Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuŵerenga Baibulo—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa

Kuŵerenga Baibulo—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa

 Kuŵerenga Baibulo​—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa

“Ulingiriremo usana ndi usiku.”​—YOSWA 1:8.

1. Kodi kuŵerenga mwachisawawa kuli ndi mapindu otani nanga kuŵerenga Baibulo kuli ndi mapindu otani?

KUŴERENGA nkhani zothandiza n’chinthu chopindulitsa kwabasi. Wafilosofi yandale wa ku France wotchedwa Montesquieu (Charles-Louis de Secondat) analemba kuti: “Nthaŵi zonse, kuphunzira kwandithandiza kugonjetsa zotopetsa m’moyo. Sindinakhalepo ndi nkhaŵa imene inalephereka kutha pambuyo poŵerenga kwa ola limodzi.” Mokulira, kuŵerenga Baibulo kumachitadi zimenezo. Wamasalmo wouziridwa anati: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima.”​—Salmo 19:7, 8.

2. N’chifukwa chiyani Yehova wateteza Baibulo kwa zaka zambirimbiri, ndipo akufuna kuti anthu ake achite nalo chiyani?

2 Monga Wolemba Baibulo, Yehova Mulungu waliteteza kwa zaka mazana ambirimbiri ku chitsutso chosakaza cha adani ake, achipembedzo ndi akunja omwe. Popeza kuti cholinga chake n’chakuti “anthu onse apulumuke nafike pozindikira choonadi,” waonetsetsa kuti mtundu wonse wa anthu ukhale ndi Mawu ake. (1 Timoteo 2:4) Kwalingaliridwa kuti pafupifupi 80 peresenti ya anthu onse a padziko lapansi angamve uthenga mwa kugwiritsa ntchito zinenero 100. Baibulo lonse lathunthu likupezeka m’zinenero 370, ndipo zigawo za Malemba zingaŵerengedwe m’zinenero ndi malilime enanso 1,860. Yehova akufuna kuti anthu ake aŵerenge Mawu ake. Amadalitsa atumiki ake omwe amalabadira Mawu ake, inde, omwe amaŵerenga mawuwo tsiku lililonse.​—Salmo 1:1, 2.

Oyang’anira Ayenera Kumaŵerenga Baibulo

3, 4. Kodi Yehova ankafuna kuti mafumu a Israyeli azichita chiyani, ndipo anafunikira kuchita zimenezo pa zifukwa ziti zomwe zikugwiranso ntchito lerolino kwa akulu achikristu?

3 Polankhula za nthaŵi yam’tsogolo pamene mtundu wa Israyeli udzakhale ndi mafumu aumunthu, Yehova anati: “Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilembere chofanana cha chilamulo ichi m’buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi; ndipo azikhala nacho, naŵerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulo ichi ndi malemba aŵa, kuwachita; kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere.”​—Deuteronomo 17:18-20.

4 Onani zifukwa zomwe Yehova anafunira kuti mafumu onse a Israyeli am’tsogolowo azidzaŵerenga buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku: (1) “kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulo ichi ndi malemba aŵa, kuwachita”; (2) “kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake”; (3)  “kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere.” Kodi oyang’anira achikristu lerolino sayeneranso kuopa Yehova, kumvera malamulo ake, kupeŵa kudzikweza pamaso pa abale awo, ndi kupeŵa kupatukira malamulo a Yehova? Ndithudi kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’kofunika kwambiri kwa iwoŵa monga momwe kunalili kofunika kwa mafumu a Israyeli.

5. Kodi Bungwe Lolamulira posachedwapa lalembera a m’Komiti ya Nthambi malangizo otani okhudza kuŵerenga Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani akulu onse achikristu akulimbikitsidwa kutsatira malangizo ameneŵa?

