Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Madzi Ndi Moyo

Madzi Ndi Moyo

Madzi Ndi Moyo

YESU anam’fotokozera mkazi wachisamariya yemwe ankatunga madzi pachitsime za kasupe wa madzi a moyo wosatha. (Yohane 4:14) Ngakhale kuti madzi omwe ankanenawo ndi ophiphiritsa, komabe madzi ndi moyo, chifukwa pa zinthu zofunika kwambiri pa moyo, madzi n’chinthu chachiŵiri, ndipo choyamba ndi mpweya. Munthu angakhale ndi moyo milungu ingapo osadya kalikonse koma sangakhale ndi moyo atapanda kumwa madzi pa masiku asanu okha!

Mbali yaikulu kwambiri ya thupi lathu ndi madzi. Madzi amathandiza pantchito monga kupukusa chakudya kuti chigwire ntchito yake m’thupi. Amachotsa poizoni ndi zinthu zina zosafunika m’thupi, amafeŵetsa mokumanira mafupa ndiponso m’matumbo, komanso amathandiza kuti thupi lisatenthe kapena kuzizira kwambiri. Komano kodi mukudziŵa kuti kumwa madzi okwanira bwino kumathandizanso kuti munthu achepeko thupi?

Muzimwa Madzi Kuti Muchepeko Thupi

Choyamba, m’madzi sanenepetsa, komanso sakhala ndi mchere wambiri. Chachiŵiri, madzi amapha chilakolako chofuna kudya. Chachitatu, madzi amathandiza thupi kuti ligwiritsire ntchito mafuta amene lasunga. Kodi zimenezi zimachitika motani? Impso sizigwira bwino ntchito ngati zilibe madzi okwanira. Zikatero, chiŵindi chimathandiza kuchita ntchito zina ndi zina za impso, komano zimenezi zimalepheretsa chiŵindicho kugwiritsira ntchito bwino mafuta. Ndiyeno, thupi limangowasunga mafutawo, inu n’kumanenepa. N’chifukwa chake, malinga ndi mmene ananenera Dr. Donald Robertson, wa pachipatala china choona za kunenepa monyanyira cha ku Scottsdale, ku Arizona, m’dziko la America, “kumwa madzi okwanira bwino n’kothandiza kwambiri kuti munthu achepeko thupi. Ngati anthu omwe akufuna kuti achepeko thupi samwa madzi okwanira, thupi lawo silingagwiritsire ntchito bwino mafuta.”

Inde, n’zoona kuti nthaŵi zambiri vuto la kuchuluka madzi m’thupi limapangitsa kuti munthu anenepe. Motero, ambiri amene ali ndi vuto la kuchuluka madzi m’thupi mwawo amaganiza kuti kuchepetsa kumwa madzi kungathetse vuto lawolo. Komatu sizili choncho. Thupi likaona kuti madzi achepa, madzi alionse amene atsalamo limawasunga mwina m’mapazi, kaya m’manja, kapenanso m’miyendomu. Motero anthu odziŵa bwino za zakudya zamagulu amanena kuti ndi bwino kuti tizimwa madzi okwanira bwino. Ndipo kumbukirani kuti mukamadya zinthu zamchere wambiri, thupi nalo limasunga madzi ambiri kuti lizisungunulira mcherewo.

Musamadzimane Madzi

Tsiku lililonse, thupi lathu limataya madzi pafupifupi malita aŵiri kudzera pakhungu, m’mapapo, m’matumbo, ndiponso mu impso. Kupuma kokha, kumatitayitsa madzi pafupifupi theka la lita tsiku ndi tsiku. Tingathe kukhala ndi vuto la kuchepa madzi m’thupi ngati sitikumwa madzi obwezeretsa madzi otayikawo. Zina mwa zizindikiro za kuchepa madzi m’thupi ndizo litsipa, kulefuka, minofu imaphwanya, kukodza mkodzo wofiirira, kudana ndi kutentha, ndiponso m’maso ndi m’kamwa m’mauma.

Ndiyeno kodi m’pofunika tizimwa madzi ochuluka motani? Dr. Howard Flaks, woona za mavuto a kunenepa monyanyira, anati: “Munthu wabwinobwino azimwa madzi osachepera matambula 8 kapena 10 patsiku. Ngati m’machita kwambiri maseŵera olimbitsa thupi kapena ngati m’makhala m’madera otentha muyenera kumamwa madzi ambiri kuposa pamenepa. Ndipo anthu onenepa kwambiri afunika kumamwa madzi ambirinso.” Koma pali ena amene amanena kuti ndi bwino kumangomwa madzi munthu ukamva ludzu basi, ngakhale n’zotheka kuti pamene mwamva ludzu kwambiri madzi amakhala atachepa kale m’thupi.

Kodi zakumwa zina zingaloŵe m’malo mwa madzi? Ngakhale kuti zakumwa zosungunulidwa ndi madzi zopangidwa kuchokera ku zipatso ndiponso ku zakudya zamasamba n’zabwino, sikuti zimakhala zopanda mafuta. Komanso zakumwa zodzaza shuga ndiponso za mkaka wambiri zimapangitsa kuti thupi lizifuna madzi ambiri kuti zipukusike. Ndipo mowa komanso zakumwa monga khofi ndi tiyi zimapangitsa kuti munthu azitayataya madzi, motero pamafunika kumamwa madzi ambiri pobwezeretsa madzi omwe atayidwawo. Palibiretu chakumwa china chimene chingaloŵe m’malo mwa madzi. Ndiyetu tamwaniko tambula imodzi pompano!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

Njira Zokuthandizani Kuti Muzimwa Madzi Ambiri

● Yendani ndi botolo la madzi.

● Pachakudya chilichonse, imwani tambula imodzi ya madzi.

● Muzimwa madzi musanayambe kuchita maseŵera olimbitsa thupi, kapena maseŵerawo ali m’kati, ndiponso mutamaliza.

● Kuntchito, m’malo momwa tiyi muzimwa madzi.

● Kuti madzi a pampopi azikoma, athireni mandimu kapena asefeni pogwiritsira ntchito zipangizo zosefera madzi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

Photo: www.comstock.com