MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzidzichepetsa—Muzipewa Kudzitama
Munthu akamadzitama amasonyeza kuti ndi wonyada, ndipo zimenezi sizilimbikitsa anthu ena. Choncho Baibulo limati: “Mlendo akutamande, osati pakamwa pako.”—Miy 27:2.
ONERANI VIDIYO YAKUTI KHALANI BWENZI LA YEHOVA—UZIDZICHEPETSA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu amadzitama nazo?
-
N’chifukwa chiyani Kalebe amadzitama kwa mnzake?
-
Kodi bambo ake anamuthandiza bwanji kuti azidzichepetsa?
-
Kodi lemba la 1 Petulo 5:5 lingatithandize bwanji kukhala odzichepetsa?