 5 Akulu achikristu lerolino amakhala ndi zochita zambiri, kotero kuti kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse kumawavuta. Mwachitsanzo, a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova komanso a m’Makomiti a Nthambi padziko lonse, onseŵa ndi amuna otanganidwa kwambiri. Komabe, kalata yaposachedwapa imene Bungwe Lolamulira linalembera Makomiti onse a Nthambi inagogomeza kufunika kwa kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse ndi kukhala ndi zizoloŵezi zabwino za kuphunzira. Kalatayo inati, zimenezi zidzawonjezera chikondi chathu pa Yehova ndi choonadi, ndiponso “zidzatithandiza kukhalabe achikhulupiriro, achimwemwe, ndi akhama kufikira mapeto aulemerero.” Zimenezi n’zofunikanso kwa akulu onse m’mipingo ya Mboni za Yehova. Kuŵerenga Malemba tsiku ndi tsiku kudzawathandiza ‘kuchita mwanzeru.’ (Yoswa 1:7, 8) Makamaka kwa iwoŵa, kuŵerenga Baibulo “n’kopindulitsa pophunzitsa, podzudzula, powongolera zolakwika, ndi polangiza molungama.”​—2 Timoteo 3:16, Revised Standard Version.

N’kofunika kwa Achinyamata ndi Achikulire

6. N’chifukwa chiyani Yoswa anaŵerengera khamu lonse la mafuko a Israyeli ndi alendo mawu onse a chilamulo cha Yehova mokweza?

6 M’nthaŵi yakale, makope a Malemba sanali kupezeka ndi munthu aliyense, choncho Baibulo linali kuŵerengedwa pa chinamtindi cha anthu. Yehova atam’thandiza kugonjetsa mzinda wa Ai, Yoswa anasonkhanitsa mafuko a Israyeli pandunji pa Phiri la Ebala ndi Phiri la Gerizimu. Atatero, nkhaniyo ikutiuza kuti: “Anaŵerenga mawu onse a chilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m’buku la chilamulo. Panalibe mawu amodzi a zonse adazilamulira Mose osaŵerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israyeli, ndi akazi ndi aang’ono, ndi alendo akuyenda pakati pawo.” (Yoswa 8:34, 35) Wamng’ono ndi wamkulu, mbadwa ya mtunduwo ndi mlendo, onse anafunikira kusindikiza, titero kunena kwake, m’mitima ndi m’malingaliro mwawo mikhalidwe yomwe ikanatha kuwadzetsera madalitso a Yehova kapena mkwiyo wake. Ndithudi kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kudzatithandiza kuchita zimenezi.

7, 8. (a) Ndani lerolino omwe ali ngati “alendo,” nanga n’chifukwa chiyani ayenera kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku? (b) Kodi “ana aang’ono” pakati pa anthu a Yehova angatsanzire chitsanzo cha Yesu m’njira ziti?

7 Mamiliyoni a atumiki a Yehova lerolino, ali ngati “alendo” amenewo m’lingaliro lauzimu. Nthaŵi inayake, ankakhala mogwirizana ndi dzikoli, koma tsopano anasintha miyoyo yawo. (Aefeso 4:22-24; Akolose 3:7, 8) Afunikira kumadzikumbutsa miyezo ya Yehova ya chabwino ndi choipa nthaŵi ndi nthaŵi. (Amosi 5:14, 15) Kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kumawathandiza kuchita zimenezi.​—Ahebri 4:12; Yakobo 1:25.

8 Pakati pa anthu a Yehova, palinso “ana aang’ono” ambiri omwe aphunzitsidwa miyezo ya Yehova ndi makolo awo koma akufunikira kutsimikizira kuyenerera kwa chifuno chake. (Aroma 12:1, 2) Kodi angachite motani zimenezo? Mu Israyeli, ansembe ndi akulu anali kulangizidwa kuti: “Muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israyeli wonse, m’makutu mwawo. Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi mlendo wokhala m’midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi; ndi kuti ana awo osadziŵa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu.” (Deuteronomo 31:11-13) Pokhala m’Chilamulo, Yesu ali mwana wamng’ono wazaka 12 anasonyeza kuti  anali wofunitsitsa kumvetsetsa malamulo a Atate wake. (Luka 2:41-49) Atakula, chinali chizoloŵezi chake kumvetsera pamene Malemba anali kuŵerengedwa ndi kutenga nawo mbali m’kuŵerengako m’sunagoge. (Luka 4:16; Machitidwe 15:21) Ana aang’ono lerolino akulimbikitsidwa kutsanzira chitsanzo cha Yesu mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku ndi mwa kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse kumene Baibulo limaŵerengedwa ndi kuphunziridwa.

