suiter, amene anali mlembi ndi msungichuma wa Watch Tower Society, anandiitana mu ofesi yake n’kundipatsa watchi imeneyo. Ndimaikondabe kwambiri.

Mmene Zinakhudzira Bambo

Pamene agogo aamuna anaikidwa m’ndende popanda chifukwa mu 1918, bambo anali ndi zaka 12 zokha. Agogo aakazi anatseka nyumba yawo ndi kuwatenga kuti adzikakhala kwawo ndi amayi awo komanso achemwali awo aang’ono atatu. Dzina la bambo a agogo aakazi linali Arthur. Ndipo a kubanja lawolo ankanena monyadira kuti mmodzi wa abale awo, Chester Alan Arthur, anali pulezidenti wa 21 wa United States.

Pambuyo poti agogo aamuna a Woodworth awalamula kukhala m’ndende kwa nthaŵi yaitali chifukwa cha milandu imene ankati analakwira dziko la United States, a kubanja la a Arthur, mwachionekere anaona ngati kuti agogo anyozetsa dzina lakwawo. Nthaŵi imeneyo inali yopweteka m’maganizo a bambo anga. Mwina kuwachitira zimenezo n’kumene kunawachititsa kukhala amantha kuchita nawo utumiki wapoyera poyambirira.

Pamene agogo aamuna anawamasula kuchoka kundende, anasamutsa banja lawo kukaloŵa m’nyumba yaikulu ya chipupa chomangidwa ndi simenti ndi yopakidwa laimu ku Quincy Street ku Scranton. Monga mwana, ndinkaidziwa bwino kwambiri nyumba ndi mbale zomwe za agogo aakazi. Tinali kuzitcha mbale zopatulika chifukwa panalibe aliyense amene anali kum’lola kuzitsuka kupatula agogo aakaziwo. Pamene agogo aakazi anamwalira mu 1943, mayi anali kuzisamala ndi kuzigwiritsira ntchito mbale zokongola zimenezo.

Kutanganidwa ndi Ntchito ya Utumiki

Tsiku lina ku Patterson komweko, ndinaona chithunzi cha Mbale Rutherford akukamba nkhani pa msonkhano wachigawo mu 1919 ku Cedar Point, Ohio. Analimbikitsa anthu onse kumeneko kuti alengeze mwachangu Ufumu wa Mulungu ndi kugwiritsa ntchito magazini amene anangowatulutsa kumene pamsonkhanowo, a The Golden Age. Agogo aamuna anawaika kukhala mkonzi wake, ndipo analemba nawo nkhani zake mpaka cha m’ma 1940, asanamwalire. Mu 1937 magaziniwo anasinthidwa dzina kukhala Consolation kenaka mu 1946 anatchedwa Galamukani!

Agogowo ankalemba nkhani zawo ali kunyumba ku Scranton ndi kulikulu la Watch Tower ku Brooklyn mtunda wa makilomita pafupifupi 240, ndipo ankatha milungu iŵiri komweko ndi milungu iŵiri kunyumba. Bambo amatiuza kuti amakumbukira kuti masiku ambiri ankamva phokoso la taipilaita faifi koloko m’maŵa . Komabe, agogowo anasamalanso udindo wawo wochita ntchito yolalikira kwa anthu. Inde, anasoka malaya achimuna amene anali ndi matumba aakulu m’kati mwake oikamo mabuku ofotokoza Baibulo. Apongozi anga amene ali ndi zaka 94, a Naomi Howell, adakali nawo malaya oterowo. Anasokanso chikwama cha akazi chonyamulira mabuku.

Nthaŵi ina, atasangalala kukambirana ndi munthu wina za m’Baibulo, mnzawo yemwe anali nawo muutumiki ananena kuti: “Inu a C. J., mwalakwitsa chinthu chimodzi.”

“Ndalakwitsa chiyani?” agogo anafunsa choncho. Anayang’ana m’malaya awo aja. Matumba onse aŵiri analibe kanthu.

“Mwaiŵala kum’thandiza kulembetsa magazini a The Golden Age.” Anaseka pwepwete kuti mkonzi waiŵala kugaŵira magazini ake.

Kukumbukira Kukula Kwanga

Ndikukumbukira nditakhala pa mwendo pa agogo aamuna ndili mwana, atandigwira dzanja pamene anali kundiuza “Nthano ya Zala.” Kuyamba ndi chala chamanthu chomwe anatcha “Tommy Chamanthu” kenako cha nkombaphala chomwe anachipatsa dzina loti “Peter Cholozera,” anandifotokozera mmene chala chilichonse chilili chofunika komanso chapadera. Ndiyeno anafumbata pamodzi bwinobwino zala zanga zonse pondiuza mfundo yake ya nthanoyo kuti: “Pamodzi zimagwira ntchito bwino kwambiri, chala chilichonse chimathandiza zinzake.”

