GALAMUKANI! July 2015 | Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?
Kodi pa moyo wanu mwakumana ndi zinthu zimene simunkayembekezera? Magaziniyi ikufotokoza zimene zingakuthandizeni.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?
Musataye mtima ngati mwakumana ndi mavuto osayembekezereka.
NKHANI YAPACHIKUTO
Vuto Limene Limakhalapo: Zinthu Zina Simungazisinthe
Onani zinthu 4 zimene zingakuthandizeni ngati mwakumana ndi vuto loti simungalisinthe.
NKHANI YAPACHIKUTO
Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika
Mukamayesa kuchita zonse nokha mukhoza kulephera kuchita chilichonse. Kodi mungatani kuti musamapanikizike?
NKHANI YAPACHIKUTO
Vuto Limene Limakhalapo: Kukhala Wosasangalala
Kodi mungatani ngati mukuvutika chifukwa cha nkhawa, kukwiya kapena kukhumudwa? Onani zimene mungachite.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?
N’zotheka kudziwa zochita mukakumana ndi mavuto.
ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la Mongolia
Moyo wa anthu ambiri ku Mongolia ndi wongoyendayenda koma amalandira bwino alendo.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Kodi Mungatani Ngati Chibwenzi Chatha?
N’chiyani chingakuthandizeni ngati chibwenzi chanu chatha?
Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?
Mukhoza kudziteteza ngati mumakhala kapena mukupita kudziko limene kuli malungo.
KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Nsagwada za Ng’ona
Ng’ona ikaluma, mphamvu zake tingaziyerekezere ndi mphamvu za kuluma kwa mkango ndiyeno n’kuziwirikiza katatu. Koma nsagwada za ng’ona zikakhudzidwa ndi zinazake ng’onayo imamva mwamsanga kuposa mmene munthu amamvera chala chikakhudzidwa. Kodi izi zimatheka bwanji?
Zina zimene zili pawebusaiti
Kuba N’koipa
Kodi Mulungu amakuona bwanji kuba? Werengani Ekisodo 20:15. Onerani vidiyoyi kuti mudziwe zambiri limodzi ndi Kalebe.