Yoweli 2:1-32

2  “Lizani lipenga m’Ziyoni+ amuna inu ndipo fuulani mfuu yankhondo+ m’phiri langa loyera.+ Anthu onse okhala m’dzikoli anjenjemere,+ pakuti tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi!  Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+ tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani. Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa m’bandakucha kumakhalira pamwamba pa mapiri.+ “Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+ Palibe mtundu wina umene ungafanane nawo kuyambira nthawi yakale+ ndipo sipadzakhalanso wina wofanana nawo ku mibadwomibadwo.  Patsogolo pawo moto wawononga+ ndipo kumbuyo kwawo moto walawilawi ukunyeketsa.+ Patsogolo pawo pali dziko ngati la Edeni+ koma kumbuyo kwawo kuli chipululu chowonongeka ndipo palibe chilichonse chopulumuka.  “Mtundu wa anthuwo umaoneka ngati mahatchi,* ndipo amathamanga ngati mahatchi amphamvu.+  Amadumphadumpha ndipo amachita mkokomo ngati magaleta oyenda pamwamba pa mapiri+ ndiponso ngati moto walawilawi umene ukutentha mapesi.+ Iwo ali ngati anthu amphamvu amene afola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+  Mitundu ya anthu idzamva ululu waukulu+ chifukwa cha mtunduwo, ndipo nkhope zawo zonse zidzakhala zankhawa.+  “Amathamanga ngati amuna amphamvu.+ Amakwera khoma ngati amuna ankhondo. Aliyense amayenda m’njira yake ndipo saphonya njira zawo.+  Iwo sakankhanakankhana ndipo amayendabe ngati mwamuna wamphamvu amene akuyenda panjira yake. Wina akalasidwa ndi kugwa enawo sabwerera m’mbuyo.  “Iwo amathamangira m’mizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda. Amakwera nyumba ndipo amalowa m’nyumbamo kudzera pawindo ngati mbala. 10  Dziko lanjenjemera pamaso pawo ndipo kumwamba kwagwedezeka. Dzuwa ndi mwezi zada+ ndipo nyenyezi zaleka kuwala.+ 11  Yehova adzalankhula+ pamaso pa asilikali ake ankhondo+ pakuti anthu a mumsasa wake ndi ambiri.+ Amene akukwaniritsa mawu ake ali ndi mphamvu. Tsiku la Yehova ndi lalikulu+ ndi lochititsa mantha. Ndani angaime pa tsiku limeneli?”+ 12  Yehova wanenanso kuti, “Tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wanu wonse.+ Salani kudya,+ lirani momvetsa chisoni ndiponso mokuwa.+ 13  Ng’ambani mitima yanu+ osati zovala zanu+ ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu pakuti iye ndi wachisomo, wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Ndithu, iye adzakumverani chisoni chifukwa cha tsokalo.+ 14  Ndani akudziwa kuti mwina adzasintha maganizo ake ndi kukumverani chisoni+ ndipo kenako adzakusiyirani madalitso,+ nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa kuti mupereke kwa Yehova Mulungu wanu? 15  “Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa mu Ziyoni amuna inu.+ Konzekerani nthawi yosala kudya.+ Itanitsani msonkhano wapadera.+ 16  Sonkhanitsani anthu onse pamodzi ndipo muyeretse mpingo.+ Sonkhanitsani amuna achikulire. Sonkhanitsani pamodzi ana ndi makanda oyamwa.+ Mkwati atuluke m’chipinda chake ndipo mkwatibwi atuluke kumalo ake ogona. 17  “Ansembe ndi atumiki a Yehova alire m’khonde mwa guwa lansembe+ ndipo anene kuti, ‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu ndipo musachititse manyazi cholowa chanu+ kuti mitundu ya anthu iwalamulire. Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+ 18  Ndiyeno Yehova adzachitira nsanje dziko lake+ ndipo adzamvera chifundo anthu ake.+ 19  Pamenepo Yehova adzayankha ndi kuuza anthu ake kuti, ‘Tsopano ndikukutumizirani mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta. Anthu inu mudzakhutadi zinthu zimenezi.+ Ine sindidzakuchititsaninso kukhala chinthu chotonzedwa pakati pa anthu a mitundu ina.+ 20  Ndidzakuchotserani mdani wa kumpoto+ kuti akhale kutali ndi inu. Ndidzamuthamangitsira kudziko lopanda madzi ndi labwinja, nkhope yake itayang’ana kunyanja ya kum’mawa*+ ndipo nkhongo yake italoza kunyanja ya kumadzulo.*+ Fungo lake lonunkha lidzamveka ndipo fungo lake loipalo lidzapitirizabe kumveka+ pakuti Mulungu adzachita zinthu zazikulu.’ 21  “Usachite mantha iwe dziko. Kondwera ndi kusangalala, pakuti Yehova adzachita zinthu zazikulu.+ 22  Inu zilombo zakutchire musachite mantha,+ pakuti malo odyetserako ziweto a m’chipululu adzamera msipu wobiriwira.+ Mitengo nayonso idzabereka zipatso.+ Mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa mpesa udzatulutsa zipatso zake zonse.+ 23  Inu ana aamuna a Ziyoni kondwerani ndi kusangalala chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+ Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera+ ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+ 24  Malo opunthira mbewu adzadzaza ndi mbewu zopunthidwa ndipo malo ogweramo vinyo watsopano ndi mafuta adzasefukira.+ 25  Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonse zimene dzombe ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko, mphemvu ndi mbozi zinadya. Limeneli ndi gulu langa lankhondo lamphamvu limene ndinatumiza pakati panu.+ 26  Pamenepo mudzadya ndi kukhuta+ ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu+ amene wakuchitirani zodabwitsa.+ Anthu anga sadzachita manyazi mpaka kalekale.*+ 27  Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndili pakati pa Isiraeli,+ ndiponso kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu ndipo palibenso Mulungu wina.+ Anthu anga sadzachita manyazi mpaka kalekale. 28  “Zimenezi zikadzachitika ndidzatsanulira mzimu wanga+ pa chamoyo chilichonse,+ ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi+ adzanenera. Amuna achikulire adzalota maloto ndipo anyamata adzaona masomphenya. 29  Masiku amenewo ndidzatsanuliranso mzimu wanga pa antchito anu aamuna ndi aakazi.+ 30  “Ndidzachita zodabwitsa kuthambo+ ndi padziko lapansi. Ndidzachititsa kuti pakhale magazi, moto ndi utsi wokwera kumwamba.+ 31  Dzuwa lidzasanduka mdima,+ ndipo mwezi udzasanduka magazi.+ Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanafike.+ 32  Ndiyeno aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka,+ pakuti m’phiri la Ziyoni ndiponso mu Yerusalemu mudzakhala anthu opulumuka+ monga mmene Yehova ananenera. Amenewa ndi anthu amene Yehova akuwaitana.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Kutanthauza, “Nyanja Yamchere.”
Kutanthauza, “Nyanja Yaikulu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.