Makolo anga atakwatirana, anasamuka kupita ku Cleveland, Ohio, kumene anakhala mabwenzi apamtima a Ed ndi Mary Hooper. Achibale awo anali Ophunzira Baibulo kuchokera kuchiyambi kwa ma 1900. Makolo anga ndi Amalume Ed ndi Azakhali Mary, mmene ndinali kuwaitanira, anali mabwenzi a ponda apo nane m’pondepo. Mwana wamkazi mmodzi yekhayo wa m’banja la a Hooper anali atamwalira. Choncho pamene ndinabadwa mu 1934, ndinakhala “mwana” wawo wapamtima. Pondilera m’banja lokonda kwambiri zinthu zauzimu limenelo, ndinadzipatulira kwa Mulungu ndipo ndinabatizidwa ndisanafike zaka zisanu ndi zitatu.

Kuŵerenga Baibulo ndiwo unali moyo wanga ndili wamng’ono. Ndime yofotokoza moyo m’dziko latsopano la Mulungu pa Yesaya 11:6-9 inali mbali ya malemba imene ndinali kukonda kuŵerenga. Nthaŵi yoyamba imene ndinayesa kuŵerenga Baibulo lonse munali mu 1944 nditalandira Baibulo langa la American Standard Version, limene linatulutsidwa monga buku lapadera pamsonkhano wachigawo ku Buffalo, New York. Ndinakondweratu kwambiri kuŵerenga matembenuzidwe ameneŵa amene dzina la Mulungu, lakuti Yehova, analiika m’malo ake pafupifupi nthaŵi 7,000 mu “Chipangano Chakale”!

Kumapeto kwa mlungu uliwonse kunali kosangalatsa. Makolo anga ndi banja la a Hooper ankapita nane kukachita umboni kumidzi. Tinkatenga chakudya chamasana ndi kukadyera m’mphepete mwa mtsinje. Kenaka tinkapita ku famu ya winawake kukakamba nkhani ya m’Baibulo panja imene tinaitanira anthu onse oyandikana nawo. Umoyo sunali wovuta. Tinasangalala monga mabanja. Patapita nthaŵi, angapo a mabwenzi oyambirira a banja lathu ameneŵa anakhala oyang’anira oyendayenda, kuphatikizapo Ed Hooper, Bob Rainer, ndi ana ake aamuna aŵiri. Richard Rainer adakachitabe ntchito imeneyi pamodzi ndi mkazi wake, Linda.

Nthaŵi zosangalatsa kwenikweni zinali za chilimwe. Ndinkakhala pa famu ya a Howell ndi achemwali anga ochokera kwa mayi anga aakulu. Mu 1949 mchemwali wanga wamkulu Grace anakwatiwa ndi Malcolm Allen. Sindinadziŵe kuti zaka zingapo pambuyo pake ndinali kudzakwatiwa ndi mng’ono wake. Msuwani wanga Marion anali mmishonale ku Uruguay. Anakwatiwa ndi Howard Hilborn mu 1966. Abale anga aŵiriwo anatumikira pamalikulu ku Brooklyn pamodzi ndi amuna awo kwa zaka zingapo.

Agogo ndi Kumaliza Kwanga Maphunziro a Kusekondale

Pamene ndimachita maphunziro a kusekondale, tinkakonda kulemberana makalata ndi agogo. Ankatumizanso zithunzi zakale za banja lathu limodzi ndi makalata awo atazitaipa kumbuyo kwake, kufotokoza mwatsatanetsatane za mbiri ya banja lathu. Ndi mmene ndinalandirira chithunzi chawo ndi anzawo amene anamangidwa mosayenera.

Cha kumapeto kwa 1951, agogo analeka kulankhula chifukwa cha kansa ya kummero. Nzeru zawo zinali bwinobwino, kungoti akafuna kulankhula anali kulemba mawu awo m’kabuku kamene ankayenda nako. M’kalasi lathu tinali kudzamaliza maphunziro a kusekondale pakati pa temuyo, mu January 1952. Kumayambiriro a December, ndinawatumizira agogo autilaini ya nkhani imene ndinkafuna kudzanena tsiku la mwambo womaliza maphunziro. Anandichongera monga mkonzi ndipo kumapeto kwa pepala lomaliza analembako mawu aŵiri amene anandifika mumtima akuti: “Agogo akondwera.” Anamaliza moyo wawo wapadziko lapansi ali ndi zaka 81, pa December 18, 1951. * Ndikuisungabe autilaini yakaleyo ya zimene ndinanena nditasankhidwa kuti ndidzalankhule potsekera imene zilembo zake sizikuonekanso bwino, yokhala ndi mawu aŵiriwo kumapeto kwake.

