Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Aliyense Akufuna Moyo Wathanzi!

Aliyense Akufuna Moyo Wathanzi!

Aliyense Akufuna Moyo Wathanzi!

ZAKA zoposa 2,700 zapitazo, mneneri wina analosera kuti nthawi inayake sikudzakhalanso matenda. Ulosi umenewu wasungidwa mpaka m’nthawi yathu ino ndipo umapezeka m’buku lakale limene Yesaya analemba. Iye analemba za nthawi imene palibe munthu amene ‘adzanena, ine ndidwala,’ ndiyeno amawonjezera kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Maulosi ena a m’Baibulo amanenanso za nthawi imeneyo ya m’tsogolo. Mwachitsanzo, buku lomaliza la m’Baibulo la Chivumbulutso, limanena za nthawi imene Mulungu adzachotse zopweteka zonse.—Chivumbulutso 21:4.

Kodi malonjezo amenewa adzakwaniritsidwa? Kodi idzafikadi nthawi imene anthu onse adzasangalale ndi moyo wathanzi, matenda onse atachotsedwa? N’zoona kuti masiku ano anthu ambiri akukhala ndi thanzi labwinopo poyerekezera ndi anthu a mibadwo ya m’mbuyomu. Koma kukhala ndi thanzi labwinopo sikutanthauza kukhala ndi thanzi labwino kwambiri. Anthu ambiri akuvutikabe ndi matenda. Ndipo kungokhala chabe ndi mantha oopa kudwala kumabweretsa nkhawa yaikulu. Ndiponso zoona zake n’zakuti, ngakhale m’masiku amakono ano, palibe amene angazembe matenda osiyanasiyana omwe alipowa, kuphatikizapo matenda a m’maganizo.

Mmene Zimakukhudzirani

Matenda amabweretsa mavuto osiyanasiyana. Limodzi mwa mavuto amenewa ndi kuwonongeka kwa ndalama ndipo anthu ambiri akuda nkhawa ndi vutoli. Mwachitsanzo, m’chaka china posachedwapa ku Ulaya, nthawi yomwe anthu amayenera kugwira ntchito, yokwana pafupifupi masiku 500 miliyoni inawonongeka chifukwa cha mavuto okhudzana ndi matenda. Zimenezi n’zimene zikuchitikanso padziko lonse. Aliyense akukhudzidwa ndi mavuto obwera chifukwa cha kulephera kugwira ntchito bwino kaamba ka matenda komanso chifukwa cha kukwera mtengo kwa mankhwala. Makampani amakhudzidwa kwambiri ndi mavuto amenewa. Pofuna kubwezeretsa ndalama zomwe zawonongeka, makampani amakweza mitengo ya katundu wawo ndipo boma limakweza misonkho. Kodi ndani amene amavutika pamapeto pake? Ndi inuyo!

N’zomvetsa chisoni kuti anthu osauka amavutika kuti apeze chithandizo chabwino cha mankhwala akadwala, ndipo ena sachipeza n’komwe. Umenewu ndi mlili womvetsa chisoni umene uli m’mayiko osauka, komwe zipatala zabwino n’zosowa ndipo mwina sizipezeka n’komwe. Ngakhale kumayiko olemera komwe kuli chithandizo chabwino cha mankhwala, zimakhala zovutabe kuti anthu ena apeze chithandizocho. Zimenezi n’zimene kawirikawiri zimachitikira ambiri mwa anthu 46 miliyoni a ku United States amene alibe njira yowathandiza kulipirira chithandizo cha mankhwala.

Sikuti matenda amangobweretsa mavuto a zachuma okha ayi. Pali mavuto ena monga kuvutika kwambiri ndi matenda osachiritsika, kuvutika ndi ululu waukulu, chisoni chimene timakhala nacho ena akamadwala kwambiri, ndiponso kuthedwa nzeru chifukwa cha imfa ya okondedwa athu.

Chiyembekezo choti tsiku lina anthu adzakhala m’dziko lapansi lopanda matenda n’chosangalatsa kwambiri. Aliyense akufuna kukhala ndi thanzi labwino. Anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Ngakhale kuti zikumveka ngati zosatheka, koma iwo amakhulupirira kuti n’zotheka ndithu. Ena amakhulupirira kuti m’kupita kwa nthawi, mwina matenda onse adzatheratu chifukwa cha kupita patsogolo kwa luso lamakono la sayansi. Koma, anthu amene amadalira Baibulo amakhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa maulosi ake akale, oti m’dziko lapansi simudzakhalanso matenda. Kodi munthu ndiye adzathetsedi matenda? Kapena Mulungu ndiye adzatero? Kodi m’tsogolomu muli zotani?