Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Wofunitsitsa Kulemera Ungakusokonezeni Motani?

Kodi Moyo Wofunitsitsa Kulemera Ungakusokonezeni Motani?

 Kodi Moyo Wofunitsitsa Kulemera Ungakusokonezeni Motani?

M’DZIKOLI muli anthu oposa 850 miliyoni amene alibe chakudya chokwanira. N’chifukwa chake ndi zovuta kumvetsa kuti pangakhale vuto lililonse ndi kukhala ndi zinthu zambiri. Lemba la m’nkhani yapitayi silikuletsa kukhala ndi ndalama kapena chuma, koma likuchenjeza za kukonda ndalama ndi kufunitsitsa kulemera. Kodi chimachitika n’chiyani anthu akakhala ndi moyo wofunitsitsa ndalama ndi zinthu zambiri? Tiyeni tione kaye mmene moyo umenewu ungasokonezere ana awo.

Mmene Zimasokonezera Ana

Pachaka chimodzi chokha, akuti ana ambiri ku America amaona malonda a pa TV okwana 40,000. Kuwonjezera pamenepo, ana amaonanso m’masitolo ndi nyumba za anzawo zinthu zosiyanasiyana monga masewera a pavidiyo, zoimbira zapamwamba, mapulogalamu a kompyuta, ndi zovala zodula. Tangoganizirani mmene anawa amavutitsira makolo awo popempha zinthu zoti awagulire. Makolo ena amagulira ana awo chilichonse chimene anawo akufuna. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi?

Makolo ena amaonetsetsa kuti ana awo asasowe kanthu chifukwa chakuti iwowo anakula movutika ndipo safuna kuti ana awonso akule chimodzimodzi. Makolo ena amaopa kuti ana awo angasiye kuwakonda akapanda kuwagulira zimene akufuna. Munthu wina amene anayambitsa bungwe lothandiza makolo kusamalira ana m’mzinda wa Boulder ku Colorado m’dziko la United States anati:  “Makolo amafuna kukhala anzawo a pamtima a ana awo ndipo amafuna kuti anawo azisangalala.” Makolo enanso amaganiza kuti popeza amatanganidwa kwambiri ndi ntchito ndipo sacheza ndi ana awo, ndi bwino kumangowagulira zinthu zambiri. Kapenanso, pambuyo pogwira ntchito mlungu wonse, makolo amakhala otopa ndipo amaona kuti n’kosavuta kungopatsa ana awo zonse zimene akufuna m’malo molimbana nawo.

Komabe, kodi makolo amene amapatsa ana awo chilichonse chimene akufuna amakhala akuwakondadi? Zikuoneka kuti ana amene amapatsidwa chilichonse, sathandizidwa kukonda makolo awo koma m’malo mwake amakhala osayamika. Sayamika ngakhale atapatsidwa mphatso imene akhala akuilirira. Mayi wina woyang’anira sukulu ya pulayimale anati: “Ndaona kuti ana akamapatsidwa mwamsanga zinthu zimene akufuna, pakapita milungu iwiri zinthuzo sazifunanso.”

N’chiyani chimachitika ndi ana amenewa akakula? Magazini ya Newsweek inanena kuti kafukufuku akusonyeza kuti ana otere akakula “amavutika kuthana ndi mavuto pamoyo wawo.” Popeza kuti sanaphunzire kulimbikira ntchito kuti apeze zimene akufuna, ambiri sakhoza bwino kusukulu, satha kugwira bwino ntchito, ndipo banja limawavuta. Mapeto ake, amangodalira makolo awo kuti aziwapatsabe ndalama. Nthawi zambiri amakhalanso ndi nkhawa kapena amavutika maganizo.

Choncho, ana amene amapatsidwa chilichonse kwenikweni amamanidwa zinthu zina. Sadziwa kufunika kogwira ntchito, sadziwerengera, ndipo sadziona kuti ndi ofunika. Dokotala wina wa maganizo dzina lake Jessie O’Neill ananena kuti: “Mukamapatsa ana zinthu nthawi iliyonse imene akuzifuna, ndiye kuti mukuwakonzera tsogolo lamavuto.”

