Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

GALAMUKANI!

Funso: Anthu ena amakayikira zoti nkhani yonena za Yesu ndi yoona, pomwe ena sakayikira n’komwe. Koma pali ena amene amanena kuti n’zosatheka kudziwa kuti zoona ndi ziti. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Perekani magaziniyo: Galamukani! iyi ikufotokoza mfundo zomwe zingatithandize kudziwa zoona zake.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Funso: Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

Lemba: Yoh. 11:11-14

Zoona Zake: Munthu akamwalira, moyo wake umathera pomwepo. Choncho sitiyenera kuopa kuti pali zinazake zomwe zidzatichitikire tikadzafa. Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Mofanana ndi zimene anachita ndi Lazaro, Yesu adzaukitsa anthu amene anamwalira kuti adzakhalenso ndi moyo padzikoli.—Yobu 14:14.

KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KUMISONKHANO (inv)

Perekani kapepalako: Ndikufuna kukuitanani kuti mudzamvetsere nkhani yochokera m’Baibulo. Idzakambidwa ku Nyumba ya Ufumu, kapena kuti malo athu olambirira. [Perekani kapepalako ndipo musonyezeni nthawi komanso malo a misonkhanoyo. Muuzeninso mutu wa nkhani ya mlungu umenewo.]

Funso: Kodi munayamba mwapitapo ku Nyumba ya Ufumu? [Ngati n’zotheka muonetseni vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.