Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mbalame Zazikulu Zouluka Mogometsa”

“Mbalame Zazikulu Zouluka Mogometsa”

 “Mbalame Zazikulu Zouluka Mogometsa”

ANTHU amanena kuti mbalame zooneka ngati bakha zomwe zili pachithunzipa ndi “mbalame zazikulu zouluka mogometsa kuposa mbalame zina zonse,” ndipo m’pake kuti amatero. Mbalamezi ndi zazikulu kwambiri pa mbalame zonse zakunyanja. Zikatambasula mapiko awo, mapikowo amatalika mpaka kufika mamita atatu. Zikamauluka zimathamanga kwambiri mpaka kufika makilomita 115 pa ola limodzi. Zikakhala pamtunda zimaoneka ngati zolobodoka, koma pa nkhani youluka, zilibe mnzake.

Pali mitundu pafupifupi 20 ya mbalame zimenezi imene ikudziwika panopa, ndipo mitundu 15 pa mitundu imeneyi imapezeka m’nyanja ya Pacific, pafupi ndi dziko la New Zealand. Dera linalake lotchedwa Taiaroa Head, limene lili pa chilumba chakum’mwera cha dziko la New Zealand ndi amodzi mwa malo ochepa amene amaweterako mbalamezi kum’mwera kwa dziko lapansi.

Mbalamezi zimayamba kubereka zikafika zaka zapakati pa 6 ndi 10, ndipo zimapitiriza kubereka moyo wawo wonse. Mbalamezi zimakhala ndi moyo wautali, moti zina zimatha kufika zaka zoposa 50. Zimaikira dzira limodzi zaka ziwiri zilizonse ndipo chaka chimodzi chinacho zimakhala zili kunyanja. Nthawi zambiri zimakhala ndi mwamuna kapena mkazi mmodzi moyo wawo wonse.

Kuyambira m’mwezi wa September, mbalame yaimuna ndi yaikazi zimathandizana kumanga chisa. Kenako mu November, mbalame yaikazi imaikira dzira limodzi lomwe limatha kulemera magalamu 500. Kwa masiku 80, mbalame ziwiri zonsezi zimathandizana kukhalira dziralo mpaka kuswa chakumayambiriro kwa February. Kenako zimathandizana kuyang’anira ndi kudyetsa mwanayo. Zimamulavulira kukhosi nsomba ndi nyama zina zam’madzi zimene makolowo anadya. Mwanayo akatha miyezi 6, amatha kulemera kuposa makolo ake, mwina mpaka kufika makilogalamu 12.

Pakatha pafupifupi chaka chimodzi, makolowo amachoka m’dera la Taiaroa Head n’kupita kunyanja kumene amakatha chaka asanabwererenso kumtunda kudzabereka mwana wina. Pa nthawi imeneyi, mwana wawo uja amakhala atachepa thupi, atamera nthenga zonse komanso ataphunzira kuuluka pambuyo poyeserera maulendo ambirimbiri. Mwanayo akachoka m’derali amapita kunyanja kumene amakakhala kwa zaka zingapo, ndipo kenako amabwereranso ku Taiaroa Head atakulirapo. Mbalame zazing’onozi zikabwerera m’derali, zimapeza mbalame zazikulu zitatanganidwa ndi kumanga zisa, kuikira mazira ndi kukhalira, koma pa nthawi imeneyi mbalame zazing’onozi zimangokhalira kudzikonzakonza, kusewera ndi kuonetsera luso lawo louluka.

 [Bokosi patsamba 25]

ULENDO WOKAONA MBALAMEZI

Kuyambira ndili mwana, ndakhala ndikuchita chidwi ndi nkhani zokhudza mbalame zooneka ngati bakha zimenezi. Choncho ndinkayembekezera mwachidwi ulendo wopita kumalo amene amasungira mbalamezi. Tsiku lomwe ndinapita kumalowa, kunja kunali mphepo yambiri. Tikuyandikira, ine ndi mnzanga amene ndinali naye tinkayang’anayang’ana kumwamba kuti tione mbalamezi, ndipo pasanapite nthawi yaitali tinazionadi. Tinagoma kwambiri ndi mmene zinkaulukira.

Titafika, munthu wina wogwira ntchito pamalowa anatitenga limodzi ndi alendo ena n’kuyenda nafe pamalowa kwa ola limodzi. Iye anationetsa zithunzi zosiyanasiyana ndi mavidiyo okhudza mbalamezi, ndipo tinaphunzira kuti mbalame zina zamtunduwu zimatha kukhala moyo wawo wonse kunyanja, mpaka kumagona pamadzi. Kaya mbalamezi zikhale pamadzi kapena m’mlengalenga, zimachita zinthu zogometsa kwambiri. Kuganizira zimene mbalamezi zimachita, kumatichititsa kutamanda Yehova Mulungu, amene ‘analenga zinthu zonse.’—Chivumbulutso 4:11.

 [Chithunzi patsamba 24]

Mbalame yaimuna ndi yaikazi zimathandizana kuyang’anira ndi kudyetsa mwana wawo, amene amatha kulemera makilogalamu 12 pofika miyezi 6

[Chithunzi patsamba 24]

Dera la Taiaroa Head, kumene kumapezeka mbalamezi

[Chithunzi patsamba 24]

Mbalamezi zimatha kukhala moyo wawo wonse kunyanja, mpaka kumagona pamadzi

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

Top: © David Wall/Alamy; bottom: © Kim Westerskov/Alamy

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Background: © davidwallphoto.com; page 24, top: Tui De Roy/Roving Tortoise Photos; page 24, bottom: Courtesy Diarmuid Toman; page 25, albatross in flight: © Naturfoto-Online/Wolfgang Bittmann