Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina anali m’gulu la asilikali a Mfumu Davide?

ENA mwa asilikali a Mfumu Davide anali anthu ngati Zeleki mbadwa ya Amoni, Uriya Muhiti komanso Itima wa ku Mowabu. a (1 Mbiri 11:39, 41, 46) M’gulu la asilikali a Davide munalinso ‘Akereti, Apeleti ndi Agiti.’ (2 Sam. 15:18) Zikuoneka kuti Akereti ndi Apeleti anali pachibale ndi Afilisiti. (Ezek. 25:16) Agiti anachokera mumzinda wa Afilisiti wa Gati.​—Yos. 13:2, 3; 1 Sam. 6:17, 18.

N’chifukwa chiyani Davide analola kuti anthu a mitundu ina akhale asilikali ake? Davide sankakayikira kuti anthuwa anali okhulupirika kwa iye komanso Yehova. Mwachitsanzo, ponena za Akereti ndi Apeleti, buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linanena kuti: “Iwo anakhalabe okhulupirika kwa Davide ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri ya ulamuliro wake.” Kodi anachita bwanji zimenezi? Mwachitsanzo, “anthu onse” atachoka kwa Mfumu Davide n’kuyamba kutsatira “munthu wina wosokoneza dzina lake Sheba,” Akereti ndi Apeleti anakhalabe okhulupirika kwa Davide ndipo anamuthandiza polimbana ndi gulu loukiralo. (2 Sam. 20:1, 2, 7) Pa nthawi inanso mwana wa Mfumu Davide dzina lake Adoniya ankafuna kulanda ufumu wa bambo ake. Koma Apeleti ndi Akereti anakhalabe okhulupirika kwa Davide ndipo anathandiza kuti Solomo, yemwe Mulungu anamusankha, akhale mfumu m’malo mwa bambo ake.​—1 Maf. 1:24-27, 38, 39.

Munthu wina amene anakhala wokhulupirika kwambiri kwa Davide ndi Itai wa ku Gati. Itai ndi asilikali ake 600 anathandiza Mfumu Davide pamene Abisalomu mwana wa Davideyo anaukira komanso kuchititsa kuti anthu a mu Isiraeli aukire mfumu. Poyamba Davide anauza Itai kuti popeza anali wa mtundu wina, siinali nkhondo yake. Koma Itai anayankha kuti: “Ndikulumbira m’dzina la Yehova Mulungu wamoyo komanso mbuyanga mfumu muli apa, kulikonse kumene inu mungapite, ine mtumiki wanu ndipitanso komweko, ndipo ndine wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi.”​—2 Sam. 15:6, 18-21.

Itai anali wokhulupirika kwa Davide yemwe anali mfumu yodzozedwa ndi Yehova

Ngakhale kuti Akeleti, Apereti ndi Agiti anali anthu a mitundu ina, iwo ankadziwa kuti Yehova ndi Mulungu woona komanso kuti Davide anali wodzozedwa wake. Davide ayenera kuti ankayamikira kwambiri kuthandizidwa ndi anthu okhulupirika ngati amenewa.

a Pa Deuteronomo 23:3-6, lamulo la Mulungu linkanena kuti a Amoni ndi a Mowabu asamalowe mu mtundu wa Aisiraeli. Koma zikuoneka kuti lamuloli linkaletsa kuti anthu a mitundu imeneyi asamavomerezedwe mwalamulo kukhala Aisiraeli, koma silinkawaletsa kuchita zinthu ndi Aisiraeli kapenanso kukhala pakati pawo. Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 95.