Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinali Msilikali Panopa Ndikutumikira Mulungu

Ndinali Msilikali Panopa Ndikutumikira Mulungu

Ndinali Msilikali Panopa Ndikutumikira Mulungu

Yosimbidwa ndi Gottlieb Bernhardt

Ndinali m’gulu la asilikali apamwamba kwambiri a ku Germany olondera Hitler ndi akuluakulu ena a boma, lotchedwa SS. Ndipo ntchito yanga ndinkagwirira kumalo enaake achitetezo ku Wewelsburg. Mu April 1945, ndinapatsidwa chikalata cholamula kuti akaidi onse a Mboni za Yehova pandende ina yomwe inali pafupi ndi malowa aphedwe. Zimenezi zinandiika pampanipani chifukwa akuluakulu agulu la SS amati akalamula palibe amatsutsa. Dikirani ndifotokoze mmene zinakhalira.

NDINABADWA m’chaka cha 1922 m’mudzi winawake pafupi ndi mtsinje wa Rhine ku Germany. Ngakhale kuti anthu ambiri m’derali anali Akatolika, banja lathu linali la chipembedzo chinachake chotchedwa Pietist, chomwe chinayamba m’zaka za m’ma 1600. Nthawi imene Hitler ankayamba kulamulira ku Germany mu 1933, n’kuti ndili ndi zaka 11. Popeza kuti ndinkakhoza bwino m’kalasi komanso ndinali katswiri pa masewera osiyanasiyana, patapita zaka zingapo, ndinasankhidwa kukaphunzira sukulu ku Poland kufupi ndi ku Marienburg, komwe panopa kumatchedwa kuti Malbork. Panthawiyi ndinayamba kukonda kwambiri mfundo za chipani cha Nazi. Ana a sukulu ankaphunzitsidwa kugwira ntchito mwakhama, kukhulupirika, kumvera, kusunga mwambo, kudzipereka komanso kulemekeza dziko la Germany.

Nthawi ya Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse

Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itayamba mu 1939, ndinalowa m’gulu la asilikali a SS. Ntchito ya asilikali a m’gulu limeneli inali kulondera akuluakulu a boma komanso nthawi zina linkatumidwa kukamenya nkhondo kumayiko ena. Moti ndinali nawo m’gulu la asilikali a SS omwe anatumizidwa kukamenya nkhondo ku Belgium, France, Netherlands, Romania, Bulgaria, ndi ku Greece. Tili ku Bulgaria, ndinapita kutchalitchi komwe mlaliki wake anali msilikali. Panthawiyi ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi adani athu komwe aliko amakhalanso ndi ulaliki woterewu?’ ‘Kodi Mulungu amadalitsa nkhondo?’ ‘Ngati amadalitsa, kodi amakhala mbali iti?’

Kenako, ndinasankhidwa kukachita maphunziro a akuluakulu a asilikali pasukulu yotchedwa Junkerschule. Nditamaliza maphunzirowa, ndinatumizidwa kukalondera likulu la chipani cha Nazi ku Berlin. Ndili kumeneko, tsiku lina ndinaona Hitler akulalatira munthu winawake wandale waudindo wake. Chamumtima ndinati sanachite bwino. Koma sindikanayesa dala kunena zimenezi mokweza.

Ndili ku Berlin komweko, ndinakumana ndi mtsikana wina dzina lake Inge, amenenso ankagwira ntchito kulikulu komweko. Titangotsala pang’ono kukwatirana, gulu lathu linasamutsidwa mwadzidzidzi pa ndege kuti tizikalondera dera linalake pafupi ndi dziko la Russia. Panthawiyi kunja kunkazizira kwambiri koma sanatipatse zovala zamphepo. Zimenezi zinatidabwitsa kwambiri chifukwa m’chaka cha 1941 ndi 1942, kunja kunazizira kwambiri mpaka madzi kumaundana. Kumeneku n’kumene ndinalandira nyota yanga yachiwiri ya Mtanda Wachitsulo. Imeneyi si inali nyota wamba chifukwa inkaperekedwa kwa asilikali ochepa kwambiri amene anamenya bwino nkhondo yoyamba kapena yachiwiri ya padziko lonse. Kenako ndinavulazidwa kwambiri ndipo ananditenga pandege n’kubwerera nane ku Germany. Pasanapite nthawi yaitali, ndinakwatirana ndi Inge mu 1943.

