GALAMUKANI! September 2014 | Kodi Mungatani Ngati Mukupanikizika Chifukwa cha Ntchito?

Kupanizikika chifukwa cha ntchito kungachititse kuti muzidwala komanso kutopa. Kodi mungatani kuti musapanikizike chifukwa cha ntchito?

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake ndi monga: lamulo latsopano la ku China lakuti anthu azionetsetsa kuti makolo awo okalamba akupeza zofunika pa moyo wawo wauzimu, vuto lochitira nkhanza akazi ndi malonda achinyengo, ndi zina.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Ngati Mukupanikizika Chifukwa cha Ntchito?

Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kuti musamapanikizike chifukwa cha ntchito.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Pemphero

Kodi tiyenera kumapemphera kwa angelo komanso kwa oyera mtima?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Musamasunge Chakukhosi?

Kodi kukhululuka kumatanthauza kuti mukuchepetsa vutolo kapena mukuona kuti silinachitike n’komwe?

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga

Anthu 90 pa 100 alionse amene ali ndi shuga wopitirira mlingo woyenera sadziwa zimenezi.

TIONE ZAKALE

Dziko la Spain Linathamangitsa Anthu Otchedwa a Morisco

Zinthu zimene zinachitika m’zaka za m’ma 1600, zinapangitsa kuti dziko la Spain likhale lachikatolika.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Chimene Chimachititsa Kuti Dzombe Lisamawombane Pouluka

Kodi n’chiyani chimathandiza dzombe kuti lisawombane likamauluka?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira pa Nkhani ya Kugonana?

Ngati mutafunsidwa kuti: ‘Kodi sunagonanepo ndi munthu chibadwire?’ kodi mungathe kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha?

Mulungu Anatumiza Mose ku Iguputo

Mose ndi Aroni anasonyeza kulimba mtima pamene analankhula ndi mfumu yamphamvu Farao. Koperani nkhaniyi ndipo mukambirane monga banja.