Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Pepani, Ntchito Yanu Yatha”

“Pepani, Ntchito Yanu Yatha”

“Pepani, Ntchito Yanu Yatha”

MABWANA a Fred * ankamugomera chifukwa iye anali munthu wodziwa ntchito kwambiri. Nzeru zake zinathandiza kuti kampani yawo ipange ndalama zambiri pa zaka 6 zimene Fred ankagwirako ntchito. Choncho ataitanidwa kuti apite ku ofesi ya bwana wamkulu, Fred ankaganiza kuti akufuna akamuuze kuti amuwonjezera malipiro kapena amukweza pa ntchito. M’malomwake bwanayo anangofikira kumuuza kuti, “Pepani, ntchito yanu yatha.”

Fred sanakhulupirire zimenezi. Iye anati: “Ndinkalandira ndalama zambiri komanso ndinkaikonda kwambiri ntchito yanga, koma mwadzidzidzi zonsezi zinasintha.” Fred atakamuuza mkazi wake Adele zimenezi, nayenso sanakhulupirire. Mkaziyo anati: “Ndinazizira nkhongono ndipo ndinadzifunsa kuti, ‘Ndiye titani tsopano?’”

Mofanana ndi Fred, chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse amachotsedwa ntchito. Tchati chimene chili m’munsimu chikusonyeza zimenezi. Komabe, manambalawa paokha sakusonyeza mmene munthu amamvera kupweteka mumtima akachotsedwa ntchito. Mwachitsanzo, Raúl anachoka ku Peru n’kupita ku New York City, ndipo ankagwira ntchito pa hotela inayake yaikulu. Atagwira ntchito pa hotelayi kwa zaka 18, anachotsedwa ntchito. Raúl ankafufuza ntchito koma sanaipeze. Iye anati: “Kwa zaka pafupifupi 30, ndinkakwanitsa kusamalira banja langa. Koma ntchito itatha, ndinkadziona kuti ndine mwamuna wolephera.”

Mmene Raúl ankamvera ntchito yake itatha ndi mmenenso anthu ambiri omwe achotsedwa ntchito amamvera. Iwo amadera nkhawa zinthu zambiri, osati ndalama zokha. Mwachitsanzo, mwamuna wa Renée dzina lake Matthew atachotsedwa ntchito, anakhala pa ulova kwa zaka zoposa zitatu. Renée anati: “Ndinayamba kudziona kuti ndine wopanda pake. Ukakhala kuti ulibe ndalama, anthu sakuonanso ngati munthu ndipo kenako nawenso umayamba kudziona choncho.”

Kuwonjezera pa mavuto amenewa, anthu amene achotsedwa ntchito amafunikanso kuphunzira kugwiritsa ntchito ndalama zochepa. Fred anati: “Nthawi imene tinali ndi ndalama zambiri, tinkawononganso ndalama zambiri. Koma kenako tinafunika kuyamba kusamala ndalama chifukwa ngakhale kuti ntchito inali itatha, tinkafunikabe kulipira mabilu amene tinkalipira m’mbuyomu.”

Pa nthawi imene mukufunafuna ntchito, mumafunika kulimbana ndi nkhawa imene munthu amakhala nayo akakhala kuti sali pa ntchito. Mungafunikenso kuphunzira kugwiritsa ntchito ndalama zochepa. Koma poyamba, tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zimene zingakuthandizeni kuti muchepetse nkhawa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena m’nkhanizi.

[Chithunzi patsamba 3]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Anthu amene sanali pa ntchito m’chaka cha 2008 m’mayiko atatu okha

Japan 2,650,000

Spain 2,590,000

United States 8,924,000