Nditangomaliza maphunziro amenewo, ndinayamba utumiki waupainiya, mmene Mboni za Yehova zimatchera ntchito yolalikira yanthaŵi zonse. Mu 1958, ndinakhala nawo pamsonkhano waukulu koposa wachigawo ku New York City, kumene anthu ochuluka zedi okwanira 253,922 ochokera ku mayiko 123 anadzadza Yankee Stadium ndi Polo Grounds. Tsiku lina kumeneko ndinakumana ndi nthumwi ina yochokera ku Africa imene inavala baji yolembedwa kuti “Woodworth Mills.” Zaka 30 m’mbuyomo, anapatsidwa dzina la agogo!

Ndine Wokondwa Chifukwa cha Choloŵa Changa

Pamene ndinali ndi zaka 14, mayi anga anayambanso kuchita upainiya. Anamwalira patatha zaka 40, mu 1988, adakali mpainiyabe! Bambo anga ankachita nawo upainiya akapeza mpata. Anamwalira miyezi isanu ndi inayi mayi asanamwalire. Amene tinali kuphunzira nawo anakhala mabwenzi apamtima kwa moyo wathu wonse. Ena mwa ana awo aamuna anapita kukatumikira kulikulu ku Brooklyn, ndipo ena anayamba ntchito yaupainiya.

Chaka cha 1959 chinali chapadera kwambiri kwa ine. Ndicho chaka chimene tinadziŵana ndi Paul Allen. Anaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda mu 1946 atamaliza maphunziro a Gileadi m’kalasi lachisanu ndi chiŵiri, sukulu yophunzitsa amishonale a Mboni za Yehova. Pamene tinakumana ndi Paul, sitinadziŵe kuti adzam’tumiza ku Cleveland, ku Ohio, kumene ndinkachita upainiya wanga. Bambo anam’konda, chimodzimodzinso mayi. Tinakwatirana mu July 1963 pa famu ya a Howell, ndipo mabanja akwathu analipo ndiponso a Ed Hooper ndiwo anakamba nkhani ya ukwatiwo. Zinali ngati kutulo ndithu.

Paul analibe galimoto. Pamene tinachoka ku Cleveland kupita kukagwira ntchito kwina, katundu wathu yense anakwanira mu galimoto langa la mu 1961 la Volkswagen Bug. Kaŵirikaŵiri anzathu anali kubwera Lolemba, tsiku limene tinali kuchoka pampingo kupita ku mpingo wina, kudzationa tikulongedza. Zinali ngati tikuchita maseŵera osangalatsa anthu kuona masutikesi, mabulifikesi, mabokosi a mafaelo, taipilaita, ndi zina zotero, zikuloŵa zonse m’kagalimoto kakang’onoko.

Ine ndi Paul pamodzi tayenda makilomita osaŵerengeka, ndipo taona zabwino komanso kupirira zoŵaŵa za moyo uno​—zonse zachitika ndi mphamvu imene Yehova yekha amapereka. Zaka zonsezi zakhala zosangalatsa, zodzaza ndi kukonda Yehova, kukondana ifeyo, ndi kukonda mabwenzi athu akale ndi atsopano. Miyezi iŵiri imene tinakhala ku Patterson pamene Paul anali kuphunzira inali yapadera kwambiri m’moyo wathu panthaŵi imeneyo. Kuliyang’anira pafupi kwambiri gulu la Yehova la padziko lapansi kunatsimikizira chikhulupiriro chomwe ndinalandira monga mbali ya choloŵa chauzimu. Chikhulupiriro chakuti: Limeneli ndilodi gulu la Mulungu. Sikusangalatsa kwake kukhala ngakhale mbali yake yaing’ono!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 44 Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi, February 15, 1952, patsamba 128.

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi Ed Hooper masiku a msonkhano wachigawo wa mu 1941 ku St Louis atatsala pang’ono kufika, kumene ndinalandira buku langa la “Children”

[Chithunzi patsamba 26]

Agogo mu 1948

[Chithunzi patsamba 26]

Pafamu ya a Howell pamene makolo anga (amene ali m’katiwo) anakwatirana

[Chithunzi patsamba 27]

Ophunzira Baibulo asanu ndi atatu amene anamangidwa mosayenera mu 1918 (Agogo ndi awo amene aima kudzanja lamanjawo)

[Chithunzi patsamba 29]

Katundu wathu yense anali kukwana m’galimoto lathu la Volkswagen

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili ndi mwamuna wanga, Paul