Kuŵerenga Baibulo Kuikidwe Patsogolo

9. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha zomwe timaŵerenga? (b) Kodi yemwe anayambitsa kulemba magazini ino ananena chiyani chokhudza zothandizira kuphunzira Baibulo?

9 Mfumu yanzeru Solomo analemba kuti: “Tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.” (Mlaliki 12:12) Wina angawonjezere kuti kuŵerenga mabuku ambiri osindikizidwa lerolino si kotopetsa thupi chabe koma, kunena zoona, n’koopsa ku malingaliro. Choncho kusankha n’kofunika. Kuwonjezera pa kuŵerenga zofalitsa zathu zothandiza pophunzira Baibulo, tiyeneranso kuŵerenga Baibulo lenilenilo. Yemwe anayambitsa kulemba magazini ino analembera oŵerenga ake kuti: “Musaiŵale kuti Baibulo ndilo Muyeso wathu ndi kuti mulimonse mmene zithandizo zathu zopatsidwa ndi Mulungu zingakhalire, izo zangokhala ‘zithandizo’ chabe osati zoloŵa m’malo mwa Baibulo.” * Chotero, pamene tikuŵerenga zofalitsa zofotokoza Baibulo mwakhama, tiyeneranso kuŵerenga Baibulo lenilenilo.

10. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wagogomezera motani kufunika kwa kuŵerenga Baibulo?

10 Pozindikira zimenezi, kwa zaka zambiri “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” waphatikiza ndandanda ya kuŵerenga Baibulo pa pulogalamu ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase mu mpingo uliwonse. (Mateyu 24:45) Pulogalamu yamakono yoŵerenga Baibulo imatsiriza Baibulo lonse m’nyengo ya pafupifupi zaka zisanu ndi ziŵiri. Ndandanda imeneyi n’njopindulitsa kwa onse koma makamaka kwa atsopano omwe sanaŵerengepo Baibulo lonse. Awo amene amakaphunzira  ku Sukulu ya Gileadi yophunzitsa Baibulo ya Watchtower kuti akhale amishonale komanso ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki limodzi ndi mamembala atsopano a banja la Beteli amayenera kuŵerenga Baibulo lonse m’chaka chimodzi. Mosasamala kanthu za ndandanda imene m’magwiritsa ntchito, inuyo panokha kapena monga banja, kuitsatira bwino lomwe, kumafuna kuika patsogolo kuŵerenga Baibulo.

Kodi Zizoloŵezi Zanu za Kuŵerenga Zimavumbulanji?

11. Kodi mawu a Yehova tingawadye motani tsiku ndi tsiku, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuwadya?

11 Ngati m’malephera kutsatira ndandanda yanu ya kuŵerenga Baibulo, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zizoloŵezi zanga zoŵerenga kapena kuonerera TV zikukhudza motani mmene ndimaŵerengera Mawu a Yehova?’ Kumbukirani zomwe Mose analemba, ndipo Yesu anabwereza mawu omwewo, kuti “munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4; Deuteronomo 8:3) Monga momwe timafunira kudya nsima kapena chakudya china chilichonse tsiku lililonse la moyo wathu kuti thupi lathu likhale lamphamvu, timafunanso kuloŵetsa malingaliro a Yehova m’maganizo mwathu tsiku ndi tsiku kuti tikhalebe ndi mkhalidwe wathu wauzimu. Tingadziŵe malingaliro a Mulungu tsiku lililonse mwa kuŵerenga Malemba.

