Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Loto Limeneli Limatanthauza Chiyani?

Werengani nkhani ya pa Danieli 2:25-45, ndipo yankhani mafunso otsatirawa.

1. Kupatulapo dongo, kodi fanoli linapangidwa ndi zinthu zinayi ziti?

․․․․․

․․․․․

․․․․․

․․․․․

2. Kodi zinthu zimenezi zikuimira chiyani?

․․․․․

3. Kodi n’chiyani chinachitikira fanoli?

․․․․․

4. Kodi n’chiyani chinalowa m’malo mwa fanoli ndipo chinakhala kwa nthawi yaitali motani?

․․․․․

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kuti Danieli anali munthu wodzichepetsa? Ngati muli ndi luso pantchito kapena zinthu zinazake, n’chifukwa chiyani muyenera kukhala odzichepetsa?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 8 Kodi anthu okwatirana ayenera kuchita chiyani mwamsanga? Aefeso 4:․․․

TSAMBA 9 Kodi anthu okwatirana afunika kusamala za chiyani? Afilipi 2:․․․

TSAMBA 11 Kodi Mulungu amachenjeza atumiki ake kuti azipewa chiyani? Deuteronomo 18:․․․

TSAMBA 21 Kodi wachinyamata akamachita zimene mawu amanena osati kungomva kokha amakhala wotani? Yakobe 1:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.

5. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Mdzukulu wanga anakhala mfumu yachiwiri ya Isiraeli.

Werengani 1 Samueli 16:13, 14; 1 Mbiri 2:12-15.

6. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Yesaya analosera kuti mmodzi wa ana anga ‘adzaima ngati mbendera ya mitundu ya anthu.’ Werengani Yesaya 11:10.

7. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinatchuka chifukwa chopanga zipangizo zoimbira.

Werengani 2 Mbiri 7:6.

▪ Mayankho ali pa tsamba  22

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Golide, siliva, mkuwa, chitsulo.

2. Maufumu anayi.

3. Linaphwanyidwa.

4. Ufumu wa Mulungu; ndipo udzakhala kwa nthawi zonse.

5. Obedi.—Luka 3:31, 32.

6. Jese.—Luka 3:32.

7. Davide.—Luka 3:31.