Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 4

Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba

Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba

Mateyu 22:41-45

MFUNDO YAIKULU: Muzithandiza anthu kuti akonzekere kumva mfundo inayake pa lemba limene mukufuna kuwerenga.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Ganizirani chifukwa chimene mukuwerengera lemba. Pouza anthu lemba limene mukufuna kuliwerenga, muzinena mawu amene angawathandize kuzindikira mfundo yofunika imene angaiphunzire palembalo.

  • Sonyezani kuti Baibulo ndi lothandiza. Ngati mukukambirana ndi anthu amene amakhulupirira zoti kuli Mulungu, muziwathandiza kuona kuti Baibulo ndi “Mawu a Mulungu” ndipo lingatipatse nzeru yapamwamba kwambiri.

  • Muzithandiza anthu kuti akhale ndi chidwi chofuna kumva mfundo yapalembalo. Funsani funso limene yankho lake lili palembalo, tchulani vuto limene njira yolithetsera ikupezeka palembalo kapena tchulani mfundo imene chitsanzo chake chili palembalo.