Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 7-11

“Mtima Wako Usapatuke”

“Mtima Wako Usapatuke”

Mfundo za Yehova zikhoza kutiteteza. Koma kuti zizitithandiza tiyenera kuzikonda ndi mtima wathu wonse. (Miy. 7:3) Mtumiki wa Yehova akalola kuti mtima wake upatuke, zimakhala zosavuta kuti Satana amupusitse. Chaputala 7 cha Miyambo chimafotokoza za mnyamata wina yemwe analola kuti mtima wake umupusitse. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira mnyamatayu?

  • Satana amagwiritsa ntchito zinthu zimene tatchulazi pofuna kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova

  • Tikakhala anzeru ndiponso omvetsa zinthu tidzatha kuoneratu ndiponso kupewa mavuto amene angabwere ngati titachita zinthu zoipa