Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kufunafuna Ndalama Kukukudwalitsani?

Kodi Kufunafuna Ndalama Kukukudwalitsani?

Kodi Kufunafuna Ndalama Kukukudwalitsani?

MUTAPEZEKA kuti mwalemera kwambiri, kodi mungatani? Kodi mungachepetse kugwira ntchito n’kuyamba kusangalala ndi moyo? Kodi mungasiye ntchito kuti mukhale ndi nthawi yambiri yocheza ndi banja lanu ndiponso anzanu? Kapena kodi mungayambe ntchito imene imakusangalatsani kwambiri? N’zochititsa chidwi kuti anthu ambiri akalemera sachita zinthu zimenezi. M’malo mwake, amakhala otanganidwa moyo wawo wonse kuti apeze ndalama zambiri. Amachita zimenezi kuti abweze ngongole zimene amatenga kapena kuti aziwonjezerabe chuma chawo.

Komabe, anthu ena amene akhala akuchita zimenezi, aona kuti kukonda chuma kumabweretsa mavuto ambiri okhudza thanzi lawo, moyo wa banja lawo, kapena khalidwe la ana awo. Posachedwapa, mabuku, mapulogalamu a pa TV, mavidiyo, ndi nkhani zinanso zalimbikitsa anthu kukhala ndi moyo wosalira zambiri m’malo mokondetsa chuma. Akatswiri ambiri anenapo kuti kufunitsitsa chuma kungakudwalitseni matenda a maganizo kapena matenda enanso.

N’zoona, anthu sanayambe lero kudziwa kuti kukonda chuma kungabweretse mavuto. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Baibulo linanena kuti: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mu msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopanda nzeru ndi zopweteka, zimene zimaponya anthu ku chiwonongeko chotheratu. Pakuti kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.”—1 Timoteyo 6:9, 10.

Koma kodi zimenezi n’zoona? Kodi anthu amene cholinga chawo ndi kupeza ndalama ndi katundu wambiri amakumanadi ndi mavuto? Kapena amakhala ndi zinthu zonse monga chuma, moyo wathanzi, ndi banja losangalala? Tiyeni tione.