Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Kodi kuphunzira za chikhulupiriro cha amuna ndi akazi otchulidwa m’Baibulo kungatithandize bwanji masiku ano?

Tchati

Tchati komanso mapu, zikuthandizani kudziwa nthawi imene anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo anakhalako komanso malo amene ankakhala.

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Pofuna kuti bukuli litithandize, Bungwe Lolamulira likulimbikitsa aliyense kuphunzira payekha komanso monga banja.

Mawu Oyamba

M’Baibulo muli nkhani zambiri zofotokoza amuna ndi akazi amene anasonyeza chikhulupiriro cholimba. Kodi nkhanizi zingatithandize bwanji?

ABELE

“Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani ya Abele, ngakhale kuti Baibulo silifotokoza zambiri zokhudza iyeyo komanso chikhulupiriro chake?

NOWA

“Anayenda Ndi Mulungu Woona”

Kodi Nowa ndi mkazi wake anakumana ndi mavuto otani polera ana awo? Kodi anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro pomanga chingalawa?

ABULAHAMU

“Tate wa Onse Okhala ndi Chikhulupiriro”

Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro? Kodi mukufuna kutsanzira Abulahamu m’njira ziti?

RUTE

“Kumene Inu Mupite Inenso Ndipita Komweko”

N’chiyani chinachititsa Rute kulolera kusiyana ndi anthu a kwawo komanso dziko la kwawo? Kodi Rute anasonyeza makhalidwe abwino ati omwe anachititsa kuti Yehova azimukonda kwambiri?

RUTE

Anali “Mkazi Wabwino Kwambiri”

N’chifukwa chiyani tinganene kuti ukwati wa Rute ndi Boazi unali wapadera? Kodi chitsanzo cha Rute ndi Naomi chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya banja?

HANA

Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima

Hana anakwanitsa kupirira mavuto aakulu kwambiri chifukwa chakuti ankakhulupirira Yehova.

SAMUELI

“Anapitiriza Kukula, Akukondedwa Ndi Yehova”

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Samueli analeredwa mwapadera? N’chiyani chinkalimbikitsa chikhulupiriro chake pamene anali kuchihema?

SAMUELI

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Anakumana ndi Mavuto

Tonsefe nthawi zina timakhumudwa komanso timakumana ndi mavuto amene angasokoneze chikhulupiriro chathu. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Samueli?

ABIGAYELI

Anachita Zinthu Mwanzeru

Kodi tingaphunzirepo zotani pa mavuto a banja amene Abigayeli anakumana nawo?

ELIYA

Sanasunthike pa Kulambira Koona

Kodi tingatsanzire bwanji Eliya tikamalankhula ndi anthu amene amatsutsa zimene Baibulo limaphunzitsa?

ELIYA

Anali Watcheru Ndiponso Anadikira

Kodi Eliya anasonyeza bwanji kuti ankakonda kupemphera pamene ankadikira Yehova kuti akwaniritse lonjezo lake?

ELIYA

Analimbikitsidwa ndi Mulungu Wake

N’chiyani chinachititsa Eliya kukhumudwa mpaka kufika popempha kuti afe?

YONA

Anaphunzira pa Zolakwa Zake

Kodi mungamvetse chifukwa chake Yona ankaopa kugwira ntchito imene Mulungu anamupatsa? Nkhani ya Yona ikutiphunzitse zambiri zokhudza kuleza mtima ndiponso chifundo cha Yehova.

YONA

Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo

Kodi nkhani ya Yona ingatithandize bwanji kudzifufuza?

ESITERE

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Kuti munthu asonyeze chikondi chololera kuvutikira ena, ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kukhala wolimba mtima ngati Esitere.

ESITERE

Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

Kodi Esitere anadzipereka bwanji potumikira Yehova komanso pothandiza anthu ake?

MARIYA

“Ndinetu Kapolo wa Yehova!”

Kodi zimene Mariya ananena kwa Gabirieli zimasonyeza chiyani chokhudza chikhulupiriro cha Mariya? Kodi Mariya anasonyeza makhalidwe ena ati?

MARIYA

‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’

Zimene Mariya anaona ndiponso kumva ali ku Betelehemu zinamuthandiza kukhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova.

YOSEFE

Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika

Kodi Yosefe anateteza banja lake m’njira ziti? N’chifukwa chiyani anatenga Mariya ndi Yesu n’kupita nawo ku Iguputo?

MARITA

“Ndimakhulupirira”

Kodi Marita anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro ngakhale pamene anali ndi chisoni?

PETULO

Anathetsa Mantha Ndiponso Mtima Wokayikira

Nthawi zina kukayikira zinthu kumakhala koipa kwambiri. Koma Petulo anathetsa mantha komanso mtima wokayikira potsatira chitsanzo cha Yesu.

PETULO

Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta

Kodi chikhulupiriro cha Petulo ndiponso kukhulupirika kwake zinamuthandiza bwanji kuti atsatire uphungu umene Yesu anam’patsa?

PETULO

Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka

Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani Petulo pa nkhani ya kukhululuka? Kodi Yesu anachita chiyani posonyeza kuti anakhululukira Petulo?

Mawu Omaliza

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mulimbitse bwanji chikhulupiriro chanu komanso kuti nthawi zonse muzikumbukira zinthu zimene Mulungu watilonjeza?

Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi

KUKHULUPIRIRA MULUNGU

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—Amuna ndi Akazi Otchulidwa M’Baibulo

Muzitengera zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo kuti muyandikire Mulungu.