12, 13. (a) Kodi mtumwi Petro anachitira motani fanizo chilakolako cha Mawu a Mulungu chomwe tiyenera kukhala nacho? (b) Mosiyana ndi Petro, kodi Paulo anagwiritsa ntchito motani fanizo la mkaka?

12 Ngati timaliyamikira Baibulo, “osati monga mawu a anthu, koma, monga momwe alili ndithu, Mawu a Mulungu,” tidzakopeka nawo monga momwe mwana wakhanda amalakalakira mkaka wa amake. (1 Atesalonika 2:13, NW) Mtumwi Petro anayerekezera choncho, ndipo analemba kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu, kuti kupyolera mwa iwo mukakule kufikira chipulumutso, ngati mwalaŵa kuti Ambuye ali wokoma mtima.” (1 Petro 2:2, 3, NW) Ngati talaŵadi, mwa zomwe zinatichitikira, kuti “Ambuye ali wokoma mtima,” tidzakulitsa chilakolako cha kuŵerenga Baibulo.

13 Onani kuti m’ndime imeneyi Petro anagwiritsa ntchito fanizo la mkaka mosiyana ndi mmene mtumwi Paulo analigwiritsira ntchito. Mkaka umapereka zakudya zonse zofunika m’matupi a makanda. Fanizo la Petro likusonyeza kuti Mawu a Mulungu ali ndi zonse zimene tingafune kuti “[ti]kakule nawo kufikira chipulumutso.” Mosiyana ndi zimenezo, Paulo, anagwiritsa ntchito kufunika kwa mkaka pochitira fanizo zizoloŵezi za kudya mosakwanira zomwe ena odzitcha achikulire mwauzimu alinazo. M’kalata yake yopita kwa Akristu achihebri, Paulo analemba kuti: “Mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusoŵanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizoloŵezi cha mawu a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:12-14) Kuŵerenga Baibulo mosamala kungatithandize kwambiri kukulitsa mphamvu zathu za kuzindikira ndi kusonkhezera chilakolako chathu cha zinthu zauzimu.

Mmene Tingaŵerengere Baibulo

14, 15. (a) Kodi Wolemba Baibulo watipatsa mwayi wotani? (b) Kodi nzeru zaumulungu tingapindule nazo motani? (Perekani zitsanzo.)

14 Kuŵerenga Baibulo kopindulitsa kwambiri kumayamba, osati ndi kuŵerenga, koma ndi pemphero. Pemphero ndi dalitso lapadera. Zimakhala ngati mukuyamba kuphunzira nkhani yovuta zedi m’buku linalake mwa kupempha wolemba bukulo kuti akuthandizeni kumvetsetsa zomwe mukufuna kuŵerengazo. Zingakhaletu zopindulitsa kwabasi zimenezo! Wolemba Baibulo, Yehova, wakupatsani mwayi umenewo. Wam’bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba analembera abale ake kuti: “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzam’patsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse.” (Yakobo 1:5, 6) Bungwe Lolamulira lamakono limatilimbikitsa nthaŵi zonse kuŵerenga Baibulo mwapemphero.

 15 Nzeru ndizo kugwiritsa ntchito chidziŵitso m’njira zothandiza. Choncho musanatsegule Baibulo lanu, pemphani Yehova kuti pamene mukuŵerenga akuthandizeni kuzindikira mfundo zofunikira kuzigwiritsa ntchito m’moyo wanu. Gwirizanitsani zinthu zatsopano zomwe mwaphunzira ndi chidziŵitso chanu chakale. Ziikeni mu “chitsanzo cha mawu a moyo” amene mwawazindikira. (2 Timoteo 1:13) Lingalirani zochitika m’miyoyo ya atumiki akale a Yehova, ndipo dzifunseni momwe inuyo mukanachitira pachochitika chofananacho.​—Genesis 39:7-9; Danieli 3:3-6, 16-18; Machitidwe 4:18-20.

