Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Pemphero

Pemphero

Kodi pali amene amamvetsera mapemphero athu?

“Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.”Salimo 65:2.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ena amanena kuti mapemphero athu amangothera m’malere. Makamaka akakhala pa mavuto ndi pamene amakaikira kwambiri ngati Mulungu amamva mapemphero awo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.” (1 Petulo 3:12) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amamvetsera mapemphero athu. Komabe Mulungu amasangalala kwambiri ndi mapemphero a anthu amene amachita zimene iye amafuna. Pa nkhani imeneyi, Baibulo limati: “Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Choncho, kuti Mulungu amve mapemphero athu, tiyenera kudziwa chifuniro chake n’kumapemphera mogwirizana ndi chifuniro chakecho.

 Kodi tizipemphera bwanji?

“Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.”Mateyu 6:7.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu a m’zipembedzo zosiyanasiyana monga Chibuda, Chikatolika, Chihindu ndi Chisilamu, amaphunzitsidwa kuti azigwiritsa ntchito mikanda n’kumanena mapemphero amene analoweza.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthufe tiyenera kumapemphera mochokera pansi pamtima komanso ndi zolinga zabwino. Sitiyenera kuloweza pemphero n’kumalinena mobwerezabwereza. Baibulo limati: “Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza ngati mmene amachitira anthu a mitundu ina, chifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu awamvera akanena mawu ambirimbiri. Chotero inu musafanane nawo, chifukwa Mulungu Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.”—Mateyu 6:7, 8.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI KULI KOFUNIKA

Munthu akamapemphera mosiyana ndi mmene Mulungu amafunira, amangotaya nthawi ndipo akhoza kukhumudwitsa Mulungu. Baibulo limanena kuti mapemphero a anthu ochita zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna amakhala ‘onyansa’ kwa Mulunguyo.—Miyambo 28:9.

Kodi tizipemphera kwa ndani?

“Anthu inu funafunani Yehova pamene iye akupezekabe. Muitaneni akadali pafupi.”Yesaya 55:6.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ena amapemphera kwa Mariya, kwa angelo kapena kwa anthu amene amawaona kuti ndi oyera mtima. Ena mwa anthu amene amati ndi oyera mtimawa ndi Anthony Woyera wa ku Padua ndipo amati ameneyu amathandiza pa nkhani “zauzimu komanso za chikhalidwe.” Wina ndi Jude Woyera ndipo amati amathandiza “anthu pa mavuto.” Ambiri amapemphera kwa anthu amenewa komanso kwa angelo n’cholinga choti akawafikitsire mapemphero awo kwa Mulungu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthu a m’chipembedzo choona ayenera kumapemphera kwa “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Baibulo limatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”Afilipi 4:6.