Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugunda kwa Mtima Kumagwirizana ndi Kutalika kwa Moyo

Kugunda kwa Mtima Kumagwirizana ndi Kutalika kwa Moyo

Kugunda kwa Mtima Kumagwirizana ndi Kutalika kwa Moyo

● Mtima wanu ndi umene umagwira ntchito yofunika kwambiri pothandiza kuti magazi aziyenda m’thupi. Ngati ndinu munthu wamkulu, mtima wanu umagunda maulendo opitirira mwina 100,000 patsiku. Ngakhale pamene mwangokhala, mtima wanu umagwira ntchito kwambiri, mwina kuwirikiza kawiri ntchito imene minofu ya miyendo yanu imagwira mukamathamanga. Ndipo nthawi zina kugunda kwa mtima wanu kumawirikiza kawiri m’masekondi asanu okha. Kwa munthu wachikulire, pa mphindi imodzi iliyonse mtima wake umapopa magazi malita asanu ngati wangakhola, koma ngati munthuyo akuthamanga, mtimawo umapopa magazi kuwirikiza kanayi kuposa pamenepa. *

Mtima sugunda paokha, koma umachita kulamulidwa ndi ubongo. Ubongo ndi umene umachititsa kuti mapampu olandira magazi a mtima akapopa magazi, azitseka nthawi yomweyo mapampu otumiza magazi asanawapope. Zimenezi zimachititsa kuti magazi amene afika m’mapampu otumiza magazi asabwerere m’mapampu olandira magazi. Phokoso limene madokotala amamva pogwiritsa ntchito chipangizo choyezera kugunda kwa mtima limakhala la kutseka kwa mapampu amenewa, osati la kugunda kwa minofu ya mtima.

Kodi Kugunda kwa Mtima Kumagwirizana Bwanji ndi Kutalika kwa Moyo wa Nyama?

Nyama ikakhala yaikulu kwambiri, mtima wake umagunda pang’onopang’ono ndipo ikakhala yaing’ono kwambiri, mtima wake umagunda mofulumira kwambiri. Mwachitsanzo, mtima wa njovu umagunda maulendo 25 pa mphindi iliyonse, pamene mtima wa mbalame yaing’ono monga chingolopiyo umagunda maulendo 1,000 pa mphindi iliyonse. Munthu akamabadwa, mtima wake umagunda maulendo 130 pa mphindi iliyonse koma akamakula umayamba kugunda pang’onopang’ono mpaka kufika pa maulendo 70 pa mphindi iliyonse.

Nyama zambiri, kuyambira pamene zabadwa mpaka kufa, mtima wawo umakhala utagunda maulendo pafupifupi 1 biliyoni. Choncho, mbewa, yomwe mtima wake umagunda maulendo 550 pa mphindi iliyonse, imatha kukhala ndi moyo pafupifupi zaka zitatu, pamene nangumi, yemwe mtima wake umagunda maulendo 20 pa mphindi iliyonse, amatha kukhala ndi moyo zaka 50. Koma anthu amasiyana ndi nyama pankhani imeneyi. Tikatengera kugunda kwa mtima wathu, anthufe timayenera kukhala ndi moyo zaka 20 basi. Koma munthu amatha kukhala ndi moyo zaka 70 kapena 80, zomwe zikutanthauza kuti mtima wake umagunda maulendo 3 biliyoni kapena kuposa pamenepa. *

Ngakhale kuti anthufe timakhala ndi moyo zaka zambiri tikayerekezera ndi kugunda kwa mtima wathu, timalakalakabe kukhala ndi moyo kwamuyaya. Ndipo maganizo amenewa ndi achibadwa, chifukwa Mulungu anatilenga kuti tisamafe. Ndiponso posachedwapa Mulungu adzachotsa uchimo womwe umabweretsa imfa. (Aroma 5:12) Kenako, malinga ndi zimene lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limanena, “imfa sidzakhalaponso.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Magazi onse a m’thupi la munthu wachikulire amakwana malita asanu.

^ ndime 6 Manambalawa ndi ongoyerekezera, chifukwa kugunda kwa mtima komanso kutalika kwa moyo wa anthu kumasiyanasiyana.

[Chithunzi patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MMENE MTIMA UMAONEKERA

Pampu yakumanja yolandira magazi

Pampu yakumanzere yolandira magazi

Pampu yakumanja yotumiza magazi

Pampu yakumanzere yotumiza magazi