Kodi N’chiyani Chimachitikira Akuluakulu?

Magazini ina yonena za maganizo inati ngati muli pa banja, “kaya mwakhala m’banja nthawi yaitali motani kapena muli ndi ndalama zambiri bwanji, nthawi zambiri ngati mwakangana, nkhani yake imakhala ya ndalama basi.” Inapitiriza kuti “zimene anthu okwatirana amachita akasemphana maganizo pankhani ya ndalama kapena akakumana ndi mavuto a ndalama, zimasonyeza ngati banjalo lidzayenda bwino m’tsogolo kapena ayi.” (Psychology Today) Mwamuna ndi mkazi amene amakonda kwambiri chuma amaika banja lawo pangozi. Akuti pamabanja 10 aliwonse amene amasudzulana, 9 amatha chifukwa chosemphana maganizo pankhani ya ndalama.

Ngakhale mwamuna ndi mkazi wake atapanda  kusudzulana, banja lawo likhoza kukhala pa mavuto ngati amangoganiza za ndalama ndi kugula zinthu zapamwamba. Mwachitsanzo, banja likakhala ndi ngongole, likhoza kumangokangana ndi kulozana chala pamavuto awo. Nthawi zina, mwamuna kapena mkazi amatanganidwa kwambiri ndi zinthu zimene ali nazo moti sakhala ndi nthawi yocheza ndi mnzakeyo. Kodi chimachitika n’chiyani wina akagula chinthu chodula n’kubisa osamuuza mnzakeyo? Zimenezi zimayambitsa nkhawa, kusakhulupirirana, ndi khalidwe lobisirana zinthu. Zonsezi zimawononga banja.

Akuluakulu ena, kaya anali pa banja kapena ayi, ataya moyo wawo chifukwa cha chuma. Anthu ena ku South Africa ankafuna kudzipha chifukwa chofuna kukhala ndi moyo wapamwamba kwambiri ngati wa ku mayiko olemera kwambiri. Ku United States, mwamuna wina anapha mkazi wake, mwana wake wa zaka 12, ndi kudziphanso chifukwa cha mavuto a zachuma.

N’zoonadi, sikuti anthu ambiri amafa chifukwa chofunitsitsa chuma. Komabe, ambiri amatanganidwa kwambiri ndi kufunafuna chuma moti amakhala ndi moyo wosakhutira. Komanso sakhala ndi moyo wabwino ngati mavuto akuntchito kapena mavuto a zachuma akuwachititsa kudera nkhawa kwambiri, kusowa tulo, kumva mutu, kapena kudwala zilonda za m’mimba. Matenda onsewa angapangitse munthu kuti asakhale ndi moyo wautali. Ngakhale munthu ataganiza zosintha moyo umenewu, madzi amakhala atafika kale m’khosi. Mwina mwamuna kapena mkazi wake anasiya kale kumukhulupirira, ana ake anasokonekera kale maganizo, ndipo thanzi lake linawonongeka kale. Mavuto enawa atha kukonzedwanso, koma pangafunike kuchita khama kwabasi. Ndithudi, anthu otere “adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.”—1 Timoteyo 6:10.

Nanga Inuyo Mukufuna Chiyani?

Anthu ambiri amafuna kukhala ndi banja losangalala, moyo wathanzi, ntchito yabwino, ndi ndalama zokwanira kuti akhale ndi moyo wabwino. Munthu sangathe kukhala ndi zinthu zinayi zonsezi pa nthawi imodzi, ngati maganizo ake onse ali pa ndalama. Kuti anthu aleke kukhala ndi moyo wofunitsitsa ndalama, pangafunike kupeza ntchito ya malipiro ocheperapo, nyumba yaing’ono, kapena kusiya kukhala ndi moyo wapamwamba kwambiri. Koma kodi ndi anthu angati amene angalole kusiya moyo wapamwamba kuti afunefune zinthu zofunika kwambiri pamoyo? Mayi wina anati: ‘Ndikudziwa kuti zinthu zonsezi si zofunika pamoyo, koma zimandivuta kusiya.’ Anthu ena amafuna kusiya moyo wapamwamba, koma safuna kuti ayambe ndi iwowo.