Kenako ananditumiza kuti ndizikagwira ntchito kulikulu la SS ku Obersalzberg, ku mapiri a Bavaria. Msilikali wamkulu woyang’anira gulu la SS, dzina lake Heinrich Himmler, ankakhalanso kumeneku. Popeza kuti panthawiyi ndinali nditavulala, iye analamula kuti ndisamalidwe ndi dotokotala wake, dzina lake Felix Kersten. Kenako ndinazindikira kuti dokotalayu anali ndi malo akulu kwambiri pafupi ndi mzinda wa Berlin, otchedwa Hartzwalde. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatsala pang’ono kutha, iye anapempha Himmler kuti akaidi amene anali a Mboni za Yehova, a ndende ya pafupi, azigwira ntchito pamalowa. Himmler analola, ndipo Kersten ankawalemekeza kwambiri akaidi a Mboni za Yehova amenewa. Munthu wina yemwe ankagwira ntchito kwa Kersten ku Sweden, nthawi zonse ankaika magazini a Nsanja ya Olonda mu chikwama cha Kersten n’cholinga chakuti Mboni za ku Germany zizikagwiritsa ntchito. *

Ndinakopeka ndi Mboni za Yehova

Chakumapeto kwa 1944, Himmler anandisankha kuti ndikhale mlembi mu ofesi ya mkulu wankhondo woyang’anira malo achitetezo a Wewelsburg. Malowa ali pafupi ndi mzinda wa Paderborn ndipo atha zaka pafupifupi 400 chimangire. Himmler ankafuna kuti malowa akhale likulu lophunzitsira mfundo za gulu la SS. Pafupi ndi malowa panali ndende yaing’ono yotchedwa Niederhagen. Pandendeyi m’pamene pankasungidwa akaidi a Mboni za Yehova, omwe ankadziwikanso kuti Ophunzira Baibulo.

Mkaidi wina dzina lake Ernst Specht ankabwera kudzandisamalira panthawi yonse imene ndinali wovulala. M’mawa uliwonse akabwera, ankati: “Mwadzuka bwanji bwana?”

Tsiku lina ndinamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani umakana kunena kuti ‘Hitler mpulumutsi wathu!’?”

Iye anayankha mochenjera kuti, “Kodi inuyo munakulira m’banja lachikhristu?”

Ndinamuyankha kuti, “Inde, makolo anga anali Akhristu.”

Iye anapitiriza kuti, “Ndiye muyenera kuti mukudziwa zimene Baibulo limanena kuti chipulumutso chidzabwera kudzera mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu basi. Ichi n’chifukwa chake sindinena kuti ‘Hitler mpulumutsi wathu!’”

Modabwa komanso mwachidwi, ndinamufunsa kuti, “Kodi unamangidwa chifukwa chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Chifukwa chakuti ndine Wophunzira Baibulo.”

Zimene ndinkakambirana ndi Ernst komanso munthu wina wa Mboni yemwe ankagwira ntchito yometa anthu tsitsi, dzina lake Erich Nikolaizig, zinandigwira mtima. Kukambirana ndi a Mboni mwanjira imeneyi sikunkaloledwa ndipo bwana wanga anandiletsa. Komabe, ineyo ndinkaona kuti ngati aliyense m’dziko la Germany, lomwe limadziwika kuti ndi dziko lachikhristu, atakhala ngati Mbonizi, bwenzi kulibe nkhondo. Ndinkaganiza kuti, ‘Anthu amenewa ndi osiririka ndipo sayenera kuzunzidwa.’

Panthawi yomweyi mayi wina yemwe anali atathedwa nzeru anaimba foni n’kupempha galimoto yoti itengere mwana wake kuchipatala. Mwanayu ankafunika kupangidwa opaleshoni mwamsanga. Ine ndinalamula kuti kupite galimoto msangamsanga koma bwana wanga analetsa. Anachita zimenezi chifukwa chakuti mwamuna wa mayiyu anali m’gulu la anthu amene ananyongedwa chifukwa choti ankafuna kupha Hitler mu July, 1944. Palibe chimene ndikanachita ndipo n’zomvetsa chisoni kuti mwanayo anamwalira. Nkhani imeneyi imandivutitsa maganizo mpaka pano.

Ngakhale kuti panthawiyi ndinali ndisanakwanitse zaka 25, ndinayamba kuona zinthu moyenerera, mosiyana ndi mmene akuluakulu a Nazi ankatiphunzitsira. Komanso ndinayamba kuchita chidwi ndi Mboni za Yehova ndi ziphunzitso zawo. Zimenezi zinachititsa kuti ndisinthe kwambiri moyo wanga.

