Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA

Kodi Mungatani Ngati Chibwenzi Chatha?

Kodi Mungatani Ngati Chibwenzi Chatha?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

“Ndinkaganiza kuti ndapeza mnyamata amene ndinkafuna. Ndinkaona kuti ndidzakhala naye mpaka kalekale. Koma ndinathetsa chibwenzicho patangopita miyezi iwiri yokha. Zinangotha ngati nthano.”—Anna. *

“Ndinkaona kuti tikufanana pa zinthu zambiri ndipo tikwatirana basi. Koma patapita nthawi, ndinaona kuti tinali osiyana kwambiri. Kenako ndinaona kuti si nzeru kukwatirana naye ndipo ndinathetsa chibwenzicho.”—Elaine.

Kodi zoterezi zakuchitikirani? Ngati ndi choncho mfundo za m’nkhaniyi zikhoza kukuthandizani.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

N’zopweteka ngakhale kwa munthu amene wathetsa. Mtsikana wina dzina lake Sarah anathetsa chibwenzi patapita miyezi 6 ndipo anati: “Ngakhale kuti ndine amene ndinathetsa, zinkandiwawa kwambiri. Ndinkaona kuti ndikwatirana naye koma basi zatha. Zinkandipweteka ndikamva nyimbo zimene tinkakonda kumvetsera kapena ndikafika kumalo amene tinkakonda kupita.”

Kuthetsa chibwenzi n’kopweteka koma nthawi zina n’kothandiza. Mtsikana wina dzina lake Elaine anati: “Umaopa kumukhumudwitsa koma umaona kuti tikapitiriza zitivuta tonse.” Sarah uja ananenanso kuti: “Ngati sukusangalala ndi munthu amene uli naye pa chibwenzi ndiye kuti sudzasangalalanso naye mukadzakhala pa banja. Choncho ndi nzeru kuthetsa chibwenzicho.”

Chibwenzi chikatha sikuti ndinu munthu wolephera. Kunena zoona sikuti chibwenzi chilichonse chimakathera m’banja. Ngati wina akuona kuti zingamuvute kukhala bwinobwino ndi mnzakeyo ndi bwino kuthetsa. Zimenezi zikachitika sikuti ndinu wolephera koma chibwenzi n’chimene chalephereka. N’chiyani chingakuthandizeni kuiwala zimene zachitikazo?

ZIMENE MUNGACHITE

Vomerezani zomwe zachitikazo. Elaine amene tamutchula poyamba uja anati: “Ndinasiyana ndi mnzanga wapamtima.” Si zachilendo kudandaula kwambiri ngati mwathetsa chibwenzi chifukwa munthuyo analidi mnzanu wapamtima. Mnyamata wina dzina lake Adam anati: “Chibwenzi chikatha zimapwetekabe ngakhale kuti chatha pa zifukwa zomveka.” Mwina mungamve ngati mmene anamvera Mfumu Davide atakumana ndi mavuto. Iye ankalira kwambiri ndipo anati: “Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa.” (Salimo 6:6) Nthawi zambiri zimenezi zikachitika ndi bwino kungovomereza m’malo mopewa kuziganizira. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuyamba kumva bwino mumtima.—Lemba lothandiza: Salimo 4:4.

Muzicheza ndi anthu amene angakulimbikitseni. Koma kuchita zimenezi si kophweka. Anna amene tamutchula kale uja anati: “Poyamba, sindinkafuna kucheza ndi aliyense. Ndinkafuna kuti ndizingoganizira zimene zinachitikazo n’kuyesetsa kuzivomereza.” Koma kenako Anna anaona kuti kucheza ndi anthu amene angamulimbikitse n’kothandiza. Iye ananenanso kuti: “Maganizo anga ali m’malo tsopano ndipo zimene zinachitikazo sizikundipwetekanso kwambiri.”—Lemba lothandiza: Miyambo 17:17.

Phunzirani pa zimene zachitikazo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndaona zinthu zina zimene ndiyenera kusintha? Kodi ndiyenera kudzachita zinthu ziti ndikadzakhalanso pa chibwenzi?’ Mtsikana wina dzina lake Marcia anati: “Patadutsa nthawi ndinayamba kumvetsa bwino zimene zinachitikazo. Poyamba, zinkandipweteka kwambiri ndipo zinkandivuta kuziganizira bwinobwino.” Adam amene tamutchula kale uja ananenanso kuti: “Panadutsa chaka kuchokera pamene chibwenzi chinatha kuti mtima ukhalenso m’malo. Panadutsanso nthawi yaitali kuti ndiyambe kuona zimene ndingaphunzirepo. Zimene zinachitikazo zinandithandiza kudzidziwa, kumvetsa bwino atsikana komanso kudziwa zimene ndingachite ndikadzakhalanso pa chibwenzi. Panopa zimene zinachitikazo zasiya kundipweteka kwambiri.”

Muziuza Mulungu nkhawa zanu. Baibulo limanena kuti Mulungu “amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Salimo 147:3) Mulungu satisankhira munthu woti tikhale naye pa banja ndipo sitingamuimbe mlandu ngati chibwenzi chathu chatha. Koma iye amatifunira zabwino ndipo tikhoza kumuuza nkhawa zathu.—Lemba lothandiza: 1 Petulo 5:7.

^ ndime 4 Tasintha mayina m’nkhaniyi.