Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 2 2019 | Makhalidwe 6 Amene Muyenera Kuphunzitsa Ana Anu

Makhalidwe 6 Amene Muyenera Kuphunzitsa Ana Anu

Kodi mumafuna kuti mwana wanu azidzadziwika ngati munthu wotani akadzakula?

  • Wodziletsa?

  • Wodzichepetsa?

  • Wopirira?

  • Wodalirika?

  • Woganiza bwino?

  • Wokhulupirika?

Ana sangakhale ndi makhalidwe amenewa paokha. Amafunika kuti inuyo makolo muwathandize.

Magaziniyi yafotokoza makhalidwe ofunika 6 omwe muyenera kuphunzitsa ana anu kuti adzakhale anthu odalirika.

 

Kudziletsa N’kofunika Kwambiri

N’chifukwa chiyani kudziletsa n’kofunika, ndipo tingatani kuti tikhale ndi khalidwe limeneli?

Muziwaphunzitsa Kukhala Odzichepetsa

Kuphunzitsa ana anu kukhala odzichepetsa kungawathandize panopo komanso m’tsogolo akadzakula.

Muziwaphunzitsa Kukhala Opirira

Ana amene amaphunzira kukhala opirira amatha kulimbana ndi mavuto omwe angakumane nawo.

Muziwaphunzitsa Kukhala Odalirika

Kodi ndi nthawi iti imene mwana angaphunzire kukhala wodalirika, pamene ali wamng’ono kapena atakula?

Ana Amafunika Munthu Woti Aziwalangiza

Ana amafunika malangizo odalirika, koma kodi n’kuti kumene angapeze malangizo amenewa?

Muziwaphunzitsa Kufunika Kokhala ndi Makhalidwe Abwino

Ana amene aphunzitsidwa makhalidwe abwino amakhala ndi tsogolo labwino.

Mfundo Zina Zothandiza Makolo

Nawonso makolo amafunika malangizo abwino omwe angawathandize polera ana. Kuti mupeze mfundo zina zothandiza makolo, pitani pa jw.org.