Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZIRO 1

Kudziletsa N’kofunika Kwambiri

Kudziletsa N’kofunika Kwambiri

KODI MUNTHU WODZILETSA AMATANI?

Munthu amene amadziletsa

  • amatha kudikira ngakhale akufunitsitsa zinazake

  • samangotsatira zimene mtima wake ukufuna

  • amatha kumalizitsa zimene akuchita ngakhale zitakhala kuti sizikumusangalatsa

  • amaganizira zofuna za ena m’malo mwa zofuna zake zokha

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?

Ana amene amadziletsa amatha kupewa mayesero ngakhale atakhala okopa bwanji. Koma ana omwe samadziletsa

  • amakhala ovuta

  • amavutika maganizo

  • amasuta, kumwa mowa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo

  • amalephera kusankha zakudya zoyenera

Kafukufuku wina anasonyeza kuti ana amene amadziletsa, akadzakula sadwaladwala, kuvutika maganizo ndi nkhani zandalama komanso savutika kutsatira malamulo. Pomaliza kuchita kafukufukuyu, Pulofesa Angela Duckworth wa ku University of Pennsylvania ananena kuti: “Munthu amapewa mavuto ambiri akakhala wodziletsa.”

MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA ODZILETSA?

Musamasinthesinthe.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mukati ‘Inde’ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayi’ akhaledi ayi.”​—Mateyu 5:37.

Nthawi zina ana amayamba kuvuta, ngakhale pagulu la anthu, n’cholinga chokakamiza makolo awo kuwachitira zimene akufuna. Makolo akamapereka zinthu kwa mwana wawo chifukwa choti akuwavutitsa, mwanayo amayamba kuona kuti kuvutitsa ndi njira yabwino yopezera zimene akufuna.

Koma ngati makolo amapewa kuchita zimenezi, anawo amaphunzira mfundo yakuti: n’zosatheka kupeza chilichonse chimene ukufuna. Dr David Walsh analemba m’buku lina kuti: “Anthu amene amamvetsa mfundo imeneyi ndi amene amakhala osangalala. Choncho kungakhale kulakwa ngati titachititsa ana athu kuyamba kuganiza kuti azidzangoyenda moyera n’kumapeza chilichonse chimene akufuna.” *

 Mukamakana kupatsa mwana wanu chilichonse chimene akufuna, sadzavutika kukhala wodziletsa akadzakula. Mwachitsanzo sangadzavutike kudziletsa akadzakopeka kuti ayambe kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kugonana asanakhale pabanja kapena kuchita zinthu zina zolakwika.

Muziwathandiza kudziwa zomwe zingatsatirepo ngati atachita zabwino kapena zoipa.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”​—Agalatiya 6:7.

Mwana wanu afunika kudziwa kuti chilichonse chimakhala ndi zotsatirapo zake. Choncho ngati atalephera kudziletsa akhoza kukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo ngati mwana wanu sachedwa kupsa mtima, anthu akhoza kumamupewa. Koma ngati amatha kuugwira mtima ambiri angamamukonde. Muzimuthandiza kudziwa kuti zinthu zidzamuyendera bwino akamayesetsa kukhala wodziletsa.

Muziwaphunzitsa kuti azichita zinthu zofunika kwambiri.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

Sikuti kudziletsa kumangotanthauza kupewa kuchita zinthu zolakwika, kumaphatikizaponso kuchita zinthu zoyenera ngakhale zitakhala kuti sizikutisangalatsa. Mwana wanu ayenera kudziwa kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, n’kumayambirira kuchita zimenezo. Mwachitsanzo ndi bwino kuti aziyamba walemba homuweki yake asanapite kosewera.

Muziwapatsa chitsanzo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.”​—Yohane 13:15.

Zinthu zokhumudwitsa zikakuchitikirani, ana anu amaona zimene mumachita. Zimene mumachita zingawaphunzitse kudziwa kuti kukhala wodziletsa kumakhala ndi zotsatirapo zabwino. Mwachitsanzo ngati mwana wachita zokukhumudwitsani, kodi mumapsa mtima n’kuyamba kumukalipira kapena mumatha kuugwira mtima?

^ ndime 20 Kuchokera m’buku lakuti, No: Why Kids​—of All Ages​—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.