Nanga bwanji inuyo? Ngati mwayamba kale kuona chuma moyenerera, mukuchita bwino. Kapena  kodi mukuwerenga nkhaniyi mwamsangamsanga chifukwa chotanganidwa kwambiri ndi kufunafuna chuma? Kodi inunso mukufuna kusiya kukhala ndi moyo wapamwamba kwambiri kuti mukhale ndi moyo wosangalala? Ngati ndi choncho chitani mwamsanga, moyo wofuna kwambiri chuma usanasokoneze banja lanu. Bokosi lili pansili lingakuthandizeni kuchita zimenezi.

Mukamaona chuma moyenerera, banja lonse limakhala losangalala. Koma Akhristu ali ndi chifukwa chinanso choonera chuma moyenerera. Iwo safuna kuti chuma chiwasokonezere ubwenzi wawo ndi Mulungu. Kodi kukonda chuma kungasokoneze bwanji moyo wanu wauzimu, ndipo mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Ana amene amapatsidwa chilichonse, nthawi zambiri amakhala osayamika ndipo sachedwa kutaya zinthu zimene amazilirirazo

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

Kukhala ndi Moyo Wosalira Zambiri

Kuti musiye moyo wokonda kwambiri chuma, muyenera kuchita khama ndi kukonzekera bwino. Nazi mfundo zimene zingakuthandizeni.

▪ CHEPETSANI KATUNDU. Kodi n’chiyani chimene mungasiye kugula? Nanga n’chiyani chimene mungagulitse kapena kupatsa ena? Zinthu zosafunika za kukhitchini? Matepi ndi ma CD? Kapena zovala?

▪ YAMBANI MWAYESA KAYE. Ngati mukuopa kuti simungakwanitse kukhala ndi moyo wosalira zambiri, bwanji osayesa kuchita zimenezi kwa miyezi 6 kapena chaka chimodzi. Ndiyeno, onani ngati kufunafuna ndi kugwiritsa ntchito chuma chanu kunakuthandizani kukhala wosangalala kapena ayi.

▪ KAMBIRANANI LIMODZI NDI ANA ANU. Mukatero, ana anu adzakuthandizani pa zimene mukuchita, ndipo ngati m’posafunika kuwagulira zinthu zimene akufuna, sizidzakuvutani kukana.

▪ M’MALO MOGULIRA ANA ANU CHILICHONSE CHIMENE AKUFUNA MUZIWAPATSA NDALAMA. Mungapatse ana anu ndalama kamodzi pamlungu kapena pamwezi. Ndipo anawo angasankhe kusunga ndalamazo kuti agule chinthu chinachake kapena kusagula chinthucho. Mwa kutero ana anu angaphunzire kudikira, kuyamikira zimene ali nazo, ndi kusankha zinthu mwanzeru.

▪ PEZANI NJIRA ZOKUTHANDIZANI KUSUNGA NDALAMA. Muzigula zinthu zimene zatsitsidwa mtengo. Muzipanga bajeti. M’malo moyendera galimoto yake yake, muziyenda pa galimoto imodzi. Muzigwiritsa ntchito magetsi mosamala. M’malo mogula mabuku anuanu, muzibwereka ku laibulale.

▪ GWIRITSANI NTCHITO NTHAWI MWANZERU. Musaiwale kuti cholinga chanu pokhala ndi moyo wosakonda chuma, si kungokhala ndi chuma chochepa ayi, koma kuti mupeze nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri, monga kucheza ndi banja lanu kapena anzanu. Kodi mukuchita zimenezi?

[Chithunzi patsamba 6]

Kufunitsitsa chuma kungayambitse mavuto m’banja