16. Ndi malingaliro othandiza ati omwe aperekedwa kuti atithandize kupanga kuŵerenga kwathu Baibulo kukhala kopindulitsa ndi kofunika kwambiri?

16 Musaŵerenge n’cholinga chongofuna kumaliza masamba otchulidwa pa ndandanda yanu. Ŵerengani modekha. Sumikani maganizo anu pa zomwe mukuŵerengazo. Ngati mfundo inayake yakusokonezani, onani malifalensi ngati Baibulo lanu lilinawo. Ngati mfundoyo simukuimvetsabe, ikanipo chizindikiro kuti nthaŵi ina mudzafufuze mozama za mfundoyo. Pamene mukuŵerenga, lembani mzera kunsi kwa malemba omwe mukufunitsitsa kuti musawaiŵale kapena lembani mawuwo penapake. Mungathenso kuwonjezamo manotsi ndi malifalensi anuanu m’mapeto mwa Baibulo lanulo. Pa Malemba omwe mukulingalira kuti tsiku linalake mudzawafuna pa ntchito yanu yolalikira ndi kuphunzitsa, sankhanipo liwu limodzi lodziŵika bwino ndiyeno lifufuzeni mu zosonyezera mawu a m’Baibulo kumapeto kwa Baibulo lanu. *

Kondwerani Poŵerenga Baibulo

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kukondwera poŵerenga Baibulo?

17 Wamasalmo ananena za munthu wachimwemwe amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:2) Kuŵerenga kwathu Baibulo tsiku ndi tsiku sikuyenera kukhala chintchito cholemetsa koma kuyenera kukhala kosangalatsadi. Njira imodzi yokuchititsira kukhala kosangalatsa ndiyo kuzindikira nthaŵi zonse kufunika kwa zinthu zophunziridwazo. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Wodala ndi wopeza nzeru . . . Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira n’ngwodala.” (Miyambo 3:13, 17, 18) Kuchita khama kuti tipeze nzeru n’kopindulitsadi, chifukwa chakuti njira zake ndi njira zosangalatsa, zamtendere, zachimwemwe, ndipo pamapeto pake, moyo.

18. Kodi chofunika n’chiyani kuwonjezera pa kuŵerenga Baibulo, nanga m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

18 Inde, kuŵerenga Baibulo n’kopindulitsa ndi kosangalatsa. Koma kodi n’kokwanira? Mamembala a m’Machalitchi Achikristu aŵerenga Baibulo kwa zaka mazana ambiri, “ophunzira nthaŵi zonse, koma sakhoza konse kufikira ku chizindikiritso cha choonadi.” (2 Timoteo 3:7) Kuti kuŵerenga Baibulo kukhale kopindulitsa, tiyenera kukuchita n’cholinga chofuna kugwiritsa ntchito chidziŵitso chomwe tingapezecho m’miyoyo yathu ndi kuchigwiritsanso ntchito pa ntchito yanthu yolalikira ndi kuphunzitsa. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Zimenezi zimafuna khama ndi njira zabwino zophunzirira, zomwenso zingatisangalatse ndi kutipindulitsa, monga momwe tidzaonera m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., tsamba 241.

^ ndime 16 Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1995, masamba 16-17, “Malingaliro Owongolera Kuŵerenga Kwanu Baibulo.”

Kubwereza mwa Mafunso

• Ndi malangizo otani operekedwa kwa mafumu a Israyeli omwe akugwiranso ntchito lerolino kwa oyang’anira, nanga n’chifukwa chiyani?

• Ndani lerolino omwe ali ngati “alendo” ndi “ana aang’ono,” ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse?

• Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watithandiza m’njira zofunika ziti kuti tiziŵerenga Baibulo nthaŵi zonse?

• Kodi mapindu enieni ndi chimwemwe tingazipeze motani pamene tikuŵerenga Baibulo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kwenikweni akulu, ayenera kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku

[Chithunzi patsamba 10]

Kutenga nawo mbali m’kuŵerenga Malemba m’sunagoge chinali chizoloŵezi cha Yesu