Mu April 1945, asilikali a mayiko amene ankamenyana ndi dziko la Germany anatsala pang’ono kufika pamalo achitetezo a Wewelsburg ndipo bwana wanga wamkulu anathawa. Panthawiyi Himmler anatumiza asilikali ena kudzatiuza kuti tigwetse malo achitetezowa ndi kupha akaidi. Bwana wamkulu wa pandende ya pafupi ndi malowa anandipatsa maina a akaidi oti aphedwe. Onse anali a Mboni za Yehova. Akuti ankafuna kupha akaidi onse a Mboni chifukwa chakuti ankadziwa kumene kunabisidwa zinthu za mtengo wapatali zimene dziko la Germany linalanda mayiko ena. Iwo samafuna kuti chinsinsi chimenechi chidziwike. Choncho, lamulo limeneli linandivutitsa maganizo kwambiri.

Ndinaganiza zopita kwa mkulu woyang’anira ndende ndipo nditafika ndinamuuza kuti: “Asilikali a dziko la America akubwera. Kodi simukuona kuti ndi bwino kuti inuyo ndi anyamata anu muthawe?” Mkuluyu sanazengereze kuchita zimene ndinamuuzazi. Apa ndinachita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene ndinatumidwa. Ndinathandiza kuti akaidi a Mboni apulumuke.

Unali Mwayi Waukulu Kutchedwa M’bale Wawo

Nkhondo itatha, ine ndi mkazi wanga Inge, tinafufuza a Mboni za Yehova ndipo titawapeza tinayamba kuphunzira Baibulo mwakhama. Mayi winawake wa Mboni, dzina lake Auguste, komanso a Mboni ena ndiwo ankatiphunzitsa. Zinthu sizinkandiyendera bwino kwenikweni chifukwa chakuti ndinavulala kunkhondo komanso nkhondo itatha panali mavuto ambiri. Komabe, ine ndi mkazi wanga tinadzipereka kwa Yehova ndipo kenako tinabatizidwa. Ine ndinabatizidwa mu 1948 ndipo mkazi wanga mu 1949.

Cha m’ma 1950, Mboni zambiri zimene zinali akaidi pandende ya Wewelsburg panthawi ya nkhondo, zinapita kukakumana pandendeyi n’cholinga choti zilimbikitsane pokumbutsana zimene zinachitika. Ena mwa anthuwa anali Ernst Specht, Erich Nikolaizig, ndi Mboni inanso yokhulupirika dzina lake Max Hollweg. Ndikuona kuti ndi mwayi waukulu kutchedwa m’bale wawo chifukwa chakuti anthu amenewa anasonyeza kulimba mtima poika moyo wawo pachiswe n’cholinga choti andilalikire ineyo. Pa anthu amene tinakakumana pandendeyi, panalinso Martha Niemann, yemwe panthawiyo anali sekiritale pandendeyi. Iyenso anakopeka ndi khalidwe labwino la Mboni za Yehova ndipo kenako anabatizidwa.

Ndikaganizira zimene zinachitika m’mbuyo monsemu, ndimaona umboni wochuluka wosonyeza kuti “dziko lonse lili m’manja mwa [Satana Mdyerekezi].” (1 Yohane 5:19) Poyamba, zimenezi sindinkazidziwa n’komwe chifukwa ndinapusitsidwa ndi mfundo za chipani cha Nazi. Panopa ndimaona kuti kutumikira Yehova ndi kosiyana kwambiri ndi kutumikira olamulira ankhanza, monga Hitler. Ulamuliro wa anthu umafuna kuti anthu azigonjera zilizonse, pamene Yehova amafuna kuti tizimutumikira chifukwa chomukonda titaphunzira m’Baibulo za umunthu wake komanso zolinga zake. (Luka 10:27; Yohane 17:3) Choncho, ndatsimikiza mtima kuti ndidzatumikira Yehova moyo wanga wonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 1, 1972, tsamba 399.

[Chithunzi patsamba 19]

Chithunzi cha ukwati wathu, mu February 1943

[Chithunzi patsamba 19]

Himmler ankafuna kuti malo achitetezo a Wewelsburg akhale likulu lophunzitsira mfundo za gulu la SS

[Chithunzi patsamba 20]

Ine ndi mkazi